Chichewa

Chilengedwe chibwerere ku Mwanza

 

Mapiri, nkhalango komanso madambo ali mbulanda. Anthu adagwetsa mitengo ndi kuotcha makala. Koma lero nkhani yasintha.

Pang’onopang’ono boma la Mwanza layamba kuvala, kubisa kusambuka kwake komwe kudadza pootcha makala.

Pulogalamu yolimbana ndi kusintha kwa nyengo yomwe ikutchedwa Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) ndiyo ikusintha maonekedwe a bomalo komanso maboma ena.

Bungwe la Centre for Environmental Policy and Advocacy (Cepa) ndi lomwe labweretsa kusinthako.

Pulogalamuyi imalimbikitsa anthu kuti atsatire njira zosiyanasiyana zomwe zingawatukule uko akusamala nkhani zachilengedwe.

Alibe nthawi yootcha makala: Kheli ndi mkazi wake kutulutsa mbuzi

Mwa zinthuzi ndi kuchita ulimi wa ziweto, wa kumunda, kugwiritsa ntchito mbaula zamakono, kuchita bizinesi, kutsatira njira zamakono zakalimidwe monga mtayakhasu komanso kulowa magulu obwereketsana ndalama banki m’khonde.

Amene akuyang’anira momwe pulogalamuyi ikuyendera paboma ku bungwe la Cepa, Stephen Chikuse akuti ngati aliyense ali ndi chochita, n’kovuta kuti mitengo isakazidwe.

“Anthu alibe zochita, alibe popezera ndalama. Kungowauza kuti siyani kudula mitengo si zimveka. Ndi bwino kuwapezera chochita monga tikuchitira,” adatero Chikuse.

Izi zasintha mabanja ambiri. Pakhomo pa James Kheli wa m’mudzi mwa Sudala kwa Senior Chief Kanduku tsopano ndi pa mwana alirenji.

Nzeru za Cepa, lero Kheli ali ndi mbuzi 10, wayamba kukolola matumba 50 a chimanga kuchoka pa 15. Kheli ndi banja lake wabzala mitengo 300; akupanga ulimi wa mleranthaka komanso ali ndi munda wa chinangwa momwe akupha ndalama.

“Ndikulipirira mwana wa folomu 3 ndipo pa telemu ndi K20 000. Ndamanga nyumba ya malata, ndagula wailesi komanso mpando wa pamwamba,” adatero Kheli.

Nthawi yopanga makala monga ankachitira kale alibe, ndipo nthawi zonse amakhala kumunda, kubusa komanso banja lake limakhala kumsika kugulitsa mandasi momwenso akupha ndalama.

Monga akufotokozera mkazi wake Sineliya, kale amadalira makala koma lero nkhani idasintha. “Kale, timapeza ndalama pootcha makala. Lero tili ndi njira zambiri zopezera ndalama,” adatero iye.

Pulogalamu ya ECRP idakhazikitsidwa ndi Christian Aid komanso Concern Universal (Discover) koma thandizo la ndalama limachoka ku UK, Irish ndi boma la Norway. K21 biliyoni ndiyo idaikidwa.

Nkhani ya Kheli ndi chitsanzo chabe cha zomwe zikuchitikanso m’maboma a  Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga, Balaka, Salima, Dedza, Kasungu ndi Karonga komwe CEPA ikugwiramo ntchito.

Iwo amayembekeza kufikira alimi 600 000 m’maboma onsewa koma afikira 1 600 000. n

Related Articles

Back to top button