Nkhani

Kalembera wa mafoni aima

Listen to this article

Boma laimitsa kalembera wa lamya za m’manja yemwe nthambi yoyendetsa ntchito za mauthenga ya Malawi Communications Regulatory Authority (Macra) idakhazikitsa mwezi watha.

Macra idalamula kuti aliyense yemwe ali ndi lamya ya m’manja alembetse nambala ya lamya yakeyo pasadafike pa 31 March 2018 apo biii nambalayo idzasiya kugwira ntchito.

Unduna wa zofalitsa nkhani wati boma laganiza zoimika kalemberayu potsatira maganizo a anthu omwe akhala akukhuthula nkhawa zosiyanasiyana zokhudza kalemberayu.

“Tikudziwa kuti kalemberayu ndi wofunika potsatira malamulo koma poti ili ndi boma lomva maganizo a anthu, tayamba taimitsa kaye kalemberayu mpaka tikonze zinthu zina,” chidatero chikalata chochokera ku undunawu.

Kuimika kwa ntchitoyi kwakwiyitsa mkulu wa bungwe loyimira ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) Davis Kapito yemwe mmbuyomo adayamikira Macra kaamba kokhazikitsa ntchitoyi.

Iye wati ganizoli ndi lolakwika chifukwa kalemberayu amatsatira lamulo lomwe lidakhazikitsidwa m’Nyumba ya Malamulo kotero kumuimika kumayenera kudzera ku nyumba yomweyo.

“Ngati padali nkhawa kaya mavuto amayenera kupititsa nkhawazo ndi mavutowo ku Nyumba ya Malamulo osati nduna kapena unduna kungodzuka mmawa n’kuyimika kalembera ofunika ngati ameneyu,” adatero Kapito.

Nkhawa zambiri za anthu pa kalemberayu zidali mayendedwe kuchoka kumudzi kukafika komwe kuli malo olembetserakowo ndi nthawi polingalira kuti posachedwapa, anthu amaima pamizere italiitali kudikira kulembetsa zitupa za unzika.

Kapito adati dziko la Malawi limakhalira mmbuyo pankhaniyi chifukwa maiko ena adayamba kale kuchita kalembera wamtunduwu.

“M’maiko ena sungangogula khadi ya lamya pamsewu n’kuyamba kugwiritsa ntchito osalowa m’kaundula n’chifukwa chake anthu amangogula khadi n’kupangira zolakwika n’kulitaya,” adatero Kapito.

Related Articles

Back to top button