Chichewa

‘Chisangalalo chafika, Samalani kuli mavuto’

Listen to this article

Mawa laliwisiri ndi tsiku la Khirisimasi ndipo Lamulungu sabata ya mawa ndi tsiku lokumbukira kulowa chaka cha 2017. Iyi ndi nthawi imene ena amasangalala ngati kulibe mawa, koma akadaulo anenetsa kuti iyi ndi nthawi yokumbukiranso kuti kuli msilikali wamkulu—mwezi wa January—amene amasiya ambiri m’matumba muli mbeee!

Ena amavulala kapena kufa kumene chifukwa chosangalala mosasamala.

Katswiri pa zachuma, Henry Kachaje, wati matumba amabooka mu January chifukwa cha kusakaza ndalama mosasamala nyengo ya zikondwereroyi.

Iye adati ndondomeko yabwino pakagwiritsidwe ntchito ka ndalama ingathandize kupeputsa ena mwa mavuto omwe amaoneka mu January monga ngongole zosakonzekera.

Anthu adali pakalikiliki kugula katundu m’sabatayi

“Iyi ndi nthawi yomwe timaona anthu akumwa, kudya ngakhalenso kuvala moposa mapezedwe awo. Mchitidwewu ndiwo umabala mavuto mwezi wa January,” adatero Kachaje.

Iye adati kukonzekera kwa nzeru n’kuonetsetsa kuti zinthu zofunikira kwambiri monga chakudya zagulidwa mokwanira nkusungidwa moyenera mapwando asadayambe.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe olimbikitsa maphunziro la Civil Society Coalition for Quality Education, Benedicto Kondowe, adati ana ena alephera kupita ku sukulu chifukwa choti makolo awo adaononga ndalama  za fizi.

Kondowe adati pomwe makolo akukonza zisangalalo zosiyanasiyana, alingalirenso za ndalama za fizi ya ana awo kuti asadzagwire njakata nthawi yotsegulira sukulu ikadzafika.

“Chowawa kwambiri pamoyo wa mwana nkuona anzake akupita kusukulu iye ali pakhomo kaamba kosowa fizi. Kuli bwino kuchepetsa chisangalalo koma nthawi ikafika, ana adzapite kusukulu,” adatero Kondowe.

Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Prince Kapondamgaga adati kusangalala n’kofunika pamoyo wa munthu koma adachenjeza alimi kuti asaiwale kugula zipangizo zaulimi kaamba kokomedwa ndi zisangalalo.

Iye adati mlimi wanzeru amaonetsetsa kuti chilichonse chomwe angafune paulimi wake chilipo asadayambe kulingalira zina chifukwa iyi ndiyo njira yomwe iye angapindule nayo paulimi wake.

“Aliyense amafuna kusangalala m’moyo mwake koma zinthu zimakoma zikamayenda ndi nthawi komanso kuthekera komwe kulipo. Osayamba maphwando ulibe zipangizo zaulimi ngati ndiwe mlimi,” adatero Kapondamgaga.

Mkulu wa bungwe loyang’anira za anthu ogula la Consumers association of Malawi (Cama) John Kapito adati anthu asaiwale za njala yomwe iliko chaka chino.

Iye adati n’zopanda phindu kusangalala masiku ochepa koma kenako n’kudzavutika masiku ambiri ndi njala zomwenso adati zingapangitse chitukuko kulowa pansi.

“Tonse timadziwa kuti munthu amagwira bwino ntchito ndi m’khuto ndiye ndi njala ya chaka chinoyi, n’kofunika kusamala kwambiri pa momwe tingakonzere zisangalalo zathu. Tiyeni tionetsetse kuti tasungako ndalama ndi chakudya m’makomomu,” adatero Kapito.

M’chikalata chake m’nyengoyi, bungwe loonetsetsa kuti malonda akuyenda mokomera aliyense m’dziko muno la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) lati nyengo ngati iyi amalonda ena amafuna kukokera ponyenga ogula.

Bungweli lati nyengoyi, anthu a mabizinesi amagwiritsa ntchito bodza potsatsa malonda awo ndi cholinga choti anthu akopeke ndipo kawirikawiri anthu sazindikira kuti apusitsidwa kaamba kakukomedwa.

“Ambiri amanama kuti atsitsa mitengo. Mwachitsanzo, amatha kunena kuti katundu wafika pa K15 000 kuchoka pa K25, 000 chonsecho katunduyo sanagulitsidweko pa K25, 000,” lidatero bungwelo.

M’sabatayi anthu adali pikitipikiti kugula zinthu monga zakudya ndi zovala kukonzekera zisangalalo za Khirisimasi ndi Nyuwere ndipo ena mwa anthuwa adalandira malangizowa ndi manja awiri. n

Related Articles

Back to top button
Translate »