Nkhani

Atenge ligi yaTNM ndani?

Listen to this article

Akatswiri pa zamasewero ndiye akamba, aphunzitsi nawo ndi ochemerera alosera zambiri koma kamuna adziwika lero nthawi ikamati 4:00 madzulo ano.

Zonse ndi lero pamene timu ya Big Bullets ndi Moyale Barracks akumane lero pa Kamuzu Stadium masewero amene angadziwitse katswiri wa ligi ya TNM ya chaka chino.bullets

Bullets ili ndi mapointi 56 ndipo yatsala ndi masewero awiri, oyamba ndi a lero ndipo imalizitsa sabata ya mawa ndi Blantyre United yomwe yatuluka mu m’ligiyi.

Moyale ili ndi mapointi 53, nayonso yatsala ndi magemu awiri, yoyamba ndi ya lero ndipo imalizitsa ndi Blue Eagles yomwe ikuphupha kuti ithere panambala 3 m’ligiyi.

Ngati Moyale ipambane lero ndiye kuti ligiyi tidikirabe sabata yamawa kuti ithe pamene matimuwa akudzasewera masewero awo womaliza.

Kulepherana mphamvu kwa matimuwa lero kapena ngati Bullets ipambane zipereka chilimbikitso kuti Bullets yatenga ligiyi.

Izi zikusonyeza kuti Moyale ikuyenera kupambana masewero alero ngatidi yathemba zotenga ligiyi. Moyale ikapambana ndiye kuti nkhondo ikhala pa zigoli zochinya ndi zochinyitsa komanso mapointi atatu amene atsala m’masewero asabata ya mawa.

Bullets yachinya zigoli 41 ndipo yachinyitsa zigoli 18. Moyale yachinya zigoli 43 ndipo yachinyitsa zigoli 22. Izi zikutanthauza kuti Moyale ikachinya Bullets ndi chigoli chimodzi komanso kudzachinya Eagles ndi chigoli chimodzi ndiye kuti Bullets ikuyenera kudzachinya Blantyre United ndi zigoli zoposa ziwiri kuti itenge ligi.

Apa nchifukwa ligiyi ili ya masamu zomwe Nicholas Mhango wa Moyale komanso Elijah Kananji wa Bullets akunenetsa kuti ndi bwino kupambana kuti nkhondoyi ichepe.

Masewero andime yoyamba, Bullets idapambana ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi ndipo masewerowa adachitikira ku Mzuzu. Lero ndi Kamuzu Stadium yomwe inyamule ntchitoyi.

Related Articles

Back to top button