Chichewa

Chilala chavuta maboma ambiri

Nduna ya zamalimidwe ndi chitukuko cha madzi, Dr Allan Chiyembekeza, wati pakhala msonkhano wounikira momwe ng’amba yakhudzira anthu makamaka m’chigawo cha kummwera.

Chiyembekeza adanena izi m’sabatayi atayendera madera omwe ng’amba yavuta m’maboma ena a dziko lino.

Ulendo wa Chiyembekeza udali wachisoni chifukwa maboma ena alimi sadabzale, ena chimanga chafota pamene madera ena sichidamere.

Gojo: Chimanga chikamasula popanda mvula sichingabereke
Gojo: Chimanga chikamasula popanda mvula sichingabereke

Malinga ndi malipoti a m’maboma amene aperekedwa ku unduna wa zamalimidwe, m’maboma a Phalombe, Chiradzulu, Nsanje, Chikwawa, Neno ndi Mwanza ndi komwe kwavuta kwambiri chifukwa cha kusowa kwa mvula.

Mwachitsanzo, boma la Phalombe lalandira mvula masiku 8 okha. Malinga ndi lipotilo, pofika Lolemba pa 25 January nkuti mvula yozama ndi mamilimita 130.6 okha itagwa. Nthawi ngati yomweyo chaka chatha n’kuti bomalo litalandira mvula kwa masiku 27 ndipo idali itazama ndi mamilimita 663.

Mkulu wa zamalimidwe m’bomalo, Osmund Chapotoka, wati chifukwa cha kuchepa kwa mvula, alimi amene adabzala koyambirira, chimanga chawo chafota pamene amene adabzala kumapeto, chimanga chawo sichidamere.

“Ngakhale mvula itagwa lero chimanga chimenechi sichingapulumuke. Apa ndiye kuti alimi ayambiranso kubzala,” adatero Chapotoka. “Tili ndi madera amene kumavuta mvula chaka chilichonse monga ku Kasongo, koma pano ndi madera omwe kumagwa bwino mvulawo kuli gwaaa! Alimi onse akulira.”

Nako ku Thyolo, ndiye angolandira mvula kwa masiku 14 yochuluka ndi mamilimita 199.9 basi. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha nkuti bomali litalandira kale mvula kwa masiku 22 yomwe idali yozama ndi mamilimita 558.2.

Kumenekonso, malinga ndi mkulu wa zamalimidwe, Raphael Mkisi, zinthu zasokonekera.

Chiyembekeza: Tikumana
Chiyembekeza: Tikumana

“Mvula idasiya chimanga chitangoyamba kupota. Yadula kwa sabata ziwiri ndiye ngakhale yayambiranso pano, sichingabereke ndipo alimi akuyenera abzalenso,” adatero Mkisi.

Ku Mulanje mvula yangogwa masiku 15 yozama mamilimita 284.8. Nthawi yonga yomweyi chaka chatha nkuti atalandira mvula kwa masiku 32 yozama ndi mamilimita 934.9.

Ku Neno ndiye angolandira mvula ya mamilimita 150.5 yomwe yagwa kwa masiku 8. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha, bomali lidali litalandira mvula ya mamilimita 806.5 kwa masiku 24.

Chiyembekeza akuti maboma a Balaka, Nsanje, Chikwawa, Ntcheu, Machinga, Chiradzulu ndi ena ali m’mavuto onga omwewa ndipo zikuchititsa mantha.

“Ili si vuto la munthu, Namalenga ndiye akudziwa zonse ndipo sitikudziwa kuti watikonzera zotani chifukwa palibe boma lomwe lili ndi nkhani yabwino,” adatero Chiyembekeza.

Kuchigawo cha kumpoto lipoti lofotokoza momwe zinthu zilili silidaperekedwe kuboma koma ndunayi yati posakhalitsapa lipotilo lituluka pamene iyo ipitenso kukayendera m’maboma ena.

“Tilibe komwe tikulandira mvula mokhazikika, chaka chino tikuyenera kusamala kwambiri chifukwa tilibe chiyembekezo kuti tipeza chakudya chokwanira malinga ndi momwe mvulayi ikugwera,” adatero Chiyembekeza.

Komabe ndunayi yati kupatula kuti boma likhala pansi kukambirana za chomwe achite, alimi akuyenera ayambe kubzala mbewu zina zosalira mvula yambiri.

“Ngati mvula itabwera, tisalimbanenso ndi kuthira feteleza chimanga chomwe sitikololapo. Ndi bwino timusunge fetelezayo kuti tikagwiritsire ntchito paulimi wamthirira.

“Alimi akonzeke kubzala mbewu zina monga chinangwa, mapira, mchewere, mbatata ndi mbewu zina zosafuna madzi ambiri ngati mvula yagwa kudera kwawo,” adatero Chiyembekeza.

Iye adati si dziko lokha la Malawi lomwe lakumana ndi chilalachi komanso maiko monga a South Africa, Lesotho kudzanso Zambia nawo ali pamoto monga zilili kuno. Chiyembekeza adati boma liyesa kupeza njira zoti lithandizire anthu.

Si vuto la mvula lokha, maboma a Phalombe ndi Mulanje ntchemberezandonda nazo zikuteketa mmera womwe wangomera.

Undunawu ukuyembekezera kutulutsa lipoti lomwe lifotokoze momwe zinthu zilili m’dziko muno ukamaliza kuyendera maboma onse.

Pamenepo ndipo padziwikenso momwe chaka chino anthu akololere ngakhale Chiyembekeza wataya chiyembekezo chokolola dzambiri.

Anthu oposa 3 miliyoni m’dziko muno ndiwo akutuwa ndi njala ndipo boma layamba kale kugawa chakudya m’maboma ena.

Koma monga akulirira Nyakwawa Gojo ya m’boma la Mulanje, chaka chino kulira kulipo chifukwa anthu alibe chakudya pamenenso chiyembekezo chokolola chachoka.

“Onani m’munda mwanga muno, chimanga chonse chamasula pamene mvula kulibe. Ngakhale itabwera lero palibe chomwe chingachitike. Mulungu amve kulira kwathu,” adalira Gojo.

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.