Editors PickNkhani

Chisankho cha Mulhako chilephereka

Listen to this article
Adanyanyala: Katunga
Adanyanyala: Katunga

Kudali kuthafulirana Chilomwe kusukulu ya pulaimale ya Nyambadwe pulaimale Lolemba masiku apitawa pamene gulu la Mulhako wa Alhomwe ku Ndirande limachititsa chisankho.

Chisankhocho chimachitika patadutsa zaka zitatu chisadachitike ndipo amasankha maudindo a mkulu wa gululi ku Ndirandeko komanso wachiwiri wake, mlembi ndi msungichuma.

Anthu amene adatsina khutu Tamvani ati chidasokoneza zonse ndi mkulu wina amene amafuna apikisane nawo koma adabwera ndi achipani amene amafuna amuvotere.

Patsikuli padali anthu atatu amene amafuna apikisane pampando wa mkulu wa gululi koma chisankho chisadayambe padachitika mpungwepungwe.

“Vuto ndiloti mmodzi mwa amene amapikisana nawo pa mpandowu ndi wachipani cha DPP moti anabwera ndi omutsatira achipaniwo. Izitu si zachipani koma zachikhalidwe cha Alhomwe,” adatero wotitsina khutuyu.

“Amene adawatenga kuchipaniwo si a mtundu wathu zomwe zidakwiyitsa anthu.”

Awiri mwa amene amafuna kupikisana nawo pampando wa wamkulu wa gululi adafumukapo kuti sapikisa nanawonso.

Mmodzi mwa amene adanyanyala kuti sachita nawo chisankhocho ndi Dolesi Katunga amene wakhala mkulu wa gululi kwa zaka zitatu.

Iye watsimikizira Tamvani kuti kudali mpungwepungwewo. “Chisankho chalephereka, sindikudziwanso kuti zitha bwanji chifukwa chichokereni sindinabwererenso,” adatero Katunga.

“Ndidachokapo chifukwa cha mpungwepungwe omwe udabuka, ndidakonzeka kuchita nawo chisankhocho koma chidandikhumudwitsa ndi zokangana zomwe zidabukazo. Sikuti ndikukakamira mpando,” adatero iye.

Related Articles

Back to top button
Translate »