Nkhani

Bingu apepese posathetsa mtima pa sitalaka

Pulezidenti Bingu wa Mutharika akuyenera kupepesa Amalawi pa zokhoma zomwe aziona pomwe ogwira ntchito kumabwalo a milandu amanyanyala ntchito.

Mkulu wa bungwe loona ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda komanso mphunzitsi wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Joseph Chunga, anena izi m’sabatayi.

Izi zadza pamene ogwira ntchito kumabwalo a milandu adayambanso ntchito zawo m’sabatayi patatha miyezi iwiri ndi theka akunyanyala ntchitozo pokwiya kuti boma limalephera kuwakwezera malipiro chonsecho Nyumba ya Malamulo inavomereza mu 2006.

Koma mneneri wa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Hetherwick Ntaba, wati maganizo a akuluakuluwa ndiopotoka komanso osowa nzeru.

Iye wati nkhani yomwe idalipo kudali kusamvana maganizo pakati pa mbali ziwirizi, kotero mbalizo zidakambirana ndikupeza mayankho ndipo boma silolakwa.

Koma Banda ndi Chunga ati Mutharika amangoonerera monse mmene anthu amaphwanyiridwa ufulu.

Iwo atinso ndibwino kuti ena apite kubwalo kukasumira boma kaamba kophwanyiridwa ufulu wawo wofuna chilungamo kumabwalo.

Mwa zovuta panthawiyi, iwo ati ena afera m’ndende kapena kukhala mopanikizika ndipo ichi n’chifukwa chokwanira kuti mtsogoleri wa dziko lino apepese mtundu wa Amalawi.

“Boma livomereze kuti zinthu sizidali bwino. Anthu akhoza kusumira boma pazimenezi. Kwachitika zambiri monga ziphuphu za belo komanso ena adwala ndikufa m’ndende,” adatero Banda.

Iye adati ndibwino amabungwe omwe siaboma akhalirane pansi ndikupeza thandizo kuti atolere zomwe zimachitika pomwe mabwalo adali otseka.

Chunga akuti monga atsogoleri ena anzeru amachitira m’maiko akunja, kukadakhala kwanzerunso Mutharika akadapepesa koma chachidziwikireni n’kuti sangayerekeze.

Iye wati anthu alisumire boma kaamba kowaphwanyira ufulu.

“Zingakhale bwino ena atasuma. Ngakhale kuli sitalaka kapena ayi komabe pakutha pa maola 48 munthu amayenera adziwe mlandu wake ndipo ngati n’koyenera apatsidwe belo.

“Ena atasuma zingapereke chenjezo kuboma pazomwe zidachitikazo ndipo ena sangadzazichitenso,” watero Chunga.

Koma Ntaba wati akuluakuluwa asayambe zosokoneza chifukwa nkhani ya mbali ziwirizi yatha ndipo amvana chimodzi.

Iye wati sakuona choti Mutharika apepesere pomwe sadalakwitse.

Limbani Kawombe wa m’mudzi mwa Kachepa T/A Likoswe m’boma la Chiradzulu wati n’chanzeru kuti Mutharika apepese chifukwa omwe adamuvotera amazunzika kundende asadapezeke ndi mlandu.

“Adakayenera kulankhulapo pomwe sitalaka imachitika koma sadalankhule zomwe zazunzitsa Amalawi,” adatero Kawombe.

Mneneri wa omwe amachita sitalakayi, Austin Kamanga wati iwo alibe zonena zambiri chifukwa agwirizana ndi boma kuti awapatsa K40 pa K100 iliyonse ya malipiro awo kuyambira 2006.

Kamanga adati boma lawatsimikizira kuti ndalamazi ayamba kulandira m’mwezi wa Epulo.

Iye adati ena adzalandira zonse pomwe ena azilandira pang’onopang’ono.

Kamanga adati sitalakayi yachulutsa mulu wantchito chifukwa pali milandu yambiri yomwe ikuyenera kukambidwa.

Malinga ndi iye, pangano lawo ndi boma n’kuti agwira ntchito mokhetsa thukuta.

Mabwalo a milandu adasiya kugwira ntchito pa 9 Febuluwale pofuna kukakamiza boma kuti likwaniritse zomwe Nyumba ya Malamulo idavomereza mu 2006 kuti malipirowo akwezedwe.

Zingapo zakhala zikuchitika pomwe anthu amalephera kutenga chiletso cha bwalo, ena amakanika kutulutsidwa pabelo, malipoti akhalanso akumveka kuti angapo amwalira m’chitolokosi akudikira milandu ndipo milandu yambiri yangokhala njiiii!

Ndende za dziko lino zimayenera kusunga oganiziridwa milandu 1 000 koma chiwerengerochi chakwera kufika pa 2 425.

Mneneri wa ndende m’dziko muno, Evance Phiri, wati chiwerengerochi chidakula makamaka m’ndende za Zomba, Chichiri, Mzuzu ndi Lilongwe.

Iye adati padali chiopsezo kuti chakudya chiyamba kusowa m’ndende kaamba ka kuchulukana.

Phiri adaonjeza kuti chiwerengero cha anthu m’ndende chakwana 13 425.

Phiri adati ndende za dziko lino mumayenera kukhala anthu a pakati pa 5 000 ndi 6 000.

Related Articles

Back to top button