Nkhani

Gule alipo pa 17 October

Listen to this article

Zipani za UDF ndi PP zaimika manja kuti sizidzapikisana nawo pamipando ya phungu pachisankho cha chibwereza chimene chikhalepo pa 17 October chifukwa maso awo ali pachisankho chapatatu mu 2019.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho cha chibwereza m’malo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene enawo ndi makhansala.

Chisankho cha chibwereza chidalikonso mmbuyomu

Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu.

Mneneri wa UDF Ken Ndanga akuti ndondomeko ya chipani chawo ndi kupikisana malo amene akudziwa kuti achita bwino.

“Komabe sikuti tangokhala, tili ndi zochitika m’maderawo,” adatero Ndanga amene wati kusapikisana kwawo si tanthauzo lothandiza chipani cha DPP.

Ndipo mneneri wa chipani cha PP, Nowa Chimpeni adati maso awo lili pomanga chipani chomwe chidzalowenso m’boma mu 2019.

“Iyi ndiye ndondomeko yathu. Musandifunse kuti ndi ndondomeko zanji,” adatero Chimpeni amene adatsindika kuti PP siyikutha.

Koma katsiwri wa ndale Mustapha Hussein wati zipanizo zikadaganiza mozama chifukwa chisankho chilichonse ndi mwayi wopima mphamvu za chipani.

Ndanga: Chipani sichikutha

Zipanizo zati maso awo ali pachisankho cha patatu chomwe chichitike mu 2019. Mmalo mwake, chipani cholamula cha DPP ndi MCP ndiwo sakumwetsana madzi.

Koma Hussein wati PP ndi UDF akuyenera aganize kawiri chifukwa chisankho chilichonse n’chofunika popima mphamvu za chipani.

“Kukonzekera 2019 kumayenera kyamba pano, ndipo njira yabwino ndi kuchita nawo chisankho chachibwereza chomwe chimaonetsa mphamvu zachipani,” adatero Hussein.

Poyankhapo pa maganizo a Hussein, Ndanga akuti chisankhochi sichisonyezo zomwe zidzachitike pachisankho cha 2019.

Chimpeni: Tikukonzekera 2019

“Taonapo chipani chikupambana chisankho chachibwereza, koma kubwera chisankho chenicheni kugonja,” adatero.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho chachibwereza m’malo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene ena ndi makhansala.

Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu.

MEC idakhazikitsa nthawi ya kampeni pa 13 September ndipo kampeniyi idzatsekedwa pa 15 October kuti pa 17 chisankho chidzachitike.

Bungweli lavomereza anthu 19 kuti apikisane nawo, amuna 15 ndi amayi anayi. Chisankho cha aphungu chichitika kumpoto chakummawa kwa boma la Lilongwe. Kumeneko apikisane ndi Ellen Shaban Kadango woyima payekha, Christopher Joseph Manja woyima payekha, Ulemu Msungama wa MCP ndi Ruben Ngwenya wa DPP.

Aphungu apikisananso kumpoto kwa Lilongwe Msozi komwe apikisane Bruno Daka wa DPP ndi Sosten Gwengwe wa MCP, yemwe adali wotsatira Joyce Banda wa PP pachisankho cha patatu mu 2014.

Ku Nsanje Lalanje apikisane ndi Gladys Ganda wa DPP, Laurence Mark Sitolo wa MCP, ndi Winnie Wakudyanaye woima payekha.

Chisankho cha makhansala chichitika ku Mtsiliza wodi komwe Brighton Golombe Edward wa UDF, Julio Benedicto Jumbe wa DPP ndi Kinwel Frank Zikaola wa MCP apikisane. Kummawa kwa Mayani wodi komwe Nicholas Fackson Josiya wa DPP, Everister Ndaziona Kusina wa UDF, Benson William Lameck wa MCP sakumwetsana madzi.

Nako ku Ndirande Makata wodi chilipo cha makhansala komwe Ishmael Chilambo wa UDF, Thom Lita wa DPP, Thom Harry Litchowa wa MCP, Mathews Joseph Shaba wa PP akupikisana.

Mneneri wa MEC, Sangwani Mwafulirwa wamema anthu ndi zipani kuti zisunge bata pa nthawiyi ndipo aliyense wodzetsa chisokoneza adzalangidwa.

Related Articles

Back to top button