Chichewa

Katundu wakwera udyo, atero anthu

 

Amalawi akonzekere kulira chifukwa cha kukwera udyo kwa mitengo ya zakudya ndi katundu wina komwe kwachitika kuyambira mwezi wa June chaka chino, latero bungwe la Centre for Social Concern, lomwe limaona momwe moyo wa anthu ukuyendera pankhani za chuma.

Bungweli lati kafukufuku wawo waonetsa kuti m’maboma a Karonga, Mangochi, Mzuzu, Lilongwe, Zomba ndi Blantyre, zakudya zakwera mtengo zomwe zivulaze Amalawi. Nawo anthu m’midzi akuti ali pamoto ndi kukwera mtengo ka zakudya. shopping

Zakudyazi ndi monga nyemba, mpunga, usipa, bread, sugar, mafuta ophikira, chimanga, chinangwa ndi zina zomwe munthu amayenera agwiritse ntchito pa tsiku. Bungweli lati ichi ndi chisonyezo kuti miyezi tikulowayi zinthu zinyanya kuwawa chifukwa chakusokonekera kwa chuma.

Kafukufuku amene bungweli lachita m’miyezi ya June ndi July waonetsa kuti banja la anthu 6 tsopano likuyenera kukhala ndi K126 457 kuchoka pa K118 663 yongogwiritsira ntchito mwezi umodzi.

“M’miyezi yomweyi chaka chatha, zakudya zidatsika mtengo ndi pafupifupi K2 pa K100 iliyonse. Ichi ndi chisonyezo kuti tikuloweraku anthu avutika kuti akwanitse kudya,” mbali imodzi ya kafukufukuyo yatero.

Izi zikusiyana ndi zomwe nduna ya zachuma Goodall Gondwe idauza mtundu wa Amalawi mu February chaka chino pamene idati kuyambira miyezi ya July ndi September zinthu zidzayamba kuyenda bwino.

“Kusefukira kwa madzi ndiko kwatisokoneza kuti chuma chisayende bwino koma tikuyembekeza kuti pofika gawo lachitatu la chaka [July mpaka September] 2015 zinthu ziyamba kuyenda bwino,” adatero Gondwe pouza The Nation.

Bungweli lati m’mwezi wa July, mtengo wa nyemba udakwera ndi K15 pa K100 iliyonse.

“Kumbali ya chimanga ndiye chidakwera ndi K6 pa K100 iliyonse mu June ndipo chakweranso mu July. Thumba la makilogalamu K50 likugulitsidwa K6 389 m’mizinda ikuluikulu.

“Ku Blantyre ndi Mangochi, mtengowu wafika pa K8 000 ndi K7 500 motsatizana. Zinthu zina monga sugar ndi nyama zakwera ndi pafupifupi K4 pa K100 iliyonse mu June ndipo mitengoyi yakweranso mu July,” watero kafukufukuyu.

Izi zikutsatiranso zomwe komiti yomwe imaona momwe chakudya chilili ya Malawi la Vulnerability Assessment Committee (MVAC) idatulutsa kuti pafupifupi anthu 3 miliyoni m’dziko muno akhudzidwa ndi njala ndipo afunika thandizo kwa miyezi isanu ndi umodzi.

Mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wati nthawi yakwana kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika abwere poyera ndi kufotokozera Amalawi zomwe achite pofuna kupulumutsa anthu kung’anjo yowawitsayi.

“Vuto ndi mtsogoleri wathu chifukwa sakulankhulapo chilichonse.

“Taonani momwe ndalama yathu ikuchitira, mudamuonapo [pulezidentiyu] akuwauza Amalawi chomwe achite? Akuyenera kupereka chikhulupiriro kwa Amalawi momwe titulukire m’mavutowa. Akuchita ngati zinthu zikuyenda bwino pamene anthu akuvutika,” adatero Kapito.

Mneneri wa Mutharika Gerald Viola adati atiyimbira kuti afotokozepo mbali ya mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika, koma pofika nthawi yomwe timasindikiza nkhaniyi iye adali asadatipatse mbali yake.

T/A Kanduku wa m’boma la Mwanza akuti m’bomalo mudali chilala choopsa chomwe chachititsa kuti anthu asamadye katatu patsiku.

“Kumudzi kuno ndi ochepa amene ungawapeze akudya mmawa, masana ndi madzulo. Ambiri akungodya madzulo okha. Chimanga chakwera mtengo. Ndowa tikugula K 3 000 pamene thumba ndi K9 000,” adatero Kanduku.

Clara Nyandula wa m’boma la Balaka akuti kumeneko thumba la chimanga lafika pa K8 500 ndipo anthu ambiri akumagula chimanga cha m’bigili pamtengo wa K1 000.

Zikatere, kudya mwakasinthasintha n’komwe kungathandize kuti anthu ayambe kudalira zakudya zina monga chinangwa, nthochi ndi mpunga.

Related Articles

Back to top button