Nkhani

‘Fodya n’kunazale’

Listen to this article

Pamene alimi a fodya ali yakaliyakali kukonzekera ulimi wa 2015/16, mlangizi wa zaulimi wa fodya m’boma la Rumphi, Charles Jere, walangiza alimi kuti atsatire ndondomeko ndi malangizo oyenera popanga nazale ya fodya pofuna kupindula ndi ulimi wawo.

Pocheza ndi Uchikumbe posachedwapa, Jere adati nazale ya fodya si ili ngati ya ndiwo zamasamba kaamba koti imafuna chisamaliro chapadera chifukwa kupanda kutero palibe chimene mlimi wa fodya angapindule ndi fodya n’chifukwa chake pali mawu akuti “fodya n’kunazale”.Fodya_Tobacco_nursary

“Choyamba mlimi akuyenera kupeza malo omwe aikepo nazale yake. Malowa akuyenera kukhala kufupi ndi madzi oyenda kapena omwe akuoneka opanda tizilombo toyambitsa matenda a mtundu wina ulionse,” adatero Jere.

Jere adati mlimi akuyenera kutipula nazale kutengera ndi kukula kwa munda wake. Mlangiziyu adati paekala imodzi bedi la nazale likuyenera kukhala lotalika mamita 30 ndi mita imodzi mlifupi pomwe hekitala imafunika mabedi atatu a muyezo woterewu.

“Akapanga bedi lija mlimi akuyenera kutenga mapesi a chimanga n’kuwasanja pabedi lija ndipo akatero awaotche ndi cholinga chofuna kupha tizilombo tomwe tidali mudothi tomwe tikadatha kuononga fodya panazalepo.

“Apa adikire masiku awiri kapena atatu kuti ayambe kufesa fodya panazalepo,” adafotokoza Jere.

Iye adati mlimi ayenera kuthira feteleza wokwana makilogalamu atatu asadafese fodya uja. Akafesa fodyayo athire mankhwala kuti aphe tizilombo monga nyerere zomwe zikhoza kudya mbewuyo.

“Mankhwala ena ofunika kuthira panazale ndi amene amapha tizilombo toyambitsa matenda ena mufodya,” adatero Jere.

Malinga ndi Jere, mankhwalawa amafunika kusungunula mutheka la madzi a mukheni ndi kuwathira panazale paja pataikidwa kale maudzu.

Akatero mlimi akuyenera kuthirira nazale ija kamodzi patsiku, koma fodya uja akayamba kumera pamafunika kuthirira kawiri patsiku ndipo kuchuluka kwa madzi kuziyenderana ndi kusunga madzi kwa dothi. n

Related Articles

Back to top button