Utsi ku Nam pamene ma Queens anyamuka

Utsi ukufukabe ku bungwe loyendetsa masewero a ntchemberembaye la Netball Association of Malawi (NAM) kaamba kosemphana zochita pakati pa mphunzitsi wa timuyi Peace Chawinga-Kalua ndi bungweli. Timu ya ntchemberembaye yomwe imangodziwika kuti Malawi Queens idanyamuka m’dziko muno Lachitatu m’sabatayi ulendo ku Sydney m’dziko la Australia komwe ikukapikisananawo m’chikho chapadziko lonse. Kugwebana kudayambika pamene zidadziwika kuti…

Mkulu wa zaka 22 akaseweza zaka 23

Wakhala akuthyola nyumba masana kasanu konse ndi kubamo katundu. Anthu ku Balaka akhala akumusaka koma adali woterera ngati mlamba. Koma la 40 lamukwanira John Bunaya, wa zaka 22, amene bwalo la milandu lamuthowa ndi zaka 23 kuti akaseweze kundende chifukwa cha kutolatola. Wapolisi woimira boma pamilandu, Inspector Isaac Mponela, wati bwalo la Balaka lidapeza mkuluyu…

Zavutanso ku Mozambique

Othawa nkhondo ayamba kufika m’dziko muno Zavutanso ku Mozambique. Nkhondo ya pachiweniweni pakati pa otsatira chipani cholamula cha Frelimo ndi chotsutsa cha Renamo yagundikanso ndipo nzika zina za m’dzikomo zayamba kuthawa nkhondo kukhamukira m’dziko muno pofuna kupulumutsa miyoyo yawo. Koma ngakhale izi zili choncho, mtendere sadaupezebe. Ambiri akugona kumimba kuli pepuu, alibe zovala, zofunda komanso…

Angry mob stones Mikolongwe College

Villagers from Saidi Village, Traditional Authority (T/A) Nkalo in Chiradzulu District on Tuesday afternoon invaded Mikolongwe College of Veterinary Science where they destroyed property, infrastructure and beat up the college principal and two guards. Limbe Police spokesperson Chifundo Chibwezo confirmed the development, but asked for more time, saying investigations to establish the cause of the…

NAM wrangles worry sponsors Airtel MW

Airtel Malawi, official sponsors of the Malawi Netball team, the Queens, have said they are worried with the continued wrangles involving Netball Association of Malawi (NAM) and some members of the team. Airtel concerns follow misunderstanding that arose between the Queens coach Peace Chawinga-Kalua and NAM over squad selection. Speaking at Chileka International Airport in…

A khonsolo ndi ankhanza—Amalonda

Ena mwa ochita malonda (mavenda) m’misewu ya mumzinda wa Blantyre alira ndi khalidwe la akhonsolo ya mzindawu kuti akuwachitira nkhanza ngati Malawi si dziko lawo. Pocheza ndi Msangulutso mavendawa akuti akupempha khonsoloyi kuti iwaganizire, maka iwo amene akuchita mabizinesi ang’onoang’ono. Koma mneneri wa khonsoloyi, Anthony Kasunda, akuti sadalandirepo dandaulo lililonse kuchokera kwa anthuwa. Iye wati…

Mayi wamalonda avulazidwa ku bt

Titha Masamba, wa zaka 31, akumva ululu wadzaoneni. Kuti ayende akuyenera agwirire ndodo; sangagone chafufumimba koma chammbali kapena chagada; moyo wamtendere watha. Akuti izitu zili chonchi chifukwa cha bala lomwe lili pabondo lake la kumanja lomwe lidasokedwa kuchipatala pambuyo pokhapidwa ndi chikwanje. Ulendo wa mayiyu wokagulitsa mandasi pa 7 July ndi womwe udabweretsa mavutowa pomwe…

Ulimi wa tomato, kabichi ndi nyemba wakolera

Alimi abebetsa ulimi wa tomato, kabitchi komanso nyemba m’boma la Ntcheu pamene ulimi wa m’madimba wachiwiri wayambika. Boma la Ntcheu, lomwe lachita malire ndi Dedza komanso Balaka, lili ndi anthu pafupifupi 700 000 tsopano malinga ndi chiwerengero cha anthu cha mu 2010. Ambiri mwa anthuwa ndi alimi ndipo ulimi wa nyemba, tomato, mbatata ya kachewere…

