National News

CDF ikuthera kugulira kwale ku Neno

Listen to this article

Thumba la chitukuko cha boma la Constituency Development Fund (CDF) m’dera la kummwera kwa boma la Neno likuthera kugulira miyala ya kwale mumapulojekiti a bungwe la Build On zomwe n’zosemphana ndi ndondomeko zoyendetsera thumbali.

Anthu m’derali akuti phungu wawo Mary Khembo amagwiritsa ntchito ndalama za CDF pa lonjezo lake lopereka kwale omangira zipinda zophunzirira zomwe bungweli lingafune pa ntchito yake.

Izi zidadziwika pamsonkhano wa makomiti a chitukuko a kwa T/A Chekucheku, Symon, Mlauli ndi Dambe pa Neno Boma masiku apitawa. Bungwe la Association of Progressive Women (APW) lidachititsa msonkhanowo kuti anthu akambirane zitukuko za CDF komanso dongosolo la matumba ena monga Local Development Fund (LDF) ndi District Development Fund (DDF).

Mwa zina, bungwe la Build On limafuna anthu okhudzidwa ndi chitukuko apereke zipangizo zomwe zimapezeka mosavuta m’dera lawo monga mchenga, njerwa, madzi ndi miyala pantchito iliyonse ingayambe.

Khansala wa dera la Ligowe Amos Chizenga adati amadabwa kuti malipoti amapulojekiti a bungweli amaonetsa kuti CDF idagula kwale pomwe phunguyu adalonjeza kupereka miyalayo ndi ndalama za m’thumba mwake.

“Tikafunsa ndalama kuti igwire ntchito pa chitukuko tasankha, Khembo amati ndalama zinathera kugula ndi kututa kwale omangira zipinda pasukulu ya Mwalaoyera ndi Mphamba zomwe adamanga a Build On. Malipoti akhonsoloyo akuwonetsanso motero,” adatero Chizenga.

Ngakhale CDF ndi thumba la phungu, makhansala ndi woyimilira komiti ya chitukuko ku dera, Area Development Committee (ADC), amasayinira fomu yotengera ndalama ya zitukuko kukhonsolo.

Koma khansala wa Lisungwi, Patrick Mwale, adati izi sizichitika ndipo zitukuko zina zomwe dera lake likulandira ndi zosafunika.

Mwale adati phunguyo adamusayinitsa fomu imodzi yosalemba kanthu pakale ndipo akumapanga fotokope sayini ya mankhansalawo ndi kumatenga ndalama.

“Palibe chitukuko cha CDF ndingaloze kuno. Ndi kungomvetsedwa kuti thumbali akugulira kwale pa lonjezo lake,” adatero Mwale.

Wapampando wa komiti ya chitukuko kwa T/A Mlauli Jonas Goliati adati safunsidwa chitukuko choyenera kudera zomwe zikuchititsa phunguyu kupanga zosiyana ndi zofuna za anthu.

“Vuto ndalama zikusakazika ndiye akungochita zitukuko zosalimba. Timafuna simenti pamlatho wa Chifunga, koma anadzangokhoma matabwa. Titafunsa adati ndalama zilipo sizingagule simenti,” adatero Goliati.

Atanfunsidwa za nkhaniyi, phungu Mary Khembo adali odabwa, ndipo adati  anthuwo ndi amene adapereka zitukuko zomwe akuchitazo.

“Izi ndi za bodza. Anthuwo ndi amene amapeza mitengo ya zipangizo zomangira ndipo zitukuko ndi kuchita adalemba okha,” adatero Khembo.

Pa nkhani ya kwale, iye adati izi zikuchitika popewa kusemphana ndi chitukuko chifukwa nthawi zambiri bungwelo likafuna kumanga anthu amakhala asanatute miyala.

“Build On imafuna anthu apereke miyala, njerwa ndi mchenga mwa zina. Nthawi zambiri zinthuzi zimapezeka kutali ndiye ine ndimatero pothandiza kuti ntchito yomanga isachedwe,” adatero Khembo.

Poyankhapo, bwanankubwa wa boma la Neno Ali Phiri adati dongosolo la mafomu a CDF lili chomwechi chifukwa phungu ndi makhansalawo adasayiniriranatu. 

Related Articles

Back to top button