Chichewa

Basi ayisempha

Listen to this article

Tsiku limenelo sitidakhale pa Wenela. Palibe ojiya, osolola, osenza ndi oitanira amene adatsala pa Wenela.
Tidakwera galimoto la mkulu wina kulowera ku Lilongwe. Si kuti timapita kuja kulikulu la boma kumene masamu ogula mmera asokonekera.
Sindingakambe nkhani imeneyo chifukwa tonse tikudziwa kuti lingaliro la Dizilo Petulo Palibe, malinga ndi kufotokoza kwa Joloji Chiponda, lidali logula chimangacho ku Brazil. Zoona mpaka kuoda chimanga ku Brazil!
Nkhani ya chimangayi kwa ine ndiyongotaya nthawi. Ngati Moya Pete adalamula asilikali ake kukwidzinga uja wogona ndi amayi oposa 100 bwanji akulephera kulamulanso amene akuganiziridwa kukazinga mmera wa tonse pano pa Wenela?
Zosamveka konse kuti mzimayi woti akufuna kugula chimanga choti adye pakhomo pake, mmalo mopita yekha kumsikako kutuma wina kuti akamugulire kenako nkumadandaula kuti waberedwa!
Abale anzanga, tingoyerekeza kuti mwalemba wantchito, ndiye mukumukaikira kuti anaba ndiwo. Kenako mukuuza akazi kapena amuna anu kuti afufuze momwe anabera ndiwozo, wantchito wanu akapita pachulu n’kumakuwa kuti: “Sindinabe ine! Sindinabe!”
Chomwe ndimadabwa pano pa Wenela n’chakuti n’chifukwa chiyani aliyense amafuna kutalika zala pankhani za chimanga? Tidamvapo kuti Adona Hilida adagulitsa matani ochuluka kupita nawo ku Kenya. Nanga za Thursday Jumbo uja naye adadyapo zake za chimanga. Za makuponi ndiye ndisachite kunena.
Nsataye nazo nthawi izo.
Chaka chino talowa
Talowa ndi adani omwe
Akufuna moyo wanga
Kuti aononge
Chauta thandizeni…
Iyi ndi nyimbo imene tinkamvera mugalimoto ya mkulu amene adatitenga. Tidafika kubwalo la mpira latsopano kumene zipolopolo ndi nyerere zimamenyana. Inu, munthu n’kupha nyerere poyiwombera!
Ndidangomva kuti ena adathyola mipando, kutenga makalilole ndi zina zotero! Komanso abambo ena ankalowa kuzimbudzi za akazi!
Utatha mpira, sindikudziwa kuti udatha bwanji, Abiti Patuma adandikoka kuti timuthawe mkulu uja.
Tidakakwera basi imene sindikuyidziwa bwino. Mudali anyamata a Chimwemwe kwambiri. Iwo amangoti 5 kwa 1, 5 kwa 1. Onse atamuona Abiti Patuma adakuwira limodzi: “Abiti Patuma! Yo-yo-yo!”
Wina adamukumbatira, wina kumupsopsona patsaya.
“Osadanda, mwayiphula basi! Ndikuthangatani nonse m’basi momwe muno,” adatero Abiti Patuma.
Koma abale! Kudalitu kulandirana! Basi imamveka ndithu kuti mashoko siali bwino komabe mmodzimmodzi adali kulandira chithandizo kuchokera kwa Abiti Patuma.
Adati tinyamuke, ulendo wobwerera pa Wenela.
Tili m’njira, yemwe amaoneka kuti ndi mkulu wa anyamatawo adati: “Tikakafika ku Mwanza, tikadzera kwa Ayaya tikayamike chifukwa watithandiza kupeza basi.”
Ulendo wa kwa Ayaya sunatheke chifukwa basi idatchona pa Manjawira. Poyamba tinkadya kanyenya kuti mwina iyenda. Kenako kudali kusaka mango, ngumbi ndi zina mpaka mdima udagwa.
Zidayamba ngati basi. Anyamata aja adayamba kukuwa: “Abiti Patuma wasempha basi! Wasempha basi!”
Mwayi wake, mkulu uja tidamuzemba nkuti akudutsa. Tidadumphira m’galimoto lake. Wautali, mpaka ku Wenela. Gwira bango, upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button