‘Jersey No. 8 ndiyo idandigwetsa m’chikondi’

Olemba, lembani. Veronica Mukhuna lero wasintha dzina ndipo ndi Veronica Zakazaka. Za mpira zenizeni, pamene Gomezgani Zakazaka, woyendetsa za mipikisano kubungwe la Football Association of Malawi (FAM) waveka ukaputeni duwali. Si zoona ayi momwe July akuchitiramu kuti Gome azikhalabe yekha. Mulungu wamphamvu, iye wakumana ndi Jersey No. 8. Kungotchula chonchi kusukulu ya Polytechnic ndiye kuti…

Atenge ligi yaTNM ndani?

Akatswiri pa zamasewero ndiye akamba, aphunzitsi nawo ndi ochemerera alosera zambiri koma kamuna adziwika lero nthawi ikamati 4:00 madzulo ano. Zonse ndi lero pamene timu ya Big Bullets ndi Moyale Barracks akumane lero pa Kamuzu Stadium masewero amene angadziwitse katswiri wa ligi ya TNM ya chaka chino. Bullets ili ndi mapointi 56 ndipo yatsala ndi…

K5 biliyoni yothana ndi matenda a mkungudza

Bungwe la Queen Elizabeth Diamond Jubilee Trust (QEDJT) lapereka ndalama zokwana K5 biliyoni kuboma la Malawi zogwirira ntchito yothetsa matenda a khungu otchedwa mkungudza (trachoma) m’dziko muno. Potsimikiza nkhaniyi, m’neneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe, wati boma ligwira ntchitoyi ndi mabungwe angapo, kuphatikizapo lodziwika bwino m’dziko muno la Sightsavers, lomwe lidalandira ndalamazi. Ntchitoyi, yomwe…

Blantyre welcomes back Thoko Suya

  The 2009 memories of when she last performed on stage are still flesh to fans who love Thoko Suya’s music. And on Sunday, fans gathered at Robin’s Park in Blantyre to witness the CD and DVD launch of Suya’s third album Adzandinyamula. Of course, not a lot of people attended the show, but the few who…

Chifunga pa za boma la fedulo

Nkhungu yowirira yakuta tsogolo la boma la fedulo (Federalism) lomwe magulu ena mdziko muno akufuna pamene ena sakugwirizana ndi maganizo otero. Maganizo a boma la fedulo adabwera chifukwa choti anthu ena akuganiza kuti pali tsankho pa kagawidwe ka maudindo ndi chitukuko m’dziko lino. M’busa Peter Mulomole, yemwe ndi mneneri wa bungwe  la anthu a chipembezo…

Boma lisakaza K1bn pa katundu wachabe

  Pomwe ntchito za maphunziro zikupitirira kukumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana, kwapezeka kuti katundu wina wophunzitsira, yemwe boma lidagula ndi ndalama zoposa K1 biliyoni m’chaka cha 2011, akungokhala m’nyumba zosungiramo katundu kaamba koti ndi wachabechabe. Mneneri wa unduna wa zamaphunziro, Manfred Ndovie, komanso mkulu wa bungwe loona zakuti maphunziro akuyenda bwino la Civil Society Education Coalition…

K85 000 kapena chaka kundende atapha galu

Ena amangopha agalu koma sapatsidwa chilango, koma khoti la Ulongwe Majisitireti ku Balaka lalamula kuti mfumu ina ilipe K85 000 apo ayi, ikakhale kundende chaka chimodzi kaamba kopha galu ndi kuwononga mmera m’dimba la mkulu wina. Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka, Joseph Sauka, mfumuyi ndi Peter Kasanga koma dzina lake lenileni ndi Michael…

George Nyirenda: Za Flames waiwalako

Zambiri zakhala zikulankhulidwa za George Nyirenda amene akusewera mu Caps United m’dziko la Zimbabwe kuti atengedwe ku Flames. Iye mwini wakhalanso akufunitsitsa ataitanidwa koma makochi a Flames amangomupatsa nkhongo. BOBBY KABANGO adacheza naye komanso pa za mphekesera yomwe yamveka kuti akubwera kudzasewerera Bullets: Moyo uli bwanji ku Caps? Zonse tayale madala koma nditangofika kumene ndiye…