Nkhani

Chotsani ndale mu ulimi wamthirira—Jalavikuba

Listen to this article

Inkosi Jalavikuba ya m’boma la Mzimba yapempha boma kuika alimi patsogolo ndi kuchotsa ndale muulimi wamthirira.

Mfumuyi idanena izi Loweruka lapitali m’dera la kumpoto m’boma la Mzimba pachionetsero cha ulimi wamthirira pomwenso idawapepesa alimiwa ati chifukwa salabadiridwa.irrigation-farming

Jalavikuba adati chifukwa boma lalowetsapo ndale paulimi wamthirira, ulimiwu sukupita patsogolo. Ndale, iye adati, zikulowa pa momwe kontilakiti zomangira masikimu a mthirira zikuperekedwera.

“Ndale zatisaukitsa, atsogoleri andale, amipingo ndi ife mafumu tiyeni tisiye ndale ndi kuchita chitukuko. Atolankhani mukanene chilungamo, ine si wandale,” adatero Jalavikuba.

Iye adati ndi zomvetsa chisoni kuti ngakhale dziko lino limadalira ulimi pachuma chake, boma silikuikapo mtima kwambiri.

“Alimi paokha akuyesetsa, mbali yatsala ndi ya boma kuti liziwapatsa thandizo loyenera,” iye adatero.

Jalavikuba adakumbutsanso alimiwo kuti ulimi ndi bizinesi ndipo aziikirapo khama.

Koma alimiwo adadandaula kuti ulimi wamthirirawu akuumva kuwawa kaamba ka ngalande  zomwe sizikugwiritsidwa ntchito chimangireni.

Iwo adati yemwe adamanga ngalandezo adamanga mwachinyengo moti zina zidagumuka chifukwa chochepa simenti, pamene zina sizitha kuthirira minda chifukwa zili mmunsi kwambiri.

Mmodzi mwa alimiwo, Austin Chavula, yemwe ndi wapampando wa sikimu ya Ndau, adati boma likufunika liunikenso momwe ntchitoyo adayigwirira.

Povomerezana ndi Chavula, Edward Mvula, wapampando wa sikimu ya Chanolo, adati alimiwa akusowa pogwira ngakhale boma lidaononga ndalama zankhaninkhani pokumbitsa ngalande m’chaka cha 2011.

“Pakadalipano tikupempha boma litiganizire potipatsa simenti yokonzeranso ngalandezi kuti mthirira uyende bwino,” Chavula adatero.

Ndipo wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya Nyumba ya Malamulo pazaulimi, Joseph Chidanti Malunga, adati komiti yake ipereka madandaulowo kuboma ndipo akukhulupirira kuti lichita kafukufuku pankhaniyi.

Malunga, yemwenso ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo m’dera la kummwera cha kumadzulo m’boma la Nsanje, adati n’zodabwitsa kuti dziko lino likuitanitsa chakudya kunja pamene lili ndi kuthekera kodzilimira.

“Ngati boma lingaike mtima powapatsa anthu zipangizo zowayenereza paulimi, sindikuona chifukwa chogulira chimanga kumaiko ena,” Malunga adatero.

Iye adati chofunika ndi kudzikonzekeretsa poika ndondomeko zogwirizana ndi momwe zinthu zikuyendera.

Ndipo Agnes Nyalonje, phungu wa derali yemwe adakonza chionetserocho, adati dera lake lili ndi kuthekera kodyetsa gawo lalikulu la dziko lino.

Dera la kumpoto m’boma la Mzimba, monga madera ambiri m’dziko muno, lidakhudzika ndi ng’amba ndipo anthuwa apulumukira ulimi wamthirira.n

 

Related Articles

Back to top button