Nkhani

Apolisi akupitirirabe kuphwanya malamulo

Listen to this article

 

A polisi atatu agwidwa ndi kutsekeredwa m’chitolokosi chawo chomwe mumzinda wa Zomba powaganizira kuti adathandizira mayi wina yemwe akuti adaba ndalama m’dziko la South Africa kutuluka m’chitolokosi.

Apolisiwa ndi Sub Inspector Khudze, Sergeant Mbalame ndi Mankhwala omwe akuganiziridwa kuti adathandiza mayiyo yemwe akuti adaba ndalama zokwana pafupifupi K17 miliyoni kwa bwana wake m’dzikolo.police-brutarity

Izi zidachititsa apolisi a dzikolo kulumikizana ndi a dziko lino omwe mwaukadaulo wawo adamugwira mayiyo, koma ena mwa apolisi omwewo akuti adapezerapo mwayi wotakata ndipo anamutulutsa mwamseri.

Ndipo ku Zomba konko wapolisi wina ,yemwe akungodziwika kuti Kalipinde, adamangidwanso poganiziridwa kuti adachita zakatangale.

Izitu zachitika patangodutsa sabata imodzi wapolisi winanso, Constable Kamoto atatsekeredwa m’chitolokosi cha polisi ya Soche mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti adasowetsa mfuti ataledzebwa pamalo ena omwera mowa.

Pakadalipano apolisi akuti mfuti idasowayo idapezeka.

Ngakhale izi zikuchitika, anthu m’dziko muno amadalira apolisi pankhani yosungitsa lamulo komanso chitetezo.

Kwa zaka zingapo tsopano, apolisi akhala akupezeka ndi milandu yosiyanasiyana, monga kulowetsa anthu omwe alibe ziphaso m’dziko muno podzera njira zosavomerezeka, umbava ndi umbanda komanso kuzunza ena mwa anthu omwe amagwidwa akuyenda usiku.

Ndipo nthawi yonseyi, boma komanso akuluakulu awo akhala akutsimikizira mtundu wa a malawi kuti izi zikhala mbiri yakale kaamba koti kagwilidwe ntchito ka apolisiwa kanaunikidwanso.

Polankhulapo mneneri  wa polisi m’dziko muno James Kadadzera adavomereza kuti ena mwa apolisi akupitirizabe kuswa malamulo ndi kusasunga mwambo.

Kadadzera adati koma akuluakulu a apolisiwa sakusekerera izi ndipo akulanga opezeka akuswa malamulowo pogwiritsa ntchito njira ziwiri.

Iye adati ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito njira zawo za polisi pomwe ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito malamulo a dziko lino.

“Mwachitsanzo apolisi anayi omwe sindiwatchula maina awo, adatsekeredwa mumzinda wa Zomba titalandira dandaulo lakuti adakhudzidwa ndi zakatangale, ndipo alangidwa potengera malamulo a dziko lino, pomwe Kamoto akulangidwa pogwiritsa ntchito malamulo athu,” adatero Kadadzera.

Iye adakana kuyankhulapo mwatsatanetsatane za milandu ya anayiwa.

Kadadzera ngakhale izi zili chomwechi, chiwerengero cha apolisi opezeka akupalamula chikuchepera.

“Koma musaiwale kuti ngakhale alipo apolisi omwe akugwira ntchito yawo molimbika ndi modzipereka, aliponso ena omwe akuswa malamulo. Choncho tili ndi nthambi yoyang’ana kagwiridwe ka ntchito mwaukadaulo ya Profession Standard Unit (PSU) yomwe ikulimbikitsa kusunga mwambo mupolisi,” adatero Kadadzera.

Ndipo nduna ya za m’dziko Grace Chiumia adati atsirirapo bwino ndemanga pankhanizi akamva tsatanetsatane wa nkhani zomwe zidachitika ku Zombazi kuti akhale ndi umboni wonse.

“Sindidalandire lipoti lililonse lokhudza nkhani za ku Zombazi. Ndifufuze kaye kuti zidayenda bwanji,” adatero Chiumia.

Koma mkulu wa bungwe lopereka upangiri ndi thandizo pa maufulu a anthu la Centre for Human Rights, Education, Advice and Assistance(CHREAA), Victor Mhango, adati mchira wanyani udakhota pachiyambi pomwe ena mwa apolisiwa ankalembedwa ntchito.

Mhango adati ambiri adalowa ntchitoyi chifukwa chodziwana ndi ena mwa andale ndipo alibe chidwi chenicheni chogwira ntchito yachitetezo koma kudzilemeretsa.

Iye adati enanso mwa apolisiwa amaona ngati lamulo silingawakhudze ndipo akhoza kupalamula ngakhale kuzunza anthu umo angathere popanda kulandira zilango zamtundu uliwonse.

“Akavala yunifolomu ija ndi kutenga unyolo m’manja amaona ngati basi palibe angawakhudze,” adatero Mhango.

Iye adati nzamanyazi kuti ena mwa apolisiwa akumafika pamlingo wochita nawo za umbava ndi umbanda mmalo moteteza anthu.

Related Articles

Back to top button