Nkhani

Chisankho chachibwereza chilipo pa 6 June

Listen to this article

Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lakhazikitsa pa 6 June 2017 kuti Amalawi adzaponye voti yachibwereza kummwera cha kummawa kwa Lilongwe patangotha mwezi bwalo lamilandu la apilo litagamula kuti chisankho cha kuderali sichidayende bwino.

Chigamulochi chidaperekedwa potsatira dandaulo la yemwe ankaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Ulemu Msungama kuti chinyengo chidachitika pachisankhocho.

Voters will still use voter ID cards in 2019

Chigamulochi chitaperekedwa, zipani zandale zidapempha MEC kuti ichititse chisankho chachibwereza kuderalo msanga kuti anthu akhale ndi phungu wowaimirira ku Nyumba ya Malamulo chifukwa chigamulocho chidatanthauza kuti deralo lilibe phungu.

Pachisankho cha pa 20 May, 204, MEC idalengeza kuti Bentley Namasasu wa Democratic Progressive Party (DPP) ndiye adapambana koma Msungama adakamang’ala ku bwalo la mirandu za chigamulochi.

Wachiwiri kwa mlembi wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka, mneneri wachipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni ndi mneneri wa United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga adati MEC isapange chidodo pa zopangitsa chisankho chachibwereza.

Mobweretsa chilimbikitso pa nkhawa ya za vuto la ndalama zopangitsira chisankhochi lomwe bungwe la MEC lidanena poyamba, bungweri lati chisankhochi chilipo pa 6 June 2017.

“Potsatila chigamulo cha bwalo la mirandu la apilo, bungwe la MEC lidapangitsa msonkhano pa 4 April omwe lidafotokozera zipani ndi okhudzidwa ena kuti lipangitsa chisankho ku dera la ku mmwera cha ku mmawa kwa Lilongwe pa 6 June 2017,” chidatero chikalata chomwe bungweli lidatulutsa.

Chikalatachi chidatinso pofuna kuti bungweli lisawononge ndalama zambiri, chisankhochi chichitika limodzi ndi zisankho zina monga kumpoto kwa Lilongwe Msozi, chisankho cha khansala wa kumpoto kwa Mayani ku Dedza ndi khansala wa kwa Mtsiliza ku Lilongwe.

Bungwe la MEC lati makandideti akale ndi atsopano ndi olandilidwa kupikisana nawo motsatana ndi malamulo a zisankho.

Pa zisankhozi, bungwe la MEC lati omwe adzaloledwe kuponya voti ndi okhawo omwe adalembetsa m’kaundula wa 2014 ndipo sipadzakhala zosintha malo okaponyera voti.

Zipani za MCP, PP ndi UDF zati nkhaniyi ndi yabwino koma zati mpofunika kuwonetsetsa kuti pasadzachitikenso zachinyengo zomwe zingadzapangitse kuti zotsatira za chisankhochi zidzakanidweso.

Related Articles

Back to top button
Translate »