Chipalamba ku Malawi

Dziko la Malawi likusanduka chipalamba. Kafukufuku wathu wapeza kuti mafumu ndi apolisi ena ndiwo akuthandizira kusambula dzikoli pamene akuthandizira kudula mitengo mosasamala ndi kuotcha makala.

Lidali dziko la nkhalango zowirira. Koma lero, madera ambiri ali mbee! Ukaona mitengo, ndiye kuti ndi pamanda.

Makala kudikira kuti awatengere kumalonda

Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, dziko lino lili pamwamba pa maiko a mu Sadc posakaza mitengo ndipo padziko lonse lapansi, lili pa nambala 4.

Mtolankhani wathu sabata yatha adalowa geni ya makala m’boma la Ntcheu. Uku ndi kumalire a Neno ndi Mwanza.

Iye adapeza anthu ochuluka akuchita bizinesi yootcha ndi kugula makala. Mitengo yambiri yatsala kuderali ndipo amene amapanga makala m’maboma a Mwanza ndi Neno asamukira kumeneko.

Mtunda woposa makilomita 90 umene udali ndi mitengo yambiri yachilengedwe lero ndi mpala. Mitengo yatha ndipo mitengoyi ikugwetsedwa m’malire a Malawi ndi Mozambique.

Mtolankhaniyu atafika, adauzidwa kuti akakumane ndi nyakwawa Kabwayibwayi ya m’boma la Ntcheu yomwe imupatse malo woti agwetse mitengo. Mfumuyo idatsimikiza kuti mitengo ilipo ndipo kuti mtolankhaniyu aotche makala, akuti amayenera kulipira ‘cha nkhalango’.

“Cha nkhalango ndi K2 000,” idatero mfumuyo.

Mtolankhani adauza mfumuyi kuti akufuna apange uvuni zisanu zotalika mamita 20. “Koditu kuli golide [mitengo], ndi zotheka,” idatero mfumuyo.

“Mita imodzi ndi K2 000, ngati mulibe ndalama ndiye mukaphula makalawo mudzapereka matumba atatu [olemera makilogalamu 50 lililonse],” adaonjeza.

Poona kuti zitenga masiku ambiri, mtolankhaniyu adaganiza zogula makala kwa ogulitsa ena kumeneko. Thumba lililonse limagulidwa K2 000.

Kuti thumba lifike ku Blantyre kokagulitsira, umayenera ulipe K2 500 kwa mwini galimoto. Kupatula izi, adatinso ndipereke K300 pa thumba lililonse yomwe imakhala ya apolisi.

“Masiku ambiri timakumana ndi apolisi amene amatilipiritsa. Ndiye timakonzeratu kunoko kuti tisavutike mayendedwe,” amene amathandiza mtolankhaniyo kupanga makalawa, Happy adatero.

Mtolankhaniyo atafunsa Happy kuti pa ‘roadblock’ ya polisi ya Zalewa akalipira chiyani, iye adayankha kuti malowo ngosavuta. Harry adaoda matumba 70.

“Mungomupatsa dalaivala K2 500 ndi K300, ndalamayi imathandiza zonsezi ndipo matumba anu akakupezani ku Blantyre,” adatero.

Anthu onse amene adali ndi makala adapereka ndalama zawo kwa woyang’anira kampuyo pamene iwo adanyamuka ulendo ku Blantyre.

Lachisanu onse amene adakwezetsa makala awo adachoka kumaloko. “Sitiyenda limodzi ndi galimotoyi, adzangotiuza kuti makala afika, tiyeni tibakadikirira ku Blantyre,” adatero Happy.

Sipadatenge nthawi, Loweruka m’ma 3 koloko mmawa, mtolankhaniyu adalandira foni kuti galimotoyo yomwe idanyamula matumba 250 yafika msika wa Khama ku Machinjiri. Onse amene adakweza makalawo adali pamalopo kugulitsa makalawo.

Patsikulo bizinesi simayenda bwino chifukwa thumba lomwe poyamba limagulidwa K9 000, limapita pa K5 000 mpakanso kumafika pa K3 500.

Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, pafupifupi mahekitala 3.4 miliyoni aonongeka pootcha makala. Mu June chaka chino, komiti yoona zachilengedwe ku Nyumba ya Malamulo idapempha undunawu kuti uletse kuotcha komanso kugulitsa makala m’dziko muno.

Wachiwiri kwa mkulu wa za nkhalango Ted Kamoto akuti dera la Neno, Ntcheu ndi Mwanza ndi lomwe likutulutsa makala ambiri pakadalipano. “Kumeneko mitengo ikugwetsedwa kwambiri pamene akupanga makala,” adatero.

Malinga ndi Kamoto vuto la kuotcha makala lakulanso kwambiri chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi komanso kuchepa kwa chiwerengero cha Amalawi amene amagwiritsa ntchito magetsi pophika.

“Amalawi 85 mwa 100 alionse amagwiritsa ntchito makala ndi nkhuni pophika. Izi zili choncho, 15 mwa 100 ndiwo amagwiritsa ntchito magetsi. Izi zafika pena chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi,” adatero iye.

Koma mneneri wa polisi James Kadadzera akuti anthu akuyenera akanene kupolisi ngati wapolisi wina akufuna ziphuphu kuti adutsitse makala.

“Ngatinso akuti akumapereka ndalama ku 997, atiuze nambala ya galimotoyo. Komanso atiuze wapolisi amene walandirayo,” adatero iye.

Share This Post