Kucheza: Afisi ogulitsa ku Dedza

January 3, 2015 • Kucheza • Written by :

Pamene chuma chasokonekera m’dziko muno, mkulu wina ku Dedza wