Nkhani

Apolisi akwidzinga  anthu 10  ku Neno

  • Akuwaganizira kuti adatengapo mbali kupha agogo anayi

Apolisi m’boma la Neno Lachinayi adanjata anthu 10 powaganizira kuti adatengapo mbali pa imfa za agogo anayi omwe adachita kuphedwa ndi anthu olusa powaganizira kuti ndiwo adalenga mphenzi yomwe idapha mtsikana wa zaka 17, Flora Kanjete, Lolemba lapitalo.mob-justice

Mneneri wa apolisi m’bomalo, Raphael Kaliati, polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali, adati kufikira Lachitatulo apolisi adali asadamange wina aliyense wokhudzidwa ndi kuphwedwa kwa anthu okalambawo podikira kuti bata likhazikike kaye kuderalo kuti ayambe bwino kufufuza za imfazo.

Koma mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalowererapo polamula mkulu wa apolisi Lexten Kachama kuti nkhaniyi aifufuze mmangummangu kuti chilungamo chioneke malinga ndi malamulo a dziko lino ndipo kuti ngati ena apezeka olakwa pamlandu wakupha alandire chilango choyenera.

Malinga ndi chikalata chochokera kunyumba ya boma chomwe adachitulutsa Lachitatu, mtsogoleri wa dziko linoyu adati adali wachisoni komanso wokhumudwa kwambiri ndi imfa za agogowo kaamba kowaganizira za ufiti.

Chikalatacho chidati: “Pulezidenti [Mutharika] akuti anthu okalamba ayenera kulandira ulemu komanso chitetezo nthawi zonse ndipo boma lake silidzalola kuti okalamba azitonzedwa kapena kuvutitsidwa m’njira ina iliyonse m’dziko muno.”

Ndipo pofika Lachinayi, malingana ndi mneneri wa polisi pa Neno, anthu 10, kuphatikizapo anyamata asanu a zaka za pakati pa 13 ndi 18, adanjatidwa ndipo ali m’manja mwa apolisi powaganizira kuti ndiwo adakonza upo wopha agogowo.

Ena mwa omangidwawa ndi Staford Chifundo, wa zaka 36; Amosi Sida, wa zaka 32; Samuel Kaudzu, wa zaka 20; John Harry, wa zaka 21; ndi Lex Mayenda, wa zaka 19. Onsewa, kuphatikizapo anyamata achisodzerawo, akuti mpachibale ndi agogo adaphedwawo.

Kaliati adati anthu khumiwa awatengera kubwalo la milandu la majisitireti ku Neno komwe akaipereke m’manja mwa bwalo lalikulu la High Court poti ndilo lili ndi mphamvu zozenga milandu ikuluikulu monga ya kupha.

Iye adati zofufuza zidakali mkati ndipo pali chiyembekezo choti lamulo ligwirapo ntchito pa onse okhudzidwa ndi nkhani yoziziritsa nkhongonoyi.

Nalo bungwe la Malawi Law Society lidati ndi lokhumudwa ndi imfa za agogowo, omwe adaphedwa pazifukwa zopanda mchere, pongowaganizira za ufiti kaamba ka ukalamba wawo.

“Omwe adakonza chiwembu chopha agogowa ayenera afufuzidwe bwinobwino ndipo akapezeka ayenera akayankhe mlandu kubwalo la milandu ndi kulandira chilango choyenera akapezeka olakwa.

“Bungwe lathu ndi lokonzeka kupereka maloya kuti athandize boma pozenga milanduyo,” chatero chikalata chomwe a bungweli atulutsa pambuyo pa kumva za nkhani yomvetsa chisoniyi, chomwe chidasainidwa ndi pulezidenti wa bungweli John Suzi-Banda ndi mlembi Khumbo Bonzoe Soko.

Oganiziridwawo adamenya agogowo mpaka kumpha zitangodziwika kuti mphenzi yapha mtsikanayo dzuwa likuswa mtengo. Malinga ndi Kaliati, anthuwo akukhulupirira kuti mphenziyo idali yokonzedwa ndi agogowo, omwe adali pachibale.

M’boma la Neno muli vuto la mvula. Chiyambireni chaka chino, mvula yagwa masiku 8 okha koma mphenzi zakhala zikung’anima ndi kupha anthu kumeneko.

Agogowo ndi Eliza Enosi Kanjete, wa zaka 86; Elenefa Kanjete, wa zaka 76; Byson Kanjete, wa zaka 73; ndi Idesi Julias Kanjete, wa zaka 69. Onsewa adali a m’mudzi mwa Chimbalanga 1.

Agogowo adaikidwa m’manda Lachiwiri limodzi ndi mtsikanayo adaphedwa ndi mphenzi uja.

Related Articles

Back to top button