Chichewa

Katsoka: Mutu wa alakatuli

Listen to this article

Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene m’dziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli m’dziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Katsoka: Ndidayamba mu 1994
Katsoka: Ndidayamba mu 1994

Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera.

Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera m’mudzi mwa Ching’amba m’boma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu.

 

Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti?

Ndidauyamba m’chaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho.

 

Kodi bungwe limeneli lidayamba liti?

Bungweli lidayamba m’chaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe.

Cholinga chake nchiya?

Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli m’Malawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera m’ndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba.

 

Iweyo udayamba liti ndakatulo?

Ndidayamba ulakatuli m’chaka cha 1994 ndili pasukulu ya sekondale ya Likuni Boys.

Uli ndi masomphenya anji pa ndakatulo mmalawi muno?

Masomphenya anga ndi akuti ndakatulo zidzafike pabizinesi ngati momwe maluso ena alili pano. Kuti izi zidzatheke mpofunika kupeza akatswiri oti adzatithandize moti boma ndi mabungwe atalowererapo zikhoza kutithandiza kwambiri. Njira ina ndi yakuti alakatuli onse azilembetsa

ntchito zawo kubungwe la Cosoma kuti tizitha kukhala ndi chithunzithunzi chenicheni cha chiwerengero cha alakatuli omwe tili nawo.

Related Articles

Back to top button