Chichewa

Atenge basi ndani?

Listen to this article

Matimu a Nyasa Big Bullets ndi Mighty Be Forward Wanderers Lolemba akhala akukumana pampikisano wa Basi Ipite Soccer Fiesta wolimbirana minibasi ya K25 miliyoni pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.

Mkulu wa Luso TV Dick Juma Lachinayi adati basiyo, imene idafika m’dziko muno Lachinayi, ipitirira kusungidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM) mpaka wopambana apezeke.

Ilowera kwa ndani?: Wachiwiri kwa wapampando wa Bullets (kumanzere) Austo Kasito ndi Christo Kananji wachiwiri kwa mlembi wa Manoma

“Basi ndi imeneyi yafika lero ndipo mawa (Lachisanu) ikaperekedwa m’manja mwa FAM kuti ayisunge,” adatero Juma.

Iye adati adasankha matimuwa kaamba ka mavuto a mayendedwe omwe ali nawo ndipo akufuna kupereka mwayi woti opambana adziombole kumavutowa.

Masewero achibwereza alipo pa January 1 2017 ku Civo Stadium mumzinda wa Lilongwe. n

 

Related Articles

Back to top button