Chichewa

Gwamba wochokera kubanja loimba

M’dziko muno muli oimba osiyanasiyana. koma kukamba za oimba nyimbo zauzimu, Gwamba ndi mmodzi mwa oimba amene akusintha miyoyo ya anthu pa Malawi pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

 

Gwamba: Ndi nyimbo zokoma kwambiri

Gwamba, ndimasule kuti ndikudziwe bwinobwino m’machezawa.

Dzina langa lonse ndi Duncan Gwamba Zgambo omaliza m’banja la ana anayi ndipo kwathu ndi m’boma la Rumphi ku mpoto kwa dziko la Malawi.

Anthu ambiri amangoti Gwamba, tawauze kuti kodi Gwambayo ndi wotani ndipo amakonda chiyani.

Zikomo kwambiri, Gwamba ndi dzina lomwe ndimatchukadi nalo ngati oyimba koma munthune ndimapanga zambiri monga mabizinesi ndi zina. Kuimbaku ndi chimodzi mwa zochita zomwe ndimapanga pamphepete pa mabizinesi.

Kodi iweyo zoimbazi udayamba bwanji?

Funso labwino ndipo anthu ambiri amandifunsa zimenezi moti ndikayankha iweyo ndiye kuti ndayankha anthu ambiri nthawi imodzi. Munthune ndimachokera ku banja la zoimbaimba. Malume anga, Bright Nkhata, adali munthu waluso kwambiri pa zoimba moti ambiri amamudziwa bwino. Kupatula apo, malume anga ena, Bernard Kwilimbe, nawonso ndiwokonda zoimba kwambiri moti oimba ena m’Malawi muno adaphunzira kwa anthu awiri amenewa. Mwachidule, zoyimbazi ndi za m’magazi osati kuchita kuphunzira kapena kukakamiza ayi.

Watulutsa chimbale posachedwapa, kodi udachitulutsa liti ndipo chimatchedwanji?

Chimbale chimenechi chikutchedwa Jesus is my Boss kutanthauza kuti Ambuye Yesu ndi bwana wanga. Ndi nyimbo ya uzimu yokoma kwambiri ndipo ili ndi tanthauzo ndi chiphunzitso chapamwamba kwa okhulupilira.

Chimbale chimenechi chidakhazikitsidwa pa 24 December 2016 ku Bingu International Convention Centre (BICC) ija ena amati 5 Star Hotel.

Chimbalechi chili ndi nyimbo zingati ndipo zina mwa izo ndi ziti?

Chimbalechi chili ndi nyimbo 11 ndipo papita luso ndikudzipereka kuti chituluke ndi kumveka momwe chimamvekeramu. Kudatengera kudzipereka kwa anthu angapo monga oimba, ojambula ndi azipangizo omwe. Muli nyimbo monga Anabwera Yesu yomwe ndimayikonda kwambiri komanso ndiyo yoyambirira. Mulinso nyimbo yotchedwa Bwana yomwe adathandizira Lulu ndipo nayonso ndi nyimbo yokoma kwambiri. Mwachidule, nyimbo zomwe zili m’chimbalechi nzokoma zokhazokha.

Pomaliza ungawauzenji amalawi okonda nyimbo?

Mawu ambiri ndilibe koma kungowapempha kuti apitirize kupereka chilimbikitso kwa oimba kuti azipita patsogolo chifukwa iyi ndi njira yokhayo yomwe nyimbo za ku Malawi zingapeze msika kunja kwa dziko

lino. Ndimazindikira kuti zambiri, dziko lino likukwera kumene ndipo zonse zikutengera Amalawi eni ake kuzitukula. n

Related Articles

Back to top button