Nkhani

Boma, mafumu salabadira mavuto a Amalawi

Listen to this article

Kusapezeka kwa boma komanso mafumu ku zokambirana zomwe adaitanitsa a bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) sabata yatha kwaonetsa kusalabadira zoombola Amalawi kumavuto omwe akula m’dziko muno.

Mkulu wa bungwe lomwe silaboma lolimbikitsa chilungamo la Justice Link, Justine Dzonzi, kudzanso mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, anena izi m’sabatayi.

Awiriwa ati ngati boma silokonzeka kukambirana zoombola Amalawi ku mavuto omwe ayala mphasa m’dziko muno ndibwino mtsogoleri wadziko lino, Bingu wa Mutharika, akapume mopanda kukankhana.

Koma mneneri wa boma, Patricia Kaliati wati uwu ndi mtopola komanso mabodza chifukwa aboma sadaitanidwe kuzokambiranazo.

Iye wati sakukhulupiriranso kuti msonkhanowo udatsekulidwa kwa aliyense chifukwa bungweri lidathamangitsa atolankhani ena kumsonkhanoko.

“Ngati amathamangitsa atolankhani ndiye ife achikhala tidapita sibwezi atatithamangitsa? Ngati amatitukwana oti sitidapiteko ndiye zikadatha bwanji achikhala tidali komweko?

“Chifukwa chiyani amaloza dzala ena kuti achokera kuboma chikhalirecho amati aitana aboma? Zamtopola ndi mabodza ife sitifuna,” adatero Kaliati.

PAC idachititsa msonkhanowo ku holo ya mpingo wa Katolika ku Limbe Cathedral mu mzinda wa Blantyre kuyambira Lachitatu mpaka Lachinayi sabata yatha komwe idaitana amipingo, aboma, mafumu, atolankhani, azipani, akatswiri azamalamulo, komanso oona zamaufulu a anthu.

Mbali zonse, kupatula mafumu ndi aboma zinafika.

Koma wapampando wa bungwe la PAC, Robert Phiri wati bungwe lawo lidatumizira kalata mafumu atatu kuti adzakhale nawo pa zokambiranazo koma mfumu imodzi yokha ndiyo idabwera.

Iye wati adadabwitsidwa ndi mfumu idabwerayo kuti idangokhala kanthawi kochepa ndipo idabwerera mosadadziwa chifukwa chake.

Phiri wati aboma adawatumiziranso kalata kuti adzakhale nawo pazokambiranazo koma palibe nkhope ndi imodzi yomwe idabwera.

“Kupatula mafumu atatuwo tidatsekula msonkhanowo kuti yemwe akufuna atha kubwera,” adatero Phiri.

Pomaliza msonkhanowo, zina mwa mbali zoitanidwazi zidamanga mfundo kuti Mutharika atule pansi udindo wake m’masiku 60 kapena aitanitse riferendamu m’masiku 90.

Apa Dzonzi, Banda ndi ena ati agwirizana kwathunthu ndi ganizoli ati chifukwa ngati Mutharika sangatule pansi udindo, chonsecho mbali ya boma osamapezekanso kuzokambirana, mavuto omwe akufinya anthu m’dziko muno sangathe.

Banda wati kusapezeka kwa boma kukusonyezeratu kuti lidadzipeza lokha lolakwa pazomwe zimakambidwa kumsonkhanowo.

Dzonzi, yemwenso ndi katswiri wa zamalamulo, wati dongosolo la malamulo a dziko lino limalongosola nthawi yoyenera yomwe pangachitikire riferendamu komanso kumupempha mtsogoleri kuti atule pansi udindo.

Iye wati riferendamu ingatheke ngati dziko likufuna kusintha malamulo ena kapena kuona ngati pulezidenti akukondedwabe ndi anthu.

Iye wati n’kothekanso kukhala ndi kukhalanso ndi zomwe maiko ena amatcha ‘masankho apakatikati.’

Apa iye wati sikulakwira malamulo kumupempha pulezidenti kuti atule pansi udindo chifukwa naye amakhala ndi liwu pa ganizolo.

Iye wati Pulezidenti atha kuchoka potula pansi udindo mwa iye yekha kapena ngati achotsedwa potsatira malamulo oikika.

Mwa zina iye adati malamulo amapereka mpati wokakamiza Pulezidenti kusintha zingapo.

Iye adatinso kuchita zionetsero zokakamiza kuti Pulezidenti atule pansi udindo n’kololedwa m’malamulo adziko lino.

Victor Sangula wa m’mudzi mwa Kasitoma kwa T/A Liwonde m’boma la Machinga wati boma silifuna kuvomereza kuti mavuto omwe adza m’dziko muno abwera kaamba kosafuna kukambirana.

Iye wati n’kutheka boma limaganiza kuti msonkhanowo ungalephereke ngati ilo silipezeka.

Sangula wati Mutharika atule pansi udindo chifukwa ngati satero mavuto m’dziko muno apitirirabe.

Assam Banda wa m’mudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere m’boma la Chiradzulu wati kusapezeka kwa mbalizi kungaunikireponso za udani omwe ulipo pakati paboma ndi amabungwe.

Iye wati mavuto a zachuma ndi ndale omwe ali m’dziko muno ndiwo angakakamize Mutharika kuti akapume.

Mfumu ina yaikulu ya m’boma la Zomba—yomwe yapempha tisaitchule dzina kuti imasuke polankhula—yati ngati m’nyumba muli kusamvana pamafunika kukambirana, osati kuchotsa bambo wa m’nyumbamo.

Iyo yati boma lidaphonya mwayi posapezeka kuzokambiranako komwe ati kukadapezeka mayankho a mavuto omwe achuluka m’dziko muno.

“Boma lidalakwa; apa zikutanthauza kuti mavuto omwe ali m’dziko muno sangathe chifukwa boma likukana zokambirana,” idatero mfumuyi.

T/A Nthache ya m’boma la Mwanza yati bungwe la PAC lidawalambalala kuzokambiranazo kotero apempha bungweli lichititse msonkhano wina omwe udzaitanitse Mutharika ndi Mafumuwa.

Mfumuyi yati atsogoleri a midzi akaitanidwa kuzokambirana, eni msonkhanowo amayenera akonze mayendedwe ndipo a PAC sachite izi.

Iyo yati mafumu amakhulupirira kukambirana ndipo adali chile kukakhala nawo pazokambiranazo.

Nthache wati sakupeza chifukwa choti Mutharika atulire pansi udindo chifukwa zimenezi zingayambitse ziwawa zomwe zingathere m’nkhondo.

“Nkhondo ya ku Mozambique idayambika motere pomwe padalibe kumvana kwa ena ndi boma; adzavutike ndi anthu a kumudzi,” akutero Nthache.

Iye wati PAC ichititse msonkhano wina womwe udzameme mafumu ndi Mutharika.

Related Articles

Back to top button