Nkhani

DPP ikhumudwitsa ku KK

Mafumu ena ku Nkhotakota ndi okwiya ndi chipani cha DPP chimene akuchidzudzula pogwiritsa ntchito galimoto ya chipatala pa ntchito zachipani.

Lachisanu pa 15, chipanicho chidatenga galimoto ya chipatala cha Nkhotakota kukasiya otsatira chipani ku Lilongwe komwe amakatsanzikana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa ulendo wake wopita ku msonkhano wa United Nations General Assembly (Unga) m’dziko la United States of America.

Galimoto limene lidanyamula a chipani kupita ku Lilongwelo

Izitu zimachitika pamene anthu pachipatalapo amasowekera thandizo la mayendedwe malinga ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Nkhotakoka, Peter Mazizi.

T/A wina amene adapempha kuti tisamutchule, adati mafumu ena akhala akupempha kuti mchitidwewu uthe komabe izi sizikuphula kanthu.

“Si koyamba kuti a DPP agwiritsire ntchito galimoto ya pachipatalapa. Timalankhula koma palibe yankho,” idatero mfumuyi. “Anthu amene akufuna thandizo la galimotoyo amadikira kaye kuti ithandize achipani.”

Koma mlembi wa chipanicho, Greselder Jeffery wati izi ndi ndale chabe ndipo si zoona kuti adagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala.

“Mmmh! abale, komatu ndalezi ndiye zafika penapake,” adatero potsutsa nkhaniyi. “Si zoona kuti tidagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala. Kodi anthu asamavale makaka a chipani chathu akakwera galimoto ya boma?

“Mwina anthuwo amapita ku maliro, chifukwa masiku ano anthu akumavala makaka achipani chathu ngakhale pa ukwati,” adatero Jeffery yemwenso ndi phungu kumpoto kwa boma la Nkhotakota.

Titafunsa mneneri wa chipatala cha Nkhotakota ngatidi zidali zoona kuti galimoto yawo idanyamula anthu a chipani, mneneriyu, Samson Mfuyeni adavomera koma adati galimotoyo si ya boma.

“Ogwira ntchito pachipatalachi ndiwo adagula galimotoyo.” Adaonjeza: “Ndi galimoto ya chipatala osati boma. Timaigwiritsira ntchito zinthu zambiri. Ndi zoona achipani cha DPP adabwereka poperekeza apulezidenti,” adatero.

Malinga ndi Mfuyeni, palibe cholakwika kubwereketsa galimotoyo chifukwa si ya boma.

Koma kafukufuku wathu wapeza kuti galimotoyo, MG 697AJ ndi ya unduna wa zaumoyo ndipo ikugwira ntchito pachipatala cha Nkhotakota.

Malinga ndi mkulu wina ku Plant and Vehicle Hire Organisation—nthambi yomwe ili pansi pa unduna wa zamayendedwe, galimotoyi yomwe ndi lole, ili m’manja mwa boma ku unduna wa zaumoyo.

Khalidwe la DPP lakwiyitsa phungu Mazizi wa deralo amene wati aka si koyamba kuti chipanichi chitenge galimotoyo.

Iye wati wakwiya kwambiri chifukwa patsiku lomwe galimotoyo imatumikira chipani, pachipatalapo padali maliro anayi amene amafunika anyamulidwe.

“Anamfedwa adandidandaulira, ndipo ndidasiya zomwe ndimachita kukawathandiza pamene galimoto yathu imatumikira chipani,” adatero.

Nkhaniyi ikudza pamene a mabungwe omwe si aboma akukakamiza chipanichi kuti chibweze K13 miliyoni yomwe chidalandira ku nthambi zaboma pa mwambo womwe chipanichi chidachititsa pa 29 July ngati njira imodzi yopezera ndalama.

Kadaulo pandale Mustafa Hussein wati zomwe chapanga chipani cha DPP pogwiritsira ntchito galimoto ya chipatala ponyamula masapota ake pokaperekeza pulezidenti Peter Mutharika ndi kulakwira Amalawi ndipo zotere zitheretu.

“Amalawi sangavomere kuti ndalama zawo zizigwiritsidwa ntchito chonchi. Ndi kulakwa posatengere chipani chomwe chikupanga izi,” adatero Hussein.

Related Articles

Back to top button