Nkhawa akafuna kudzathandiza

  Ngati satenga madzi kunyumba, amavutika akafuna kuchita chimbudzi chifukwa kumalo awo antchito kulibe madzi. Ichi ndi chibalo chomwe ogwira ntchito kunthambi yosunga katundu wa boma ku Blantyre, Central Government Stores, akuchita chifukwa bungwe la Blantyre Water Board (BWB) lidadula madzi mu March chaka chino. Apa n’kuti madziwo atangotuluka mu January ndi February kuchokera pamene…

Kwin Bee: Kulimbikitsa ufulu wa atsikana

Atsikana oimba chamba cha Afro ndi hip hop alipo ndithu m’dziko muno, koma munthu wotchula mndandandawu amayenera kusololetsa milomo yake chifukwa muli Kwin Bee. Uyu ndi mtsikana yemwe watchuka ndipo wavekedwa chisoti chomenyera ufulu akazi kutsatira nyimbo ya Ndadutsa Pompo yomwe adaimba ndi anzake. Nyimboyi imayankha mwano wa anyamata kwa atsikana womwe uli mu Wadutsa…

Aganyu okhala ndi ziphaso

Mwa zina zidabweretsa mawu woti tawuni ya Limbe imalira ochenjera, ndi kuberedwa kwa katundu ndi munthu yemwe udamukhulupirira kuti akunyamulire, wa ganyu. Tsopano padepoti ya Fumbi pali dongosolo lowumbanso chikhulupiriro chomwe chidagumuka pakati pa aganyu ndi mabwana komanso madona. TEMWA MHONE adakumana ndi Kassimu Sitande, mkulu wa anyamatawa, ndipo adacheza motere: Akutanthauza chani anyamatawa ponena…

Apempha anthu kupanga manyowa

  Sukulu ya aphunzitsi Development Aid from People to People (Dapp) Chilangoma ku Blantyre yapempha anthu kupanga manyowa kuti akhale ndi mbewu zathanzi komanso zochuluka. Mkulu wa mapologalamu pasukuluyo, Hope Funsani, adanena izi Lachiwiri pamwambo wopereka chimbudzi chamakono m’dongosolo la School Garden and Nutrition (SGN) pa sukulu ya pulaimale ya Samama m’mudzi mwa Kamowa kwa…

Engage certified electrical installers, advises Mera

Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) has appealed to the public to engage certified electrical installers to ensure safety of  lives and their properties. Mera board chairperson the Reverend Joseph Bvumbwe said this on Tuesday in Blantyre during a stakeholders’ awareness meeting on the new regulatory framework for renewable energy and electrical installers. He said people…

Minibasi zikwera Mwachinunu

  Nthawi zonse minibasi zikamakweza mtengo, makamaka mafuta akakwera, bungwe la eni minibasi limalengeza, ndi kuika mitengo ya minibasi kuti aliyense adziwe. Koma kuchokera Loweruka lapitalo, mitengo ya minibasi m’madera ena idakwera mwachinunu. Izi zidachitika patangotha tsiku limodzi kuchokera pomwe oyendetsa minibasi adanyanyala ntchito zawo ati pokwiya ndi zilango zina zimene amalandira akaphwanya malamulo a…

‘Kunyalanyaza kudzetsa ngozi’

Sabata yangothayi ngozi zidakuta dziko lino pomwe anthu 17 adafa. Pamene anthu amati akhazikitse mitima pansi, anthu 8 atafa pa ngozi ya basi pamlatho wa Rivirivi ku Ntcheu komanso anthu 4 adamwalira ku Bunda ku Lilongwe ndi 4 kwa Magalasi mumzinda wa Blantyre, Lachisanu kudalinso ngozi ina mumzinda wa Blantyre pomwe munthu mmodzi adamwalira. Ndipo…

Afufuza za mkalabongo

Zambiri zakhala zikukambidwa za mkalabongo, mowa waukali umene suchedwa kutenga amene akuumwa koma tsopano, makampani 21 akufufuzidwa pamadandaulo amene Amalawi amakhala nawo. M’sabatayi, bungwe loona za chilungamo pa malonda la Competition and Fair Trade Commission (CFTC) lidatulutsa chikalata chopempha Amalawi kupereka madandaulo awo pa makampani otcheza mkalabongowo. Akuluaku a mabungwe amene akhala akulimbana ndi mowawo,…

‘Sitilembetsa mayeso’

