Nkhani

Ine ayi, Dausi wakana Chaponda

Listen to this article

 

Zomwe zachitika ku bwalo la mirandu ku Lilongwe m’sabatayi zalephera kupherezera mwambi woti khoswe akakhala pa mkhate sapheka.

Khwimbi la anthu lidapita kubwaloli Lachiwiri kukamvera mlandu wa nduna yakale ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi George Chaponda koma adachokako akupukusa mitu.

Dausi: Anangotenthedwa

Zomwe aliyense samayembekezera zidachitika nduna yazofalitsa nkhani Nicholas Dausi itanena mmaso muli gwaa kuti siikudziwapo kanthu pa ndalama zomwe zidapezeka m’nyumba mwa Chaponda, mlandu omwe akuyankha pakali pano.

Chaponda akuyankha mlandu wopezeka ndi ndalama zankhaninkhani za m’Malawi komanso zakunja m’nyumba popanda chilolezo cha Reserve Bank of Malawi monga momwe zimayenera kukhalira.

Podziteteza ku mlanduwu, Chaponda adauza bwalo la milandu kuti K95 miliyoni pa ndalamazo zidali za chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) ndipo kuti Dausi ndiye amayenera kukatenga ndalamazo n’kukapereka kuchipani.

Poperekera umboni wake, Dausi adauza bwalolo kuti zoti ndalamazo zidali za DPP nzabodza komanso kuti dzina lake lidangotchulidwamo nkhaniyi iye sakudziwapo kanthu.

“Zoti ine ndikudziwapo kanthu nzabodza. Mwina [Chaponda] adangosokonekera ponditchula chifukwa munthu akakhala pampanipani oterewu, kaya ndi phungu kapena nduna, mphamvu zimatheratu,” adatero Dausi.

Chaponda adali mmodzi mwa nduna zikuluzikulu za boma ndipo zake zidatembenuka chaka cha 2017 ali nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi pomwe adayamba kufufuzidwa poganiziridwa kuti amakhudzidwa ndi kusokonekera kwa kagulidwe ka chimanga ku Zambia.

Chaponda adamangidwa limodzi ndi mkulu wa kampani ya Transglobe Produce Export Limited Rashid Tayub ndi Grace Mijiga Mhango wa bizinesi yemwenso ndi wa pampando wa bungwe la makampani ogula ndi kugulitsa mbewu.

M’mwezi wa February, nthambi yolimbana ndi katangale idakachita chipikisheni ku nyumba ndi ku ofesi ya Chaponda komanso ku mawofesi a Admarc komwe kudapezekanso zododometsa zina.

Kuofesi ya Admarc, nthambiyi idalanda makina a kompyuta pomwe kunyumba kwa Chaponda idapezako ndalama zankhaninkhani za  dziko lino ndi maiko ena monga za ku Amereka zomwe zidapangitsa kuti nkhaniyi yomwe poyamba imakhala ngati ingawakomere a Chaponda, itembenuke.

Related Articles

Back to top button