Nkhani

Blantyre yawala, iwalirabe

Listen to this article

Kuyenda usiku tsopano sikukhalanso koopsa ganizo la khonsolo ya mzinda  wa Blantyre lipherezeke.

Mneneri wa khonsoloyi, Anthony Kasunda, wati khonsolooyi ikuganiza zoika magetsi m’misewu kuti aziwala usiku wonse mumzindawu.

Mmbuyomu ena adaba zitsulo za magetsi
Mmbuyomu ena adaba zitsulo za magetsi

Kasunda wauza Tamvani kuti pasadathe miyezi 6 msewu wa Masauko Chipembere Highway ukhala ndi magetsiwa kuchoka ku Blantyre mpaka ku Limbe.

“Anthu aona kuwala ndithu. Ife talowa mum’gwirizano ndi bungwe la Roads Fund Administration kuti tigwire ntchito imeneyi, yomwe idye ndalama zokwana K400 miliyoni,” adatero Kasunda.

Iye adati m’misewu ina ingapo ntchitoyi yagwirika kale.

“Tapanga kale kuchoka pa Kandodo Corner Shop mpaka pa Kameza Roundabout; Kwacha Roundabout mpaka pa Kudya kudutsa MBC TV, CI mpaka Green Corner; ndinso Sunnyside mpaka ku Manyowe.

“Ntchito imeneyi yatitengera ndalama pafupifupi K145 miliyoni, zomwe ndi gawo la K1.8 biliyoni zochokera kuboma za ntchito yachitukuko cha mumzinda wa Blantyre,” adatero Kasunda.

Mneneriyu adatinso khonsolo ikamapeza ndalama, ionetsetsa kuti misewu yonse ya mumzinda wa Blantyre ikhale ndi magetsi.

“Magetsi amathandiza kukhwimitsa chitetezo. Ndikhumbo la khonsolo ya Blantyre kuti mzinda ukhale wowala usiku. Tikumema anthu onse a mumzindawu kuti atithandize poteteza magetsi amenewa, makamaka potsina khutu apolisi kapena akulu a khonsoloyi akaona wina akuononga dala zipangizo zamagetsi monga mapolo ndi nthambo zamagetsi,” adaonjezera Kasunda.

Related Articles

Back to top button
Translate »