Nkhani

Gulewamkulu ndi mankhwala

Listen to this article

Matenda akagwa pakhomo, makolo amakhala ndi njira zochuluka zothetsera matendawo malinga ndi zikhulupiriro zawo. Ena okhulupirira gulewamkulu akuti ngati m’thupi mwabaya, akangovina wodwala amachira pomwepo. M’mudzi mwa Siledi kwa Senior Chief Kanduku m’boma la Mwanza muli mayi wina amene ati adachira gulewamkulu atapalasa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mkulu wa dambwe kumeneko, Maxwell Kondwerani.

Gulewamkulu akuti ndi mankhwala
Gulewamkulu akuti ndi mankhwala

Tidziwane maudindo wawa…

Ndili ndi maudindo angapo, ndine nduna ya mfumu m’dera lino. Ndimamemeza anthu am’mudzi muno ngati pali zina kuti zichitike kapena mfumu yaitana. Ngati anthu am’mudzi muno ali ndi zochita zina monga mwa zikhulupiriro zawo amandifikira kuti ndipereke uthenga kwa mfumu yathu yomwe imaloleza zochitikazo komanso kudambwe ndili ndi gawo langa.

Tikambe nkhani ya gulewamkulu…

Mufuna ndikambe nkhani iti kumeneku? Pajatu zakudabwe saulula, mumadziwa zimenezo?

Inde koma, n’zabwinobwino, osati zofwala gule.

Chabwino, nkhani yake ndi yotani yomwe mufuna ticheze?

Tikumva kuti guleyu ndi mankhwala, ndi zoona?

Ndi zoona. Ife Achewa timakhulupirira zimenezi. Izi kuno zimachitika ngati mizimu yalamula kuti tichite.

Zimakhala bwanji kuti mpaka zifike poitana gule?

Timakhala talamulidwa ndi mizimu kuti gulewamkulu avine ndi cholinga chochotsa matendawa. Izi sizitheka popanda kulamulidwa ndi mizimu.

Talongosolani chiyambi chake chimakhala chotani kuti mizimu ilamule?

Munthu ngati akudwala, timayenda naye mwa asing’anga momwe timakaombeza za chiyambi cha matendawo. Kumeneko n’komwe amanena ngati matendawo akufunika kuvinira gule kapena angomwa mankhwala. Apa ndikutanthauza kuti sizingatheke kuti mungoyamba kuvinira matenda ngati mizimu sidanene.

Akati gule akavine zimakhala bwanji?

Amanena kuti mukatenge chikho cha msunje ndipo tikaikemo ufa ndi kukanda. Apa mumayamba kumuzungulitsa chikho chija. Pomwe mukuzunguliza chikho chija mumaimba nyimbo. Tikatha amati tikataye patsinde pa mtengo. Pomwe tikuchita izi ng’oma zimakhala zikusweka komanso zilombo zikuvina.

Taimbani nyimboyo ndimve…

Timati….Tidzutsire wathuyu bwino, ngati ndi mizimu wathuyu adzuke. Mizimu mudzutse wathu pofika mawa…

Kodi matendawa amakhala atafika pothiphwa kwambiri?

Eee! Matenda amakhala afika povuta ndipo tikamati tidzutsire wathuyu ndiye kuti amakhala salinso mwakanthu.

Akamati mukavine gulewamkuluyo amakupatsani mankhwala alionse?

Palibe mankhwala alionse omwe amatipatsa ndipo machiritso amagona pamenepo. Mukavina ndi kutsata zomwe akunenazo matenda amathera pomwepo.

Ndani amayenera kupezeka pamwambo ngati umenewo?

Akuluakulu a gule amapezeka pamalopo komanso mwini mbumbayo. Pomwe tikusankha mwini mbumba timayenera kusankha yemwe adalowa gule wamkulu osangotenga aliyense.

Kodi zimatheka kuti gule avine chikhalirecho sindiwe wolowa?

Sizingatheke. Kuno zimachitika chifukwa aliyense adameta kapena kuti kugula njira.

Kodi munthu amachira?

Kwambiri ndipo chitsanzo chabwino ndi matenda omwe tidali nawo miyezi yapitayi. Mayi ameneyo adalumidwapo ndi njoka kawiri, titapita naye kokaombeza adatiuza kuti tikufunika tikamuvinire gulewamkulu. Tidapempha mfumu kuti timuvinire. Tidachita izi ndipo adachira tsiku lomwelo. n

Related Articles

Back to top button