Adzudzula JB zomanga mfumu

Mphunzitsi wa za malamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College Mwiza Nkhata wati ndi zodabwitsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda walamula apolisi kuti anjate T/A Chimombo ya ku Nsanje. Nkhata wati ngakhale pulezidenti ndi komanda wa asilikali ndi apolisi, sakuyenera kutero chifukwa kunjata munthu kumafunika kufufuzidwa kaye kunjatako kusadachitike. Banda Lachiwiri adalamula apolisi kuti…

Sabatayi yakhala yomvetsa mutu ndi nkhani ya Gabadihno Mhango. Zachitika m’sabatayi aganyu zatiwawa ndipo tikufuna bungwe la FAM komanso timu ya Big Bullets afotokoze bwino za zaka za Gaba. Sitikumvetsa zomwe lero FAM ikunena. Kuyambira chaka chatha mpaka lero zakhala zikumveka kuti matimu akunja agwa m’chikondi ndi Gaba. Aliyense amadziwa kuti zikapsa Gaba anyamuka m’dziko…

Chalaka bakha nkhuku singatole. Linda madzi apite ndiye udziti wadala. Miyambiyi ndiyo idatsanuka m’sabatayi kaamba ka jombo yomwe idathudzula Nyerere komanso kudiriza Maule mwachipongwe. Oyambirira kudandaula ndi jombo adali neba winayu ku Zomba kumene amati zikamuyendera. Iye adanyang’wa kuti adadya kale mkango wa umuna ndipo udatsala ndi waukazi koma awo adali maloto amasana chifukwa pakutha…

Amalawi apindulanji ndi kutsogolera Sadc

Akuluakulu pa zachuma komanso mafumu m’dziko muno ati mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda afunika masomphenya kuti dziko lino lipindule pamene ali wapampando wa mgwirizano wa maiko a kumwera kwa Africa wa Southern Africa Development Community (Sadc). Banda wangosankhidwa sabata yathayi pamsonkhano wa Sadc omwe umachitikira ku Lilongwe komwe atsogoleri a maiko 14 adasonkhana. Aka…

Chikho cha Carlsberg chafika pachimake

Thambo lagwa, chikho cha Carlsberg chaka chino chabwera ndi zake pamene anyamata ovala jombo atenga malo kugwedula matimu omwe amakula mtima. Chikhochi tsopano chafika m’ndime ya semifayinolo pamene dzulo Evirom imakumana ndi Red Lions pa Kamuzu mumzinda wa Blantyre. Lachitatu Big Bullets idatulutsidwa ndi Kamuzu Barracks ku Dedza 1-0 Bullets itapha Silver Strikers ku Kamuzu.…

Marvellous Deeds 3rd album launch Sunday

All is set. The much-awaited time has come for Blantyre fans as the Lilongwe-based Marvellous Deeds will be launching their third album Sanathane Nane at Robins Park this Sunday, August 25. The CD was launched in Lilongwe on July 7at the Sheaffer Marquee. “This is the time for our Blantyre fans and surrounding areas to…

Aika mwala wa maziko kawiri pachipatala

Lolemba m’sabatayi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adatsogolera anthu a m’boma la Ntcheu pomwe amayala mwala wa maziko pa chipatala cha amayi apakati. Kuyala kwa mwalaku kumadza mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Callista Mutharika atayalanso mwala wamaziko pamalopo m’mbuyomu. Mutharika adalonjeza ndalama pafupifupi K18 miliyoni zomwe amati zimangire chipatalacho pomwe Banda adalandira…

La 40 lakwana. Zochitika ku Zambia komwe Flames imakapikisana nawo mumpikisano wa Cosafa zadziwika. Kumeneko Flames idataya bomwetamweta koma ati idatenga mapointi onse kwa mahule. Asungwana a pa Zed tidatenga malo kumeneko ati mpaka kukwera nawo basi ya Flames uko akuyamikira anyamatawa ndi makochi kuti amasewera bwino. Timaganiza kuti poti akwera nawo basiyo ndiye kuti…

Apereka ambulansi ku Bangwe

Kwa kanthawi anthu makamaka amayi oyembekezera akhala akuvutika mayendedwe popita ku chipatala cha Bangwe Clinic mumzinda wa Blantyre. Anthu omwe amavutikawa ndi omwe akukhala ku Mpingwe ndi Mvula chifukwa kumaloko sikufika ma minibasi kaamba koipa kwa msewu. Pano mavutowa tsono angakhale mbiri yakale pomwe anthuwa alandira minibasi komanso ambulance yomwe idziyenda kumeneko. Zinthuzi zaperekedwa ndi…

