Nkhani

Asemphana pankhani ya malata, simenti sabuside

Listen to this article

Pali kusiyana Chichewa pandondomeko ya malata ndi simenti zotsika mtengo, pamene anthu omwe akuyenera kupindula ndi ndondomekoyi akuti boma tsopano likungopereka zipangizo zokha popanda ndalama zomangira nyumba monga momwe lidawalonjezera.

Koma mneneri wa unduna wa zamalo, Charles Vintulla, watsutsa zoti pali kusintha kulikonse ponena kuti boma lapereka kale zipangizo kuphatikizapo ndalama kwa anthu ovutika zoti amangire nyumba.

Iyi mdi imodzi mwa nyumba zomwe zamangidwa kupyolera mu pologalamu  ya sabuside ya malata ndi simenti
Iyi mdi imodzi mwa nyumba zomwe zamangidwa kupyolera mu pologalamu
ya sabuside ya malata ndi simenti

Ena mwa amene apindula ndi ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo zomangira nyumba auza Tamvani kuti boma lidawapatsa malata ndi simenti mu January chaka chino ndipo ati mu February adauzidwa kuti alandira ndalama zomangira nyumbazo.

Mpaka mwezi uno wa May boma akuti silidawapatsebe ndalamazo, zomwe zapangitsa kuti anthu ena ayambe kugulitsa zipangizozo komanso ena ayamba kumanga pogwiritsa ndalama zam’thumba.

Elina Bamusi wa m’mudzi mwa Gulupu Chalunda, kwa T/A Phambala, m’boma la Ntcheu, ndi mmodzi mwa anthu amene ayamba kumanga nyumba pogwiritsira ntchito ndalama zawo.

“Ndidalandira malata 30 komanso matumba a simenti 30. Nditalandira katunduyo, adati tidikire ndalama zomangira. Tadikira mpaka lero, kenaka akutiuza kuti timange ndi ndalama zathu.

“Ndapeza anyamata amene akundimangira pamtengo wa K130 000. Achibale ndiwo andithandiza ndi ndalamayi komanso kwinako ndidapanga geni ya makala,” adatero mayiyu.

Bamusi adati pamwamba pa malata ndi simenti adawauzidwa kuti boma liwapatsa K190 000 aliyense yomangira nyumba.

“Adatiuza kuti ndalama yonse yomangira nyumba ndi K380 000 koma adati ife tidzabweza K190 000, boma lidzaikaponso K190 000 koma tikudabwa kuti izi sizidachitike ndipo angotipatsa zida popanda ndalama,” adatero mayiyu.

Anthu ena atatu amene sadafune tiwatchule maina, adati chifukwa cha kusintha kwa ndondomekoyi, iwo agulutsa zipangizo zomwe adalandira kuchokera kuboma.

“Ndinalandira malata 30 ndi matumba 30 a simenti ndipo ndimadikirira ndalama zomangira nyumba koma mpaka lero kuli zii. Ndangogulitsa matumbawo moti angotsala asanu ndi malata 20,” adatero mkuluyo.

Koma izi zikudabwitsa Vintulla, yemwe wati zomwe akukamba anthunzi ndi zosiyana ndi mgwirizano womwe boma lidapanga ndi iwo.

“Ndi zoona kuti akalandira zipangizo, boma lizipereka ndalama yomangira nyumba. Ndalama yake ndi K50 000, osati K190 000, monga akukambira ndipo ndalamayi tidatumiza kale m’maboma awo,” adatero Vintulla.

“Munthu aliyense akumayang’ana yekha womanga, ife tikumangopereka K50 000 yoti amangire. Ngati womangayo wawatchaja ndalama zambiri, ife tidzaperekabe K50 000,” adaonjezera Vintulla.

Pokambapo pa za anthu ena amene akugulitsa zipangizo zawo, iye adati palibe chosintha, anthuwo adzaperekabe gawo lawo kuboma ngakhale katunduyo wagulitsidwa.

“Ndondomekoyi ndi yothandiza anthu ovutikitsitsa, iwo ndi boma aliyense akuperekapo theka kuti nyumba imangidwe. Ngati agulitsa zipangizo, adzaperekabe mbali yawo,” adatero.

DC wa boma la Ntcheu, Harry Phiri adati akuyenera afufuze kaye ngatidi alandira ndalamazo. “Paja ndili paulendo wopita ku Phalombe, ndiye ndikuyenera ndifufuze kaye,” adatero.

DC wa boma la Nkhata Bay, Alex Mdooka adati kumeneko alandira ndalamazo Lolemba lathali.

“Tangolandira kumene Lolembali, koma zipangizo ndiye zidafika kale. Apa ndiye kuti anthu akuyenera apatsidwe ndalamazi kuti ayambe kugwiritsa ntchito,” adatero.

T/A Nkhulambe wa ku Phalombe akuti kumeneko palibe chachitika ngakhale madera ena anthu ayamba kusangalala ndi ndondomekoyi.

“Maina adalemba kalekale, koma mpaka lero palibe walandirapo malata kapena simenti. Sitikudziwa kuti vuto n’chiyani. Anzathu ku Mulanje adalandira kalekale koma kunoko palibe chikuchitika,” adatero.

Chimodzimodzi Senior Chief Kanduku ku Mwanza akuti nakonso ndalama zoti anthu amangire nyumba sizidafike kumeneko koma zipangizo zokha.

Ndondomeko yopereka zipangizoyi ikuyembekezeka kupindulira anthu 80 m’dera la phungu aliyense wa Nyumba ya Malamulo.

Pachiyambi penipeni anthu amaganiza kuti boma lidzatsitsa mtenngo wa malata ndi simenti monga ankakambira panthawi ya kampeni, koma mapeto ake boma lidasintha kuti ndondomekoyi ikhala ya anthu ovutikitsitsa okha, osati aliyense. n

Related Articles

Back to top button