Nkhani

JB asankha Kachali

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda Lachitatu adasankha Khumbo Kachali kukhala wachiwiri wake.

Kachali, yemwe ndi phungu wa ku Mzimba, ndi wachiwiri kwa Banda m’chipani cha People’s Party (PP).

Kachali ndi wachinayi kukhala paudindowu kuchokera pomwe dziko lino lidayamba ndale za zipani zambiri mu 1994. M’mbuyomu, Justin Malewezi, Cassim Chilumpha ndi Banda adakhalapo paudindowu.

Kusankhidwa kwa Kachali kudadza tsiku limene Banda adasuntha mlembi wamkulu muofesi ya mtsogoleri wadziko lino ndi nduna zake woona za madyedwe ndinso za HIV Dr Mary Shawa kupita kuunduna woona za amayi.

Maudindo ambiri akhala akusinthidwa m’sabatayi kutsatira imfa ya mtsogoleri wakale wadziko lino Bingu wa Mutharika, yemwe adamwalira pa 5 Epulo kunyumba ya boma ku Lilongwe atadwala nthenda ya mtima.

Thupilo adalitengera kuchipatala cha Kamuzu Centre mumzinda wa Lilongwe koma malinga ndi malipoti achipatala akuti Mutharika adali atamwalira kale pomwe amafika kuchipatalako.

Madzulo a Lachinayilo, boma lidati Mutharika amutengera ku KCH komwe adati akudwala mtima.

Lachisanu pa 6 mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bakili Muluzi komanso Banda adachititsa msonkhano pomwe adati malamulo adziko lino akuyenera kutsatidwa pa yemwe alowe m’malo mwa Mutharika ngati iye wadwalika kapena wamwalira.

Lachisanu lomwelo cha m’ma 11 koloko usiku, akuluakulu ena aboma monga Patricia Kaliati, Nicholas Dausi, Kondwani Nankhumwa, Symon Vuwa Kaunda adachititsa msonkhano wa atolankhani ku Area 4 mumzinda wa Lilongwe.

Pa msonkhanowo, Kaliati adatsutsa zomwe Muluzi komanso Banda adanena ndipo adati Banda sakuyenera kukhala mtsogoleri chifukwa adachoka m’chipani chomwe chimalamulira cha DPP ndikukayambitsa chipani chake cha PP.

Kaliati adakananso kuti sanena momwe Mutharika akupezera koma adangoti ali ku chipatala cha Milpark m’dziko la South Africa.

Apa n’kuti nyumba zoulutsira mawu zamaiko ena zitalengeza kuti Mutharika wamwalira.

M’mawa wa Loweruka Ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna idalengeza kuti Mutharika wamwalira ndipo idati Amalawi akhuza malirowo kwa masiku khumi.

Lowerukalo, yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleriyu, Joyce Banda adalumbiritsidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino.

Mutharika yemwe adali mwana wa mphunzitsi adabadwa mu Febuluwale 1934 ndipo amachokera m’mudzi mwa Kamoto m’boma la Thyolo.

Mutharika dzina lake adali Ryson Webster Thom ndipo adasintha dzinali m’zaka za m’ma 1960.

Malemuwa omwe adali katswiri pa zachuma adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko la Malawi mu 2004 kukhala mtsogoleri wa dziko lino ataimira chipani cha UDF.

Related Articles

Back to top button