Dipo la chithyolakhola limawawa pazovuta

Munthu akakwatira mkazi mongozemba osatsata ndondomeko amati wathyola khola. Nthawi ikafika yoti munthu otere alongosole banja, amalipitsidwa madipo osiyanasiyana kwa makolo ndi malume a mkaziyo ndipo limodzi mwa madipowo limatchedwa chithyolakhola. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi gogo Eveline Posiano a ku Mchinji za dipoli.

Choyamba agogo talongosolani kuti dipo ndi chiyani?

Dipo ndi chidule cha malipiro ndipo monga tidziwa, malipiro amaperekedwa mwaufulu kapena mokakamizidwa kutengera ndi nthawi komanso cholinga cha malipirowo. Kupereka malipiro kapena kuti dipo mokakamizidwa pamakhala kuti pali mlandu pomwe dipo la mtendere sipakhala mlandu.

Chindapusacho chimapitanso kwa amfumu

Chabwino pano tikukamba za dipo la chithyolakhola, limeneli ndi dipo lanji?

Ili ndi limodzi mwa madipo a milandu ndipo mlandu wake umakhala wokhudzana ndi za banja. Chifukwa chodzadzidwa n’chinyamata, nthawi zina anthu amangotengana n’kukwatirana osadziwitsa makolo kapena kutsatira mwambo koma imakwana nthawi yoti zinthu zilongosoledwe ndiye pamenepo ndipo pamavuta.

 

Kuvuta kwake kotani?

Chomwe chimachitika nchoti potengana mudangobana koma pachikhalidwe chathu, pokwatira mkazi, mwamuna amayenera kupeleka dipo lomwe amati chimalo ndipo ili limakhala dipo lomverera poyerekeza kuti mwatsata mwambo komanso mwalemekeza makolo. Tikakhala ngati ife Achewa, imakhala nkhuku yomwe amati ya chinkhoswe kapena ndalama yokwana kugula nkhukuyo. Pakakhala zoonjezera ndiye zimakhala zongogwirizana pakati pa mabanja awiriwo koma sizikhala ngati chithyolakhola.

 

Tsopano timve za chithyolakhola.

Chithyolakhola ndilo dipo lowawa kwambiri chifukwa akuchikazi ampangira chipsera mtima kuti udawaderera poyamba potenga mwana wawo osawadziwitsa. Kachiwiri amafuna kuti ukhale ndi mantha kuti ngati uli wankhanza, mwana wawoyo ukamusamale bwino komanso dipolo silipita kwa makolo ndi amalume okha ayi komanso amfumu chifukwa udaphotchola m’mudzi mwawo, choncho nawo amayenera kupepesedwa. Akawonkhetsa zonse zomwe ukuyenera kulipira pa chithyolakhola pokha, umadziwanso kuti akulangadi.

 

Nanga utaona kuti zanyanya, sungangomusiya mkaziyo?

Poti masiku ano achinyamata alibe mantha ndi umunthu mwina zikhoza kutheka koma taganizirani poti nthawiyi yadza chifukwa chazovuta. Mwina mosakuluwika, mkazi wamwalira mwadzidzidzi ndiye sungakayike kwanu akwawo osavomereza komanso ukapita naye kwawoko amakati Iwo akufuna munthu wamoyo yemwe udaba utathyola khola lawo. Apa, ena ouma mtuma amati sitiyika kaye maliro mpaka mlandu ukambidwe ndipo zonse zoyenera zichitikiretu ndiyetu chithyolakhola chake amanena choti ukhaule chifukwa akudziwa kuti uli pa msampha osapeweka. Pamenepa, ngakhale abale ako amatha kukuthawa mukakumana ndi mtundu wovuta komanso wosamvetsa. Koma pachilungamo chake sikukhala kuvuta kungoti amadziwa kuti mukangoika maliro, mwina uthawa basi iwo apusa.

 

Nanga akakhala kuti mkaziyo sudakamutenge kwawo adadzangokulowera mnyumba yekha?

Mpomwe pamafunika kudziwa ndi kutsata mwambo pamenepo. Iweyo ngati mwamuna ndipo ukudziwa mwambo wakwanu, ukuyenera kulingalira zotsatira za kukhalira limodzi kwanuko ndipo choyenera kuchita n’kuuza akwanu kuti adzamuthamangitse ngati walephera kutero wekha. Apo ayi umakauza akwanu kuti atsatire kwawo kwa mkaziyo kukafotokoza chomwe chachitika ndipo akuluakuluwo amagwirizana chochita. Apa umakhala kuti watsata mwambo chifukwa walemekeza makolo a mkaziyo pokawagwadira. Apa sipakhala za chithyolakhola ayi.

Nanga mkazi oti adzakutulira chifukwa wamuchimwitsa zimakhala bwa?

Kukutulira mkazi kuli ndi chisinsi chimodzi: osakana ngati ukudziwa kuti mkaziyo udamuchimwitsadi ndiwe chifukwa chomwe amafuna makolo n’kuchoka manyazi kotero amangofuna kuti zinthu zilongosoke mimbayo isadaonekere patali. Apa mumangokambirana za dipo la chimalo kapena miyambo ina koma sipakhala dipo la chithyolakhola kenako mumapanga chinkhoswe n’kutengana zinazo n’kumakazionera kubanja komweko.

 

Lamulo latsopano lokhudza za mabanja limati mwamuna ndi mkazi akangokhalira limodzi kokwana miyezi isanu, basi banja lakwana. Kodi apa munthu sungatetezedwe ku chithyolakhola?

Choti mudziwe nchoti chikhalidwe chidakhalako kuyambira kalekale malamulo asadabwere ndipo kupatula kuti ngati nzika za dziko timayenera kutsatira malamulo, malamulo nawo sadabwere kudzaononga chikhalidwe. Zomwe mukunena inu n’zamukhothi koma zachikhalidwe zimathera pabwalo la anfumu kapena m’kanyumba komata. Mmenemo mulibe malamulo mukune nawo ndiye siyani kuganiza mobwerera mmbuyo kuti poti mudapita kusukulu ndiye zachikhalidwe mulibe nazo ntchito. Makolo anu tidakulira momwemu ndipo inu mwabadwira momwemu tsono tiyeni tilemekeze chikhalidwe.

Share This Post