Chichewa

Khama Khwiliro: Katakwe pa nyimbo zauzimu

Listen to this article

Khama Khwiliro ndi mmodzi mwa oimba nyimbo zauzimu amene ambiri otsata nyimbozi amamudziwa. CHIMWEMWE SEFASI adakumana naye ndipo adacheza motere:

Ndikudziwe…

Dzina langa ndine Khama Khwiliro, ndidabadwa pa 15 April 1983. Kwathu ndi m’mudzi mwa Mtengula, kwa T/A Chikowi ku Zomba.

Kodi udakwatira?

Maso patsogolo: Khwiliro
Maso patsogolo: Khwiliro

Khama ali pabanja ndipo adakwatira Jackina Meleka ndipo adadalitsidwa ndi mwana mmodzi, dzina lake Tawina.

Kodi  zoimbaimba udayamba liti?

Ndidayamba kuimba m’ma 1990. Koma mu 2010 mpamene ndidatulutsa chimbale changa choyamba chomwe mutu wake  ndi Nthawi Yanga Yakwana.

Kodi uli ndi zimbale zingati?

Inetu ndili ndi zimbale ziwiri: Nthawi Yanga Yakwana komanso Ndaona Kuwala.

Uthenga wako wagona pati nanga umaimba zamba zanji?

Uthenga wagona pa za mawu a Mulungu okamba zoyenera kuchita monga Akhristu makamaka nthawi yotsiriza ino. Nyimbo zikulukidwa mu zamba monga manganje, kwaito ndi zamba zina za kwathu kuno.

Pambali poimba umagwiranso ntchito ina? Nanga umakonda chiyani ngati sukuimba?

Inetu ndimagwira ntchito ku Blantyre Synod Health and Development Commission komanso ndikakhala kuti ndili ndi mpata, ndimakonda kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Kumbali ya zakudya, ndimakonda nsima ya chisoso ndi chambo.

Kuimba umafuna utafika nako pati?

Ndimafuna kuimba kutafika ngati mmene anzathu akunja amachitira komanso anthu azitha kukwanitsa kusamala mabanja awo kudzera m’kuimba ndi kupeka nyimbo.

Kodi ndi mavuto ati omwe mumakumana nawo ngati oimba?

Oimba ambiri timasowa thandizo kuti nyimbo zathu zifikire ponseponse. Sitigona poganizira kuti nyimbo tikajambula kuti, adzatithandize ndani? Nanga tidzagulitsa motani? Timalingaliranso kuti tikonza bwanji ma show, pompo tikulingalira kuti anthu obwerawo tidzawasangalatsa bwanji?

Pali mawu owonjezera?

Ndikuthokoza Amalawi onse chifukwa cha sapoti yomwe amatipatsa. Lathu ndi lonjezo kuti tipitiriza kufalitsa uthenga munyimbo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »