Nkhani

‘Chaponda abapondaponda’

Listen to this article

Mpungwepungwe omwe udayamba n’kukayikirana pa kagulidwe ka chimanga ku Zambia, wafika pamponda chimera ndi kuchotsedwa kwa George Chaponda ngati nduna ya zamalimidwe.

Mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika adachotsa Chaponda Lachitatu patangotha tsiku limodzi bungwe la apolisi ndi bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau atapeza K200 miliyoni ku nyumba ya ndunayo ku Area 10 ku Lilongwe. Ndalamazo zidali K124 miliyoni, US$57 200 (K42 miliyoni) ndi ndalama zina za ku South Africa ndi Botswana.

Adachotsedwa: Chaponda

Sabata yatha, ACB idati ngakhale komiti imene Mutharika adakhazikitsa kuti ifufuze Chaponda, komanso komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo adati ACB ndi apolisi afufuze Chaponda, iwo adali atayamba kale kufufza nkhaniyo mu January.

Izi zidadza pamene komiti yapadera ya ku Nyumba ya Malamulo ndinso imene adakhazikitsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika zitalangiza apolisi ndi ACB kuti afufuze bwino Chaponda pakukhudzidwa kwake pa nkhani yoti boma, kupyolera mu bungwe la Admarc, litagula chimanga ‘mwachinyengo’ kuchokera ku Zambia.

Chikalata chochokera kunyumba ya boma chidasonyeza kuti Mutharika adachotsa Chaponda, ndipo ntchito zake azigwira ndi Mutharika.

“Pogwiritsa ntchito mphamvu zomwe malamulo amamupatsa, mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika wachotsa George Chaponda yemwe adali nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi paudindowu,” chidatero chikalatacho.

Ganizo lochotsa Chaponda labwera patapita nthawi mabungwe ndi anthu osiyanasiyana kuphatikizapo zipani zotsutsa boma zikukakamiza boma kuti lichotse mkuluyu kutamveka kuti amakhudzidwa ndi zachinyengo zomwe zikuganiziridwa kuti zidachitika pa kagulidwe kachimanga.

Poyamba, mabungwe ena adakatenga chiletso kukhothi choletsa Chaponda kupita ku ofesi kwake kapena kugwira ntchito ngati nduna, pomwe Chaponda adachotsedwa pampando wake wa mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo.

Zingapo zochititsa chidwi zachitika pankhaniyi, pomwe ngakhale bwalo la milandu lidalamula kuti Chaponda asagwire ntchito ngati nduna, iye adapita m’dziko la Germany. Komanso, pamene kafukufuku wa makomiti awiriwo adatuluka, ofesi ya Chaponda ku Lilongwe idaotchedwa ku Lilongwe Lachitatu sabata yatha.

Popitiriza kafukufuku wake, nthambi ACB ndi apolisi adapitanso kuofesi ya Admarc ndi Transglobe. Transglobe ikukhudzidwa ndi nkhaniyo chifukwa idapatsidwa mphamvu zogula chimanga ku Zambia, zimene makomiti adadzutsa nazo nsidze kuti mwina padayenda chinyengo.

Katswiri wa zamalamulo Justine Dzonzi adauza wailesi ya Zodiak kuti malamulo a zakayendetsedwe ka ndalama mdziko muno salola munthu kusunga ndalama zakunja popanda chilolezo cha mkulu wa banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi.

Iye adanena izi poyankha ngati Chaponda adaswa malamulo posunga ndalama (za Malawi ndi zakunja) m’nyumba mwake.

Chaponda ndi phungu wa ku Nyumba ya Malamulo wa kummwera cha kumadzulo m’boma la Mulanje ndipo wayendetsapo maunduna angapo. n

  • Nkhani idaphulika ndi otsutsa ku Zambia
  • Mkulu wa Admarc adakana kukhudzidwa pankhaniyo
  • Naye Chaponda adati ayi
  • Mutharika adakhazikitsa komiti yofufuza
  • Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa komiti yapadera
  • Makomiti onse adati Chaponda, Admarc ndi ena afufuzidwe pankhaniyi

Related Articles

Back to top button
Translate »