Nkhani

Bajeti yosadalira ena iphwasuludwa

Listen to this article

Kwatha! Ndondomeko ya chuma (bajeti) yosadalira thandizo la maiko akunja ikhadzulidwa, boma latero.

Nduna ya zachuma, Ken Lipenga yanena izi pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe Lachiwiri lathali pa 8 Meyi.

Polankhulapo, Lipenga adavomereza kuti ndondomekoyo sinkayenda n’komwe. Zidali za mkutu za zii zopanda ndi mchere omwe.

Lipenga wati zimafika pena poti boma limakabwerekera ndalama kudzasokerera zigamba bajetiyo, kuti chuma chisaonekere mberewere.

Mwachitsanzo bungwe lotolera msonkho la MRA linafika pobwereka ndalama ku ma banki kuti likwanilitse zofuna za boma mu bajeti.

Ndunayi yati ndondomekoyo idadza chifukwa maiko ndi mabungwe akunja sadathandize dziko lino ndi ndalama zoti ziyendetsere nkhani zachuma m’mchakachi potsatira kusemphana maganizo ndi abwenzi a Malawi.

Iye adati pano maiko ndi mabungwe omwe amathandiza dziko lino anenetsa kuti athandiza dziko lino ndi ndalama zomwe zithandizire ndondomeko yazachumayo kusonyeza kuti dziko lino liyamba kugwiritsa ntchito ndondomeko yakale yomwe idzithandizidwa ndi abwenziwa.

Apa abwenziwa ati boma lifufuze nkhani yoti a bungwe lotolera misonkho lidafika pokaputa ngongole ya K4 biliyoni ku mabanki kuti lipereke chithunzithunzi kuti ndondomekoyi ikuyenda.

Ndondomeko yosadalira maiko akunjawa idayamba muulamuliro wa mtsogoleri wakale, malemu Bingu wa Mutharika yemwe adati dziko lino latha zaka zambiri litadziimira palokha kotero sikungakhale kulondola kuti lidzidalirabe thandizo la maiko akunja.

Related Articles

Back to top button