Chichewa

Gogo apezeka atafa atadulidwa manja, mwendo

Gogo wina wa zaka 75 wapezeka atafa m’nkhuti yokumbamo dothi loumbira njerwa m’mudzi mwa Tebulo Gondwe ku Enukweni m’boma la Mzimba, koma alibe manja ndi mwendo umodzi.

Malinga ndi mdzukulu wa gogoyu, Petrona Nkunika, Gogo Watson Mapala adachoka kunyumba kwake Lamulungu sabata ziwiri zapitazo atatsanzika mdzukulu wakeyo kuti akukaona achimwene ake pamtunda wa makilomita anayi.

crime

Nkunika adati anthu a m’mudzi wa Tebulo Gondwe adali odabwa pa 15 August polandira uthenga woti akaone munthu yemwe adapezeka atafa m’deralo.

“Kuchokera kumayambiriro a mwezi uno agogo tinali nawo pasiwa popeza mayi anga adamwalira. Tidakhala nawo mpaka tsiku losesa sabata ziwiri zapitazo pomwe adanditsanzika kuti akupita kwa achimwene awo,” Nkunika adatero.

Iye adati sadafufuzenso ngati gogoyu adafika kwa mbale wawoyo.

Nkunika adati akuganizira kuti gogoyu adaphedwa chifukwa cha mkangano kaamba ka malo.

Iye adati pali magulu awiri omwe akukanganirana malo omwe ali pakati pa Enukweni ndi Kavala ndipo Mapala ndi amene amadziwa bwino mbiri yake.

Iye adati mmodzi mwa anthu omwe akukanganirana malowo adaospeza gogoyu kuti amupha sabata ziwiri zapitazo.

“Ife tikuganizira kuti agogo adaphedwa ndi munthu yemwe adawaospezayu,” Nkunika adatero.

Iye adati apolisi atafika pamalopo adapempha anthuwo kuti ayang’ane ziwalo zosowazo m’tchire lozungulira deralo, koma sadazipeze.

Mneneri wa polisi m’chigawo cha kumpoto, Morris Chapola, adatsimikiza za nkhaniyi koma adati adakali mkati mofufuza.

Related Articles

Back to top button