Nkhani

K85 000 kapena chaka kundende atapha galu

Listen to this article

Ena amangopha agalu koma sapatsidwa chilango, koma khoti la Ulongwe Majisitireti ku Balaka lalamula kuti mfumu ina ilipe K85 000 apo ayi, ikakhale kundende chaka chimodzi kaamba kopha galu ndi kuwononga mmera m’dimba la mkulu wina.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka, Joseph Sauka, mfumuyi ndi Peter Kasanga koma dzina lake lenileni ndi Michael Mailosi, wa  zaka 62.arrest

Sauka adauza Tamvani m’sabatayi kuti nyakwawayi pa 19 March chaka chino idapezeka m’dimba la Yona Nansambo ikuswa malambe. Poswapo akuti idawandanso chimanga cha mkuluyu.

Iye adati Nansambo atadzudzula mfumuyi kuti isiye zimene imachita m’dimbamo, iyo idakula mtima ndipo idayamba kuthafulira mwini dimbali ndipo ndewu idabula pakati pa awiriwa.

Achibale 6 a mfumuwo akuti atamva kuti mfumuyi ikugogodana ndi munthu, adathamangira kudimbako komwe adakalowerera ndewuyo.

“Bwalo la milandu lidamva kuti anthuwo sadalekere pomwepo koma adalonda mwini dimbayu kunyumba kwake komwe adakaswa galasi la galimoto komanso kupha galu,” adatero Sauka.

“Kubwaloko, anthuwa adakana za mlandu wopha chiweto malinga ndi gawo 343 la malamulo a dziko lino, komanso adakana mlandu wowononga galimoto malinga ndi gawo 344. Koma bwalo litabweretsa mboni, anthuwa adapezeka ndi mlandu.”

Wapolisi woimira boma pamlanduwo, Sergeant Yohane Chaomba, adapempha bwalo kuti lithambitse mfumuyi ndi chilango chokhwima chifukwa monga mfumu sidaonetse chitsanzo chabwino.

Sauka adati mfumuyi idapempha bwalo kuti limumvere chisoni chifukwa ndi yokalamba komanso kuti mkazi wake akudwala.

Koma Third Grade Magistrate Peter Mkuzi adalamula mfumuyi kuti ilipe K60 000 powononga komanso K25 000 popha galu, apo ayi, akaseweze chaka kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga.

Mkuzi adalamulanso abale asanu a mfumuyi kuti alipe K25 000 aliyense, apo ayi, akaseweze kundende miyezi isanu ndi inayi (9).

Omangidwa akuchokera m’mudzi mwa Peter Kasonga, kwa T/A Kalembo m’bomalo. Pofika Lachinayi pa 11 June n’kuti anthuwa asadapereke chindapusacho.

Related Articles

Back to top button