Nkhani

Chipako pa nkhani ya simenti, malate

Listen to this article

Ngati mudakhulupirira lonjezo la chipani cha DPP nthawi ya kampeni chisanachitike chisankho cha pa 20 May 2014 kuti chikadzalowanso m’boma chidzatsitsa mitengo ya malata ndi simenti, iwalani—pano nyimbo ndi ina, Tamvani watsimikiza.

Mmalo motsitsa malata ndi simenti monga ambiri amayembekezera, boma lati lakonza zomangira nyumba anthu ovutika ndipo ikatha, mwini nyumbayo azidzapereka theka la ndalama zomwe nyumbayo yadya.

Kayelekera_villageMneneri wa unduna wa za malo, Ayam Maeresa, adaulula izi Lachinayi poyankha mafunso a Tamvani itafuna kudziwa za nthawi yomwe anthu ayambire kugula katunduyu motsika mtengo patangotha sabata ziwiri Nyumba ya Malamulo itavomereza K7 biliyoni yothandizira ndondomekoyi.

“Tikudikira mvulayi ingotha. Ofuna kukhala pachilinganizochi ayenera kukhala nawo m’magulu amene akhazikitsidwe m’madera awo,” adatero Maeresa.

Iye adati pamodzi ndi makhansala undunawo ukha-zikitsa ndi kuphunzitsa magulu oima paokha amene azitchedwa kuti Housing Development Groups. Maguluwa azikhala mwa gulupu aliyense.

“Maguluwa ndiwo ayendetse ndondomekoyi ndiponso ndiwo azipeza amene akuyenera kupi-ndula ndi ndondomekoyi. Maguluwo akonzedwa chifukwa munthu aliyense ali ndi makondamakonda a nyumba yomwe akufuna, ndiye ife tizingomanga ndipo tikamaliza mwini nyumbayo azidzalipira theka la ndalama zomwe zagwiritsidwa ntchitozo,” adatero Maeresa.

Kusintha kwa ndondomekoyi kukusemphana ndi zomwe anthu akhala akuyembekezera.

Mwachitsanzo, Edison Diverson wa m’mudzi mwa Ntaja kwa T/A Dambe m’boma la Neno ndipo ali ndi zaka 67, akuti amayembekezera zogula malata ndi simenti zotsika mtengo. Iye wati kusinthaku kwamudabwitsa.

Iye ndi mlimi ndipo adagwira ntchito kumigodi m’dziko la South Africa m’ma 1970. Chibwerereni ku Theba, Diverson sagwira ntchito, mmalo mwake ali pakalapakala kuyendera kuboma kuti amulipire ndalama za ku Thebako.

Khumbo la Diverson mwa zina ndi lakuti ngati angamulipire ndalama zake amange nyumba kumudziko chifukwa akugona m’nyumba yofolera ndi udzu ndipo imathonya mvula ikamagwa.

“Ndilibe ndalama, sindingakwanitse kugula simenti kapena malata, n’zodula kwambiri koma nditamva za ndondomekoyi, ndidali ndi chimwemwe kuti mwayi womanga nyumba uja wapezeka,” adatero bambo wa ana asanu ndi awiriyo.

Koma Maeresa akuti kusinthaku kwadza chifukwa cha kukhazikitsidwa kwa pologalamu yomanga nyumba zabwino yomwe akuitcha kuti Decent and Affordable Housing Subsidy Programme (DAHSP) yomwe idakhazikitsidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ku Msampha 1 kwa T/A Chadza ku Lilongwe mu December chaka chatha.

Iye adati kukhazikitsidwa kwa pologalamuyi kukutanthauza kuti boma liyamba kumangira nyumba anthu ovutikitsitsa m’madera 193 a aphungu onse m’dziko muno.

Mneneriyu akuti munthu amene akumangiridwa nyumba azipemphedwa kupeza njerwa, mchenga ndi madzi ndipo ikamangidwa boma lidzawerengetsa ndalama zomwe zalowapo ndipo mwini nyumbayo adzalipira theka la ndalama zomwe zagwiritsidwa ntchito.

“Mwini nyumbayi adzakhala akulipira ndalamazo kwa zaka 5. Pali chiyembekezo kuti nyumba pakati pa 80 ndi 100 ndizo zimangidwe m’dera lililonse la phungu,” adatero Maeresa.

Nthawi ya kampeni chipani cha DPP chidalonjeza zodzatsitsa mtengo wa simenti ndi malata potsutsana ndi njira yomwe chipani cha PP chimachita pomangira nyumba anthu osauka m’midzi.

Nthawi ya kampeni, Peter Mutharika, yemwe pano ndi Pulezidenti wa dziko lino, adati ndi bwino kuti mitengo ya simenti ndi malata itsitsidwe kuti aliyense akhale ndi mwayi womanga yekha nyumba yomwe akufuna.

Related Articles

Back to top button