Chipatala cha khansa chitheka September

Odwala khansa ayembekezere kupuma umoyo wina. Chipatala chachikulu chothana ndi matendawa chitsegulidwa September chaka chino mumzinda wa Lilongwe.

Nduna ya zaumoyo Atupele Muluzi yatsimikiza za nkhaniyi ndipo yati chifukwa cha ichi, boma lichepetsa kapena kusiyiratu kutumiza odwala ena kunja kukalandira thandizoli.

Peter Mutharika kukhazikitsa ntchito yomanga chipatala cha khansa

“Odwala khansa timawatumiza kunja kukalandira thandizo, kumangidwa kwa chipatalachi kwatonthoza ambiri chifukwa mmalo mopita kunja, azithandizidwa m’dziko momwemuno,” adatero Muluzi.

Malinga ndi nthambi yowona zaumoyo padziko lonse ya World Health Organisation (WHO), matenda a khansa amapulula anthu pafupifupi 9 miliyoni pa chaka.

WHO ikutinso anthu pafupifupi 8 mwa 10 alionse amene akupululuka ndi khansa ndi ochokera m’maiko osauka makamaka mu Africa momwe muli dziko la Malawi.

M’dziko muno, khansa yomwe yafala ndi yokhudza chiberekero, pakhosi komanso m’magazi yomwe anthu akulephera kuphupha.

“Chifukwa chachikulu n’kuchedwa kupita kuchipatala komanso maiko 30 mwa maiko 100 alionse osauka ali ndi zipatala zoyenera zothandiza khansa,” adatero Leslie Mgalula woimilira WHO m’dziko muno.

Lachitatu m’sabatayi, Tamvani itayendera chipatalachi idapeza ntchito yokhoma malata ili mkati, kupereka chiyembekezo kwa Amalawi amene akhala akulira kwa zakazaka.

Mmodzi mwa anthu amene adapulumuka ku khansa, Janet Bonwel wa m’mudzi mwa Ndindi m’boma la Salima, kumangidwa kwa chipatalako ndi chokoma kwa odwala matendawa.

“Ndidapezeka ndi khansa ya pamwendo mu 2001. M’zipatala amangondipatsa panado basi, ululu sumatha,” adatero pamene adati adavutika ndi matendawa kwa zaka 6.

Iye wati boma lionetsetse kuti chipatalachi chithandize aliyense osati kusala osauka.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za anthu ovutika ndi khansa la Cancer Association of Malawi, Regina Njirima, wati khansa imafunika chipatala chakechake ngati momwe zakhaliramu.

“Izi zimachitika chifukwa anthu a vuto la khansa amafunika kuonedwa pafupipafupi,” adatero.

Njirima adati boma likuyenera kuchilimika kufalitsa uthenga momwe anthu angapezere thandizo kuchipatalachi ponena kuti aliyense akuyenera adziwe za thandizo lomwe chipatalachi chidzipereka.

Share This Post