Kubwera kwa 1 000 Kwacha kukusonyeza sizikuyenda

Kubwera kwa ndalama ya K1 000 yogwirana ndi chisonyezo kuti zinthu sizili bwino pa chuma m’dziko muno, atero akadaulo a zachuma, andale ndi ena.

Akuluakuluwo adanena izi kutsatira kulengeza kwa gavanala wa nkhokwe ya mabanki m’dziko muno (Reserve Bank of Malawi), Perks Ligoya Lachisanu lapitalo kuti pofika Julaye chaka chino, dziko lino likhala ndi ndalama yatsopano ya pepala ya K1 000.

Mkulu wa bungwe lounikira za chuma la Malawi Economic Justice Network (MEJN) Dalitso Kubalasa, yemwe adali nduna yazachuma m’boma la UDF yemwenso ndi phungu wa ku Nyumba ya Malamulo, Cassim Chilumpha, mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA), John Kapito, kudzanso anthu ena ati ganizo lobweretsa K1 000 yapepala ndichisonyezo kuti ng’ombe zayang’ana kudazibomu.

Malinga ndi Kubalasa, kupangidwa kwa K1000 kukutanthauza kuti ndalama ya dziko lino yachepa mphamvu.

“Zili choncho chifukwa ndalama zomwe timagulira katundu wochuluka zaka zapitazi sungagwiritsire ntchito lero ngati ukufuna kugula katundu yemweyo,” adatero Kubalasa.

Izi zikusemphana ndi kulankhula kwa Ligoya yemwe adati kubweretsa kwa ndalama yatsopanoyo, ndi kuchepetsa kukula kwa ndalama zina zapepala sizikutanthauza kuti zinthu sizili m’chimake koma kuunikira zoti ndalama yapepala ya K500 ikugwiritsidwa ntchito kwambiri.

Ligoya adati padakali pano pa ndalama 100 zomwe zimasindikizidwa, 85 zimakhala ma K500, choncho n’kofunika kubweretsa ndalama yokulirapo.

Chilumpha, yemwenso adali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino mu 2004 mpaka 2009, wati kubwera kwa K1 000 ndiumboni kuti boma likuvomereza kuti zinthu m’dziko muno sizili bwino.

Iye wati maiko amene mitengo ya katundu ili yotsika ndalama zawo zimakhala zochepa monga, dziko la South Africa, Britain ndi United States. Malinga ndi Chilumpha, ndalama yaikulu kwambiri ku South Africa ndi 200 rand, ku Britain ndalama yaikulu kwambiri ndi £60 pomwe ku America ndalama yaikulu kwambiri ndi $100.

“Ngati tikufika pokhala ndi K1 000 ndiye kuti tikulowera ku zomwe adaziona ku Zimbabwe kapena Zambia komwe ndalama yaikulu imagula zochepa,” adatero Chilumpha.

Iye adati K500 ikumakwanira kungogula buledi ndi sugar zomwe zikusonyeza kuti kubwera ndi K1 000 ndikuthina kwa zinthu.

Koma Chilumpha wati kuchepetsa ndalama zina kulibe vuto koma nthawi yokonzera ndalamayi ndiyo ili yoipa kaamba ka vuto la zachuma lomwe layanga m’dziko muno.

“Uku kuli ngati kutenga madzi m’kapu ndikukathira mumtsinje. Ndibwino tidikire nthawi ina,” adatero phunguyu.

Ndipo Kapito wati dziko likafika pobweretsa ndalama ina zimasonyeza kuti yachepa mphamvu.

Iye wati izi zili chonchi chifukwa katundu amene amagulidwa ndi ndalama yochepa akugulidwa ndi ndalama yaikulu.

Kapito adati K500 tsopano yayaluka, chifukwa ikugula katundu ochepa.

“Katundu amene timagulira K500 lero uyenera kutulutsa K2 000 pakatundu yemweyo. Kwacha yagwa mphamvu. K1 000 sikuti ikulowa m’malo mwa K500 koma mwina ili ngati K300,” Kapito adatero.

Iye adati mwachitsanzo, mu 2001 pomwe ndalama ya K500 imabwera, ulendo wina wabasi umakwanira ndalama imeneyo, koma adati padakali pano ulendo omwewo, K1 000 siingakwanire.

Kapito wati kuchepetsa ndalama zina chingakhale chosangalatsa chifukwa dziko lino ndilokhalo lomwe lidali ndi ndalama zikuluzikulu.

Ndipo Nelson Chasauka wa m’mudzi mwa Mphusa kwa T/A Ndamera m’boma la Nsanje wati ndalamayi yakulitsa kotero singathandize.

Mkuluyu wati zikadakhala bwino ndalamayo ili ndi mphamvu chifukwa bwenzi zogula zikuchuluka.

Samuel Chimowa wa kwa Kameza kwa T/A Machinjiri mumzinda wa Blantyre wati monga wa buzinesi sakuona kuti K1 000 ibweretsa phindu pantchito yake.

“Timavutika kuti tipeze ndalama yosintha, tizivutika kwambiri. Zikusonyeza kuti mphamvu ya ndalama [yathu] siili bwino,” adatero mkulu wogulitsa zitsulo zagalimotoyu.

Share This Post