NkhaniSociety

Escom ikhazikitsa ntchito yatsopano ya magetsi

Listen to this article

Boma kudzera ku bungwe la magetsi la Electricity Supply Corporation of Malawi (Escom) lakhazikitsa pulojekiti yotchedwa ‘Ndawala’ yobweretsa magetsi kumidzi pofuna kukweza chiwerengero cha anthu ogwiritsa ntchito magetsi m’dziko muno.

Ntchitoyi cholinga chake ndi kufulumizitsa kulumikizira anthu magetsi m’madera akumudzi komanso m’matauni pangongole yopanda chiwongola dzanja ya ndalama zokwana K75 000, yomwe idzakhale ikuperekedwa pang’onopang’ono podula K20 pa K100 pamagesti olipiriratu a Escom.Escom_meter

Kudzera mu ntchitoyi, yomwe ndi yandalama zokwana K350 million, bungweli likumaikira lokha mawaya munyumba za anthu omwe akumayenera kupereka ndalama zokwana K5 000 kuti awalumikizire magetsi.

Poyankhula pa mwambo wkhazikitsa ntchitoyi ku Ntcheu, Nduna ya zachilengedwe, zamagesti ndi zamigodi, Bright Msaka, adati ndondomekoyi ithandiza Anthu ambiri kupeza magetsi m’dziko muno, makamaka madera amene anthu ena sangathe kupeza ndalama zokwanira kuikira mawaya ndinso kulumikiza magetsi.

“Chifukwa cha chitukuko cha magetsiwa kuno kumudzi, ntchito zambiri zomwe timachita kukwerera basi kupita kutauni, anthu ambiri tizitha kuchitira konkuno kumudzi. Izi zizapangitsa kuti anthu ambiri athe kupeza ntchito komanso kuyambitsa mabizinesi konkuno kumudzi,” adatero a Msaka.

Iye adawonjeza kunena kuti izi zidzachepetsa nthawi imene anthu amataya posakasaka makontilakita komanso kuyendera maofesi a Escom.

M’mawu ake, wapampando wa bungweli, Jean Mathanga, adapempha anthu omwe apindule kudzera mu ntchitoyi kuti asamalire zipangizo zamagesti kuti chitukuko chimenechi chifalikire m’madera ambiri m’dziko muno.

“Mukapeza munthu akuononga zipangizozi, chonde tiuzeni kapena kanenei kupolisi ngakhalenso kwa atsogoleri a m’madera mwanu. Komanso tikapeza waya wa Escom atagwa pansi tiyeni tiwauze a Escom kapena kupanga lipoti kupolisi mwansanga,” adatero Mathanga.

Imodzi mwa mafumu ku Ntcheu, Inkosi Chakhumbira, idati ndi yokondwa kwambiri ndi ntchitoyi ponena kuti ilimbikisa ntchito zamalonda, kuthandizira poteteza zachilengedwe komanso kukhwimitsa chitetezo m’bomalo.

Pakadalipano, kudzera mu ntchitoyi, bungwe la Escom lalumikiza kale magesti kunyumba zoposa 100 mb’oma la Ntcheu.n

Related Articles

Back to top button