Chichewa

Khama ndiye yankho poweta ng’ombe zamkaka

Listen to this article

Kuchionetsero cha zaulimi cha National Agriculture Fair ku Trade Fair Grounds mumzinda wa Blantyre, Peacewell Edward Mlanga, wochokera kwa Senior Chief Somba m’boma la Blantyre adachita mphumi ndi kupeza chikho atapambana alimi anzake onse omwe adabwera kuchionetserochi. Ulimi wake udapatsa chidwi ngakhale mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe adatsegulira chionetserochi. Kodi chinsinsi cha mlimiyu n’chotani? Esmie Komwa adacheza naye motere:

Chidakopa anthu paulimi wanu kuchionetserochi n’chiyani?

Choyambirira ng’ombe yomwe ndidapita nayo kuchionetseroku imaoneka ya thanzi komanso ndi yoti imatulutsa mkaka wochuluka ndipo anthu adadzionera okha.

Ng’ombe za Mlanga zakwana 16 tsopano

Ng’ombe zanu zimatulutsa mkaka wochuluka bwanji?

Imodzi imatulutsa mkaka wosachepera malita 35 pa tsiku.

 

Chinsinsi chanu kuti muzipeza mkaka wochuluka chagona pati?

Zakudya zokwanira komanso za kasakaniza ndi madzi wokwanira tsiku lililonse.

 

Mumadyetsera zakudya zanji?

Kuonjezera pa udzu omwe ndimadyetsera nthawi zonse, m’zaka za mmbuyomu ndimadyetsera chakudya chogula cha ng’ombe chotchedwa dairy marsh koma nditaona kuti chakwera  mtengo kwambiri, ndidasiya mmalo mwake ndidayamba kugula zotsalira popanga mowa ku kampani ya Carlsberg, zotchedwa spent green. Ndichotsikirapo mtengo kusiyana ndi chakudya cha kusitolo chifukwa pamwezi ndimagula cha K135 000 pomwe chogulacho kuti chikwane pamafunika ndalama yosachepera K200 000. Kuonjezera apa, ndimadyetseranso madeya a nandolo ndi a chimanga.

 

Mutasiya kugwiritsa ntchito dairy marsh, mkaka sunatsike?

Ayi ndithu udakali chimodzimodzi.

 

Mumazipatsa chakudya chochuluka bwanji pa tsiku?

Alangizi adatiuza kuti ng’ombe iliyonse tiziyipatsa chakudya chokwana makilogalamu 200 koma mukudziwanso kuti sizocheza kuti munthu ufike pamenepa kotero nthawi zambiri ndimabwerera pa makilogalamu 170 pa ng’ombe iliyonse.

 

Nanga madzi amakhala wochuluka bwanji?

Madzi ndiye sindinganene, ndimaonetsetsa kuti azikhalamo nthawi zonse. Adandilumikizira mapaipi a madzi ku makola kotero momwera muli mipopi yomwe ndimangotsegula ndikaona kuti atsika.

Munayamba liti kuweta ng’ombe za mkaka?

Ndidayamba mu 2000 ndi ng’ombe imodzi kenako m’chaka chotsatiracho ndidagulanso ina basi kuchokera pamenepo zinadzichulukitsa zokha chifukwa nthawi zina zimaswa mapasa.

 

M’maweta ng’ombe za mtundu wanji?

Zija zimadziwika ndi dzina loti Friesian.

 

Pano zilipo zingati?

Zilipo 16 koma zomwe tikukama 7. Bwenzi zitapotsera pamenepa chifukwa zina zimatha kuswa mapasa koma ndimapatitsakonso ena.

 

Muli ndi za mphongonso?

Ayi, kuti zitenge bere timaitana alangizi kuti adzadzipatsire umuna wa mtundu wa ng’ombezi kuti tisasakanize mtundu.

 

Chidakupangitsani kuti muyambe ulimiwu n’chiyani?

Mayi anga adadwala ndipo kuchipatala adawauza kuti azimwa mkaka tsiku lililonse kotero ndidailowa ntchito yogula mkaka wa m’mapaketi. Kenako ndidaganiza zongogula ng’ombe ya mkaka kuti ndizingokama n’kumawapatsa ndipo tsiku lomwelo ndidayamba kukama. Ng’ombeyi imatulutsa mkaka wodzadza ndowa pa tsiku ndipo umandichulukira choncho wina ndinkangogawa kwa anthu ena a m’mudzimu. Posakhalitsa mnzanga wina adanditsina khutu kuti anthu akupanga ndalama pogulitsa ku kampani ya Lilongwe Dairy yomwe imabwera ku Blantyre konkuno n’kumagula kotero ndidayamba kuperekera kumeneko ndipo chaka chachiwiri ndidaonjezera ina. Phindu lomwe ndimapeza lidandipangitsa kuti ndilimbikire kwambiri mpomweno ndidakhazikika.

 

Ndi phindu lanji lomwe mwakhala mukupeza kuchokera ku mkaka?

Ndidagula malo ndikumangapo nyumba ziwiri zopangitsa lendi, ndagula malo ena wokwana nyumba zitatu zomwe malata ake ndagula kale komanso ndikuphunzitsa ana anga awiri ku poly. Ndidagawirakonso abale anga ena ng’ombezi omwenso akuthandizikira mu njira zosiyanasiyana mmakomo mwawo, kunena pakhomo panga ndiye sitisowa kanthu.

 

Mumakagulitsa kuti mkaka wanu?

Kuyambira Lamulungu mpaka Lachisanu ndimakagulitsa kwa amwenye m’tauni pa mtengo wa K180 pa lita wotsalawo ndimakagulitsa ku bulking group pamtengo wa K160 pa lita ndipo Loweruka, ndimakagulitsa kwa mzungu wina wake ku Nyambadwe pa mtengo wa K400 pa lita.

 

Mawu kwa alimi anzanu ndi wotani?

Ulimi wa ng’ombe za mkaka ndi waphindu koma kuti upindule umafuna kulimbikira. n

Related Articles

Back to top button