Nkhani

Kalembera wa nzika wayamba

Listen to this article

Boma, kupyolera m’nthambi ya National Registration Bureau (NRB), Lachitatu lidayamba gawo loyamba lolemba Amalawi kuti akhale ndi zitupa za unzika.

Gawo loyamba la kalemberayu idayamba m’maboma a Nkhotakota, Ntchisi, M   chinji, Kasungu, Salima ndi Dowa. Ntchitoyi, imene ikhale m’magawo atatu, idya K36.5 biliyoni ndipo Amalawi 9 miliyoni alowa m’kaundula.

Ntchito ya kalemberayo ku Mchinji Lachitatu

Malinga ndi mneneri wa nthambi ya boma imene ikuyendetsa ntchitoyi ya NRB Norman Fulatira, kalemberayu wayamba bwino ndipo ndiwothandiza kwambiri.

“Kukhala ndi chitupa cha unzika kuthandiza m’njira zambiri. Apolisi, akaona munthu amene akumukaikira kuti ndi wakunja, azidzamufunsa kuti aonetse chitupa chake. Polembetsa anthu opindula pa ntchito za mthandizi, sabuside, nthawi ya chisankho komanso kuchipatala, Amalawi azidzangoonetsa chitupa cha unzika,” adatero Fulatira.

Fulatira adatsutsa malipoti oti pali mavuto ndi malipiro a anthu omwe akugwira ntchitoyi. Iye adati boma silidalandire lipoti lina lililonse lokhudza mavuto.

“Zomwe tikudziwa n’zoti malipiro adachedwa masiku awiri oyambirira okha pomwe anthuwa amachita maphunziro awo chifukwa choti tidali tikuwakonzera ziphaso,” adatero Fulatira.

Pamene ntchito yopereka zitupa za unzikayo yayamba, bungwe lophunzitsa anthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (Nice) likuthana ndi mphekesera zina zimene zingafoole Amalawi kukalembetsa.

Malinga ndi mkulu wa Nice m’chigawo chapakati, anthu ena akhala akufalitsa kuti kalemberayu ndi njira yothandiza kudzabera pachisankho cha 2019.

“Azipembedzo ena amauzanso anthu kuti kalemberayu akusonyeza kuti dziko likutha. Ndipo ena akuti boma likungofuna kugwiritsa ntchito kalemberayu pokapemphera thandizo kumaiko a kunja. Zonsezi ndi nkhambakamwa chabe,” adatero Naphiyo.

Iye adati bungwelo lifikira Amalawi ambiri pofuna kuthana ndi mphekeserazo zimene zingasokoneze ntchito ya kalemberayo.

Mkulu wa Nice Ollen Mwalubunju adati ntchito yophunzitsa anthu za kalemberayu imavuta chifukwa madera ena adali ovuta kufika.

“Kudali malo ena m’maboma a Ntchisi ndi Dowa komwe sitidafikeko chifukwa n’kovuta mayendedwe. Choncho tidapempha mafumu komanso aphunzitsi kuphunzitsa anthuwa za kalemberayu,” adatero Mwalubunju.

Mkuluyu adatinso agwiritsa ntchito wailesi za m’madera pofalitsa uthenga.

Iye adati bungwe lake lidakumananso ndi vuto la kusowa kwa galimoto chifukwa ntchitoyi imafuna kufikira m’madera ambiri.

Kupatula apo, Mwalubunju adatinso ophunzitsa anthuwa adakumana ndi anthu a zikhulupiro zina zomwe sizilola kulembetsa.

“Koma tidawalimbikitsa kuti kalemberayu ngwa aliyense ndipo kupanda kutero kukhala kusemphana ndi malamulo a dziko lino,” adatero Mwalubunju.

DC wa boma la Mchinji, Rosemary Nawasha adati m’bomali mudalibe mavuto ena aliwonse pokonzekera kalemberayu.

“Anthu achilandira bwino kwambiri ndipo sitidakumane ndi mavuto,” adatero Nawasha

Polankhulapo, mlembi wa Traditional Authority Mkanda m’boma la Mchinji Friday Nkhoma adati anthu a m’derali ndiwokonzeka kulembetsa. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »