Nkhani

Kolondoloza: Mwambo wokaona mwana wa Inkosi

Listen to this article

Kumayambiriro kwa chaka chino Angoni ochokera m’boma la Mzimba adali chimwemwe tsaya kaamba ka kubadwa kwa mwana wamwamuna kubanja lachifumu la Inkosi ya Makhosi M’mbelwa ku Edingeni m’boma la Mzimba. Mwa mwambo wa Angoni, mwanayu ndiye akuyembekezereka kudzalowa ufumuwu mtsogolo muno. MARTHA CHIRAMBO adacheza ndi Ndabazake Thole, mlembi wamkulu wa bungwe la Mzimba Heritage, yemwe akulongosola za momwe mwambowu udayendera motere:umthepo

Ndakupezani wawa, ndamvetsedwa kuti mudapita kokaona mphatso ku Edingeni. Talongosolani, kodi mwambowu umayenda bwanji?

Poyamba ndinene kuti koyambirira kwa chaka chino ife Angoni tidasangalala kwambiri ndi kubadwa kwa mwana wa mwamuna kwa Inkosi ya Makhosi M’mbelwa. Paja ufumu wa Agonifetu timaupitiriza ndi kubadwa kwa mwana wamwamuna kubanja lachifumu. Zikatero timakhala ndi chikhulupiriro chonse kuti ufumu upitirira ndipo timapemphera mwamphamvu kuti Mulungu amuteteze mwanayu.

Zikomo wawa, pitirizani kulongosola za mwambowu tsopano.

Mwanayu atabadwa, uthenga udatumizidwa kwa makhosi onse kapena nditi mafumu onse Achingoni ku Ekwendeni, Elangeni ndinso ku Emucisweni komanso midzi ina yonse. Uthengawu udatipezanso ife.

Mutalandira uthenga mudachitapo chani?

Ife tidayamba kutsata ndondomeko yake yoti tikaone mwanayu. Sikuti umangodzuka lero ndi lero basi ndikukaona mwana, ayi, sititero. Ulendo wathu udali ndi zolinga zitatu monga kukamuona mwanayu, kukadziwa dzina lake, komanso kukapereka mphatso. Tidapempha kudzera kwa Inkosi Mpherembe yomwe ndi mlembi wamkulu wa khonsolo ya mafumu mwa a M’mbelwa. Kupatula apo, tidapemphanso kwa nduna ya komwe kulikulu ku Edingeni yomwe idatiloleza. Tidabwereranso kwa Mpherembe kukapemphanso chilolezo.

Nthawi yokaona mwana itakwana zidatani?

Adatipatsa Inkosikazi Mtwalo kuti ndiyo itsogorere ulendowu. Pajatu ntchito yokaona mwana imaimira kwambiri azimayinu. Mwa ichi pagulu lathu abambo tidalipo ochepa kulekana ndi amayi.

Mwakambapo zokapereka mphatso. Mudanyamula mphatso zanji?

Azimayi adatenga ufa, shuga ndi zina ndi zina zokhudza mwana, pomwe ife madoda tidanyamula kandiwo kake. Tidatenga mbuzi ngati ndiwo. Nanga ufa umayenda wopanda ndiwo zake?

Tsopano mutafika ku Edingeni, mudayambira pati?

Ife ngati madoda tidapereka malonje. Koma sitidakambeko kalikonse zokhudza kuona mwana. Pajatu tati ntchitoyi eniake enieni ndi amayi. Inkosikazi ndiyo idafotokoza cholinga cha ulendowo womwe tidapita a Mzimba Heritage ochokera ku Mzuzu, Mzimba boma komanso ku Lilongwe. Apa tidapereka mphatso.

Mudapereka mwana musadamuone? Talongosolani bwino pamenepa.

Iyo idali ya malonje chabe chifukwa ife Angoni tisadamuone mwana uja pamakhala ‘mboni’. Iyi ndi ndalama yomwe timaika m’mbale yosonyeza kuti mtima wathudi tikufunitsitsa timuone mwanayu. Ndipo posakhalitsa amayi ndi agogo ake aakazi a mwana adatutuluka naye. Komatu tonse sitidamugwire kupatula inkosikazi chifukwa uyu ndi mwana wachifumu.

Zonsezi zimachitika musadadziwebe dzina?

Eya. Udali mwambo wopatsa chidwitu ndi wosangalatsa kwambiri. Tidaperekanso ‘mboni’ ina kuti tidziwe dzina ndipo makolo ake adatiuza kuti ndi Londisizwe lomwe likutanthauza ‘mtetezi wa dziko’ kapena kuti ‘mvikiliri wa charo m’Chitumbuka’. Atangotchula dzina azimayi adalulutira komanso kuvina, ndipo ife a bungwe tidayamba tsopano kutumiza mauthenga palamya komanso paintaneti kwa abale ndi abwenzi za dzina. Dzina la mwana wa

Inkosi ya Makhosi sumangouzidwa basi; pamakhala ‘mboni’ ngati momwe zidachitikiramo.

Kodi akadabadwa mwana wamkazi chisangalalo chikadakhala chimodzimodzi?

Pachikhalidwe chathu, akakhala mwana wamkazi zimapereka maganizo ndithu kwa anthu poganizira kuti ufumuwu salowa ndi munthu wamkazi. Koma akakhala mtsikana timadziwa kuti tsiku lina adzakwatiwa ndipo adzachoka pamudzi.

Related Articles

Back to top button