Aphunzitsi amene alembetse mayeso a Fomu 4 a chaka chino omwe ayambe pa 22 June, aopseza kuti sadzagwira ntchitoyo ngati Unduna wa Maphunziro salandira ndalama zomwe amapatsidwa akamapita kutchuthi. Izi zikudza pamene ophunzira ndi makolo ena m’sukulu za pulaimale akudandaula kuti sitalaka ya aphunzitsi isokoneza kukonzekera mayeso a temu yachitatu omwe ayambe kumayambiriro kwa mwezi…

Apolisi mbweee! ku PAC

Kwa munthu wongofika kumene mumzinda wa Blantyre, ngakhale nzika za mzindawu, sabata imene yangothayi kudali chitetezo chokhwima zedi pomwe apolisi adali ponseponse. Kuyambira m’mawa, apolisi adali ndi ma ‘rodibuloku’ adzidzidzi m’madera ena. Mmodzi mwa anthu okhala ku Machinjiri, Leston Kampira, Lachitatu adati adadabwa ndi mndandanda wa galimoto umene udalipo pa Wenela. “Tidayenda pang’onopang;ono mpaka kukafika…

Farmers bemoan poor milk prices

  Farmers in the country have bemoaned poor milk prices offered on the market. They made the remarks on Thursday during World Milk Day commemorations held at the Malawi University of Science and Technology (Must) football ground in Thyolo. One of the farmers, Elizabeth Chitimbe of Namahoya Milk Bulking Group in Thyolo, said they do…

‘Ndalama zaperewera m’magawo ofunikira’

Ngakhale maunduna a zamalimidwe, umoyo ndi maphunziro alandira ndalama zochuluka kwambiri mundondomeko ya momwe boma liyendetsere chuma kuyambira pa 1 July chaka chino mpaka pa 30 June chaka cha mawa, akadaulo a nthambizi ati ndalama ndi zochepa kupititsa patsogolo ntchito za maundunawa. Izi zikudza pomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo alowa m’milaga kukambirana ndondomeko ya…

Apolisi ati miyoyo ya anthu ikupululuka kaamba ka matola omwe akuchulutsa ngozi pa msewu. Malingana ndi chikalata chomwe apolisi atulutsa posachedwa, kugwiritsa ntchito galimoto zonyamula katundu potengera anthu ku masewero, ukwati, maliro si kovomerezeka. Chikalatachi, chomwe wasayinira ndi mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera, chikukumbutsa madalaivala kuti aziyendetsa anthu pa galimoto zoyenera monga maminibasi…

Chipembedzo chikukolezera kupemphapempha m’misewu

Kukhulupirira chipembedzo kukukolezera mchitidwe wopemphapempha m’misewu, zimene zachititsa kuti ntchito yochotsa opemphawa ivute, watero mkulu wa bungwe limene limachotsa ana m’misewu la Chisomo Children’s Club. Ngakhale boma lakhala likulengeza kuti aliyense wopezeka akupemphetsa m’misewu adzamangidwa, izi sizikutheka. Sabata zingapo zapitazo, bomalo limalengeza mozungulira mzinda wa Blantyre kuti aliyense wopezeka akupereka ndalama kwa opemphetsa adzamangidwa. Koma…

CDF ikuthera kugulira kwale ku Neno

Thumba la chitukuko cha boma la Constituency Development Fund (CDF) m’dera la kummwera kwa boma la Neno likuthera kugulira miyala ya kwale mumapulojekiti a bungwe la Build On zomwe n’zosemphana ndi ndondomeko zoyendetsera thumbali. Anthu m’derali akuti phungu wawo Mary Khembo amagwiritsa ntchito ndalama za CDF pa lonjezo lake lopereka kwale omangira zipinda zophunzirira zomwe…

Kulira, chimwemwe  ndi banki m’khonde

Ngakhale adali ndi chidwi choyamba bizinezi kuti atukuke, kusowa kwa mpamba kumapondereza khumbolo. Sanderson Yuba wa m’mudzi mwa Namalima kwa T/A Nazombe m’boma la Phalombe adakanika kutenga ngongole kubanki kaamba kosowa chikole komanso kuopa chiongola dzanja chokwera. Lero mkuluyu ndi mmodzi mwa makhumutcha m’deralo kutsatira ngongole yomwe adatenga kubanki m’khonde ndi kuyamba bizinezi ya matabwa…