Chichewa

Dzombe kukoma, koma…

Listen to this article

 

Kuyambira makedzana, panthawi ya ulendo wa ana Aisiraele kuchoka ku Aigupto kupita kudziko lolonjezedwa lija la Kenani ngakhalenso nthawi ya Yohave Mbatizi anthu akhala akudya dzombe, chiwala chomwe ambiri amachitama kuti chilibe chinzake kumbali ya makomedwe.

Ku Malawi kuno dzombe si lachilendo ndipo anthu akhala akusimba za kandiwo koutsa mudyoka.

Ngakhale m’dziko mukagwa dzombe limaononga mmera m’minda ndi zomera zina, kumbali ina amakhala madalitso chifukwa ngati ndiwo, zoulukazi zilinso ndi ubwino wake kuthupi la munthu chifukwa zili ndi ma protein ochuluka komanso zinc ndi iron, michere yomwe imathandiza kumanga thupi, malingana ndi kafukufuku wa bungwe la Food and Agriculture Organisation (FAO).

Ngakhale pali chiletso, dzombe likugulitsidwa malicheromalichero m’misika monga ku Limbe ndi ku Blantyre
Ngakhale pali chiletso, dzombe likugulitsidwa malicheromalichero m’misika monga ku Limbe ndi ku Blantyre

Mmene zidamveka pa July 22 chaka chino, kuti dzombe latera kusikimu ya Nyamula m’boma la Nsanje ndipo likukhamukira ku Bangula mpaka lafika ku Chikwawa, odziwa za kukoma kwa ziwala zosowazi adangoti laponda lamphawi-ndiwo zapezeka!

Ndi njala ndi njala yomwe yabonga m’maboma awiriwa ambiri sakadatha kuchitira mwina koma kuthokoza Mulungu chifukwa chowatumizira dzombe kuti akhwasule. Nanji kuti lambiri limapezeka lofooka komanso lina lofa kale!

Mauthenga ochenjeza anthu kuti asabwekere dzombeli chifukwa lapoperedwa mankhwala kuti lisapitirize kuononga mmera kuchigwa cha Shire, koma ena akhala akunyalanyaza ndipo sakusiya kutola ndi kukazinga dzombeli n’kumadya mtima uli mmalo.

Senior Chief Malemia wa m’boma la Nsanje komanso mtsogoleri wa komiti yokhazikitsa chitetezo m’boma la Chikwawa, Mike Kalula, atsimikizira Msangulutso za nkhaniyi.

“Uthenga wafika paliponse kuti tisadye dzombeli chifukwa alipopera mankhwala. Koma ena akumatolabe n’kulitsuka kenaka akukulidya. Ndi zoopsa kwambiri, komabe tikuyesetsa kuwalangiza kuti asiye kudya dzombeli,” adatero Kalula.

“Vuto la kuno ndi njala. Kuli njala yadzaoneni ndiye anthu sangapirire kuti asadye

dzombeli pamene alibe podalira, komabe sakuyenera kutero. Ndi bwino kufa ndi njala kusiyana kufa ndi mankhwala.”

Naye Malemia akuti nkhaniyi yawadzidzimutsa ndipo apempha kuti anthu asiye kudya dzombe lofa ndi mankhwala.

“Malipoti oti anthu akumatsuka dzombeli ndi kudya atipezadi, ndipo tili ndi mantha chifukwa titha kutaya miyoyo ya anthu,” adatero Malemia.

Iye adati kutsatira chiletso cha boma, m’boma la Nsanje anthu aleka kugulitsa dzombeli komabe ena akugulitsabe mobisa.

“Chinthu chikaletsedwa, palibe amene angagulitsire poyera, n’kutheka ena akugulitsa mobisa koma ndikuti ayenera kusiya mchitidwewu chifukwa avulaza anthu,” adatero.

Mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, wati wakhumudwa ndi nkhaniyi ndipo wapempha anthu kuti alekeretu kudya dzombeli ponena kuti zingathe kuika miyoyo yawo pachiopsezo.

“Awanso ndiye mavuto enatu, ife taletsa kuti anthu asadye dzombeli chifukwa angathe kukumana ndi mavuto. Ngati boma lalankhula ndiye kuti laonapo kuipa komwe anthu angakumane nako akadya dzombe lofa ndi mankhwala oopsa.

“Atha kudya mwina osaona kukhudzidwa kwake, koma izi zingathe kuwakhudza patsogolo, kotero akuyenera kusiya. Tipemphe amabungwe, atolankhani ndi ifeyo kufalitsa uthengawu kuti anthu asaononge dala miyoyo yawo chifukwa chosusukira dzombe,” adatero Maganga.

Iye adati chiletso chosadya dzombe ndi ziwala chakhudza maboma a kuchigawo cha kummwera chifukwa ndiko kwayandikira maboma a Chikwawa ndi Nsanje amene akhudzidwa ndi kugwa kwa dzombeli.

“Vuto ndi loti ndi zinthu zouluka, ndiye pena uzipeza zafika ku Thambani mpaka kukalowa m’boma la Neno lomwe layandikana ndi maboma amene akhudzidwawa. Ndiye tikuti maboma onse kuchigawo cha kummwera asadye ziwalazi. Tikugwira ntchito ndi apolisi kuti asapezeke wina akugulitsa dzombe kapena ziwala,” adaonjeza Maganga.

Dotolo wina amene adati tisamutchule dzina chifukwa sayankhulira unduna wa zaumoyo, wati anthuwa ali pachiopsezo ngati akudyadi dzombeli.

“Pali mavuto oti angathe kumachita chizungulire, kumva zoyabwa m’thupi komanso kutentha thupi chifukwa cha mphamvu ya mankhwalawa,” adatero poyankhapo zomwe zingawachitikire anthu amene adya dzombe lopoperedwali.

Mkulu woyang’anira za mbewu ku Shire Valley ADD, Ringstone Taibu wati mahekitala ambiri athiridwa mankhwala ndipo ntchito yachitika kwa sabata zitatu.

Kupatula kusasantha mmera wa alimi, dzombeli lidadyanso nzimbe kuminda ya kampani ya Illovo zomwe zidachititsa kuti alipopere mankhwala.

Si minda yokha ya Illovo yomwe yathiridwa mankhwala. Nawo a Shire Valley ADD adapopera minda ya anthu yomwe yakhudzidwa ndipo akugwiritsa ntchito mankhwala a cypermethrin omwe akupheratu dzombelo.  (Zoonjezera: Joseph-Claude Simwaka) n

Related Articles

Back to top button
Translate »