Kati deru kadazizwitsa mlenje. Ife aganyu tadzidzimuka ndi ganizo la mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet yemwe tsopano wanena kuti sakufunanso K3.3 miliyoni akakapuntha Nigeria pa 7 September. Ife tidayamba kutolera za m’mageti kuti pofika pa 7 zikhale zitakwana koma lero kudzidzimuka akuti ndalama ayi. Ah ah ah! Zataninso wawa? Pamene Uncle Tom amabwera adagwirizana ndi…

Chalaka bakha nkhuku siyingatole. Nkhani ya Gabadinho Mhango ndi Lucky Malata ndiyo yatinenetsa mwambiwu. M’sabatayi nkhani idawawasa ndi ya anyamatawa omwenso amasewera Flames. Akamunawa akadatola chikwama pang’onong’ono ku Joni koma ena alepheretsa. Aganyu sitinadandaule koma pena sitikumvetsa njomba yomwe yaseweredwa apa. Ife sitidamvepo wosewera chigawo cha pakati atalowera kummwera kukayesa mwayi ndi Blantyre United koma…

Chisankho chanunkhira, koma ku MCP kuli chuuu!

Pamene anthu m’madera ena ayambe kulembetsa maina awo m’kalembera wa chisankho cha magawo atatu cha chaka chamawa Lolemba likudzali, sizidadziwikebe tsiku lomwe chipani chachikulu chotsutsa cha MCP chichititse msonkhano wake waukulu pokonzekera chisankho. Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa za msonkhano waukulu (konivenshoni) wa chipanichi, Joseph Njobvuyalema, wati akomiti akudikira pulezidenti wa chipanichi, John Tembo, kuti…

Wrangle over Bvumbwe chieftaincy

Controversy continues to chase Traditional Authority (T/A) Bvumbwe of Thyolo after a family has accused his clan of robbing them of the chieftaincy. The Mphedzu family of the area has sought the intervention President Joyce Banda to redress what they believe is great injustice. Village head Mphedzu told Nation on Sunday on Friday that he…

Malawi wapindulanji muzaka 49?

Pamene dziko lino lero likukumbukira kuti lakwanitsa zaka 49 lili pa ufulu wodzilamulira, Amalawi ena ati ngakhale pali zina zolozeka kuti zikuyenda, zambiri zaphotchoka chifukwa cha dyera la andale ena omwe kwawo nkudzikundikira chuma. Maiko omwe sadasiyane ndi Malawi potenga ufulu wawo mu Africa muno ndi monga Botswana (1966, Mozambique 1975), South Africa (1961), Tanzania…

Nkhani yavuta m’sabatayi ndi ya Nyerere kuti zidagenda pomwe zimasewera ndi Blue Eagles. Aganyu sitivomereza kugenda ndipo tafuna timvetsetse chomwe woimbira masewerowo Fransisco Scova adalakwa kuti nthawi zonse nkhani idzikhala yake. Scova adamenyedwa ku Mwanza pa 30 May 2013 poimbira mpira wa Ntelo ndi Chinangwa Madrid. Osewera a Ntelo adakupa Scova ati amakondera Chinangwa. Iye…

Ntchito yomanga njanji yochoka ku Kachaso kupita ku Nkaya ayiimitsa mpaka kampani ya  Mota-Engel ndi ogwira ntchito kukampaniyo atamvana chimodzi. Ogwira ntchitowo akunyanyala pofuna kukakamiza mabwana awo kuti awakwezere malipiro komanso kuti nzika 300 za ku Thailand zipakire. Kunyanyalaku kudayambira Lolemba pa 24 June ndipo Lachiwiri Nduna ya za Ntchito Eunice Makangala idatsetserekera kumeneko kukalankhula…

Mmodzi mwa akatswiri a za malamulo Edge Kanyongolo wati lamulo lomwe likukamba za katundu ndi chuma cha atsogoleri a dziko liunikidwenso ndi cholinga chopatsa mphamvu zochuluka kwa Amalawi akafuna kufufuza atsogoleri omwe akugwiritsa ntchito maudindo awo podzikundikira chuma. Izi zadza pamene dziko la Malawi ladzidzimuka ndi kuchuluka kwa chuma cha mtsogoleri wakale wa dziko lino…