Nkhani

Gulewamkulu, agumula sitolo

Gulewamkulu wina Lachwiri lapitalo akumukayikira kuti adagumula sitolo ina pamsika wa Nkhalambayasamba m’boma la Mchinji ndipo akumukaikira kuti adasakaza katundu wa K3.5 miliyoni.

Mneneri wapolisiyo, Kaitano Lubrino, Lachisanu adati apolisi amanga anthu 16 amene akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo.

Apolisi kuyendera sitolo idathyoledwayo

“Anthu onsewa tikuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi zophwanya sitoloyo komanso kuba katundu,” adatero Lubrino.

Malinga ndi Lubrino, kuderalo kudamwalira mkulu wina wa bizinesi Rabson Wisalamu ndipo imfayo idadabwitsa anthu.

Malinga ndi mfumu Nani yomwenso ndi mbale wa malemuyo, imfayo anthu amaganiza kuti imfayo idali yamatsenga.

“Adali mushopu yake akugulitsa katundu. Kenaka tidangomva kuti m’thupi mukumuwawa, kupita naye kuchipatala cha St Gabriel, adangoti ndagona pano. Kwathu sadayambane ndi aliyense, tikupenekera kushopuko kuti alipo adayambana naye kuti mpaka amuchitire chipongwe,” adatero Nano polankhula naye pafoni.

Patsiku logumula sitoloyo, maliro a Wisalamu adaikidwa, ndipo mwambo utatha, akuti kudavumbuluka gulewamkulu pamsikawo.

Guleyo akuti adalipo 20, ndipo atafika pagolosale ya Julaye, adagumula shopuyo ndi kuyamba kutenga katundu wina akumusakaza.

“Kafukufuku wathu wapeza kuti pamene guleyo amafika n’kuti Julaye ndi banja lake atathawa kale ndipo komwe ali sikukudziwika koma tikufufuzabe,” adatero Lubrino. “Izi zitachitika guleyo adabwerera atatuta katundu wa m’shopumo.”

Mphekesera zikumveka kuti guleyo amachokera ku dambwe la Nani chifukwa kumeneko ndi komwe kumachokera malemuwo.

Koma mfumu Nani yauza Msangulutso kuti ilo ndi bodza. “Ine ndi anthu anga titachoka kumanda tidabwerera kunyumba kukapitiriza mwambo wa maliro. Dziwani kuti ife tidavomereza imfa ya munthu wathu ndipo palibe amene tikumuganizira,” adatero amfumuwo.

Lubrino wati apolisi anjata gulupu Kabuthu amene dzina lonse ndi Tenthani Nsaima a zaka 46 komanso woyang’anira msika wa Nkhalambayasamba, Daniel Joseph wa zaka 40 onse a kwa mfumu Mavwere m’bomalo kuti akayankhe mafunso angapo za umbandawo.

Posakhalitsapa, gulewamkulu adagwidwa ku Chikwawa ataba mbuzi, komanso mumzinda wa Lilongwe guleyo wakhala akugenda galimoto zomwe sizimupatsa ndalama.

Mfumu ya mtundu wa Achewa, Kaomba akuti uyu si gulewamkulu koma zigandanga dzomwe zikufuna kuononga chikhalidwe chawo.

“Awa akungotionongera mbiri. Gulewamkulu amasunga mwambo. Ichitu ndi chikhalidwe,” adatero.

Apolisi ati akufufuzabe kuti anjate amene adachita chipongwecho.

Related Articles

Back to top button