Chichewa

‘Idali nthawi ya buleki’

Listen to this article

 

Sukulu iliyonse imakhala ndi nthawi yopumira kapena kuti nthawi ya buleki. Ena amakangosewerako, ena amakadya, koma Paul Chidale ndi Dolica Mchenga adasinthana Chichewa.

Paul Chidale ndi katswiri wosewera golf komanso akugwira ntchito ku Gestetner ngati ICT Engineer. Dolica ndi wabizinesi.

Kukumana kwawo sikukugwirizananso ndi ntchito yawo chifukwa adakumana onsewa ali pasukulu ku Bangwe Private School mumzinda wa Blantyre.

Paul akuti panthawiyo adali fomu 3 pamene Dolica adali fomu 1. Iwowa adakhala akuponyerana maso, koma zonse zidakathera kubuleki.

Paul kusayinira kuti watengadi Dolica patsiku lodalitsa ukwati wawo
Paul kusayinira kuti watengadi Dolica patsiku lodalitsa ukwati wawo

“Timaponyerana maso mosonyeza kuti timafunana. Tidapezera mwayi nthawi ya buleki pamene tidakumana ndi kucheza,” adatero Dolica.

“Adati akundifuna, koma ndidavutavuta ngakhale pansi pa mtima nanenso ndimamufuna Paul. Kungoti Paul amandisangalatsa machezedwe ake ndi anthu komanso malankhulidwe ake opatsa chikoka,” adaonjezera.

Paul akuti padatenga kanthawi kuti amumasule Dolica ndi mawu akukhosi chifukwa amafuna aone ngati namwaliyu adali ndi makhalalidwe abwino.

“Zooneka bwinozo ndiye musakambe, namwaliyu ali bwino komanso ndimafuna kuonetsetsa makhalalidwe ake. Nditakhutira, ndidaganiza zomupezera nthawi ndipo kudali kubuleki komwe ndidakamuuza mawu anga,” adatero Paul.

Izitu ati zimachitika mwezi wa April mu 2007.

Ukwati ndiye adamanga pa 4 October 2015, ku Feed the Children ku Nyambadwe mumzindawu.

“Amene sadakwatire afatse kaye chifukwa ukwati weniweni umachitika kamodzi pamoyo wa munthu mpaka Mulungu adzakulekanitseni. Ndiye akuyenera atsimikizedi za yemwe akufuna amukwatire kapena kuwakwatira,” adatero Paul wa m’mudzi mwa Luwanje kwa T/A Chikumbu m’boma la Mulanje, polangiza omwe akulingalira za banja.

Dolica ndi wa m’mudzi mwa Chidale kwa T/A Makwangwala m’boma la Ntcheu. Awiriwa tsopano adalitsidwa ndi mphatso ziwiri. n

Related Articles

Back to top button