Nkhani

Kasakaniza pa Khrisimasi

Pa 25 Disembala chaka chilichonse Akhristu padziko lapansi amakumbukira kubadwa kwa Yesu.

Tsikuli ndi mawa laliwisili.

M’malo ambiri m’nyengoyi, chisangalalochi chimakathera m’maphwando a kunyumba komanso kuntchito, mpaka kulowa m’chaka chatsopano.

Pofika tsiku la Khirisimasilo, chisangalalo chimakhala chitakuta miyoyo ya anthu ambiri.

Ena amakayambira kutchalitchi n’kukamalizira kunyumba komwe pena fumbi limakhala liri koboo! magule ndi maphwando ali mkati.

Uku zifuyo zimakhala zikuphedwa kuti zikometsere zonse.

Zakumwa zimayenda ponseponse, wailesi zikusonkhezera dansi za mnanu pomwe ana amakonza maulendo kukayendera abale.

Koma pomwe ena akuti chaka chino ziyenda monga kale, ena akuti mavuto akula ndipo chisangalalochi chiwalambalala.

Makosa Fumani wa m’mudzi mwa Mankhamba 2 kwa T/A Tomasi m’boma la Thyolo wati kukhala kovuta kuti munthu wakumudzi alowerere manyado a Khirisimasi.

“Chaka chatha zinthu zidali bwino ndipo tidakwanitsa kugula zoyenera pachisangalalo.

“Chaka chino mavuto ayanga ponseponse ndipo chisangalalo chasowa,” watero Funani.

Geoffrey Assam Banda wa m’mudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere m’boma la Chiradzulu wati iye sadaonepo chaka chowawa ngati chino.

Iye wati zinthu zakwera mtengo kangapo konse chaka chino, zomwe wati zisokoneza chisangalalo.

Pambali pa mapemphero, iye wati chaka ndi chaka amasonkhana ndi anzake komanso banja lake n’kudyera limodzi.

Izi akuti zimafuna pafupifupi K10 000.

Koma iye wati chaka chino izi kulibe chifukwa sizingatheke kuti atulutse ndalamayi.

“Nyengoyi ambiri tayilowa tilibe mtendere wa mumtima,” adatero Banda.

Njerina Mapuno wa m’mudzi mwa Yoyola kwa T/A Masasa m’boma la Ntcheu wati amayenera adye kankhwiru n’kutsitsira ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi.

Koma iye wati chaka chino sizitheka.

“Kodi chisangalalo chingakhalepo pomwe nkhawa zili poti fetereza palibe?

“Pano koponi [ya fetereza wotsika mtengo] ili m’manja; sitidagule fetereza.

“Kachimanga kafika pothira fetereza koma kogulako fetereza wasiya kubwera. Iyi si khirisimasi yabwino,” adatero Mapuno.

T/A Nthache ya m’boma la Mwanza yati khirisima iyi ikhala yovuta chifukwa zolira maganizo zachuluka.

Iye wati anthu ali manja m’khosi kaamba kosowa mvula ndi ndalama.

“Zinthu zakwera mtengo kotero n’kovuta kupeza ndalama yogulira chakudya chapadera cha pa khirisimasi.

“Manja ali m’khosi pomwe tikumva kuti m’madera ena abzala kale. Apa palibe khirisimasi; nanga khirisimasi imakhala ya dzuwa?” adadandaula Nthache.

Koma Mfumu Yaikulu Chikulamayembe ya m’boma la Rumphi yati pali chiyembekezo kuti chisangalalo cha chaka chino chisiyana ndi zaka zina.

Mfumuyi yati chaka chino banja lake liri ndi ziweto zothandizira kukometsa chisangalalochi.

Iye wati chaka chatha sadasangalale bwino chifukwa adasowa chiweto chomwe akadapha koma chaka chino m’makola muli ng’ombe, mbuzi ndi nkhuku zomwe angasankhepo pokometsera chisangalalochi.

Koma mfumuyi yati kusowa kwa ndalama ndi mafuta agalimoto ndiko kungasokoneze chisangalalochi, maka kwa anthu ake.

T/A Kachindamoto ya m’boma la Dedza yati chisangalalo cha chaka chino chili bwino ndipo padali chiyembekezo kuti Lachinayi pa 22 kukhale kusangalala ndi magulupu ake.

“Tsiku la khirisimasili ndikhala ndili ku Zomba ndiye Lachinayili ndikhala ndikusangalala ndi magulupu adera langa.

“Apa tidzakhala tikuvina magule achikhalidwe chathu komanso kuonetsa za miyambo ya mafumu.

“Uku n’kusangalala kuti tagwira ntchito yolemetsa chaka chikuthachi; uku n’kuchalirira momwe tigwirire ntchito chaka tikuchilowachi.

“Khilisimasi ya chaka chino ikhala yosiyana ndi ya chaka chatha chifukwa chaka chino takonzekera bwino ndipo zinthu zomwe tikufuna kudzachita zili kale m’malo,” akutero mfumuyu.

Iye adati kusowa kwa ndalama ndikusowa kwa mafuta sizingasokoneze chisangalalochi chifukwa izi zimakhudza anthu akutauni osati iwo chifukwa kumudziko amakwera ngolo ngati afuna kuyenda.

Mneneri wa boma, Patricia Kaliati, wati khirisimasiyi ikhala yopambana chifukwa akadzachoka kopemphera adzakhala akusangalala ndi anthu osiyanasiyana, kumwa thobwa.

Iye wati khilisimasi ya chaka chino ndi chaka chatha sikusiyana chifukwa khirisimasi iliyonse imabweretsa chimwemwe kubanja lake kaamba koti adabadwanso pa 21 Desembala.

“Khilisimasi imeneyi ingokhala yothokoza Mulungu potitumizira mwanayo [Yesu] kuti adzatifere kumachimo athu.

“Tikuyenera kukhululukirana mangawa monga mwanayo adakhululukira ifenso ku machimo athu.

“Pomwe tikusangalala tikuyenera kutenga ena angapo kuti tisangalale nawo,” adatero Kaliati.

Related Articles

Back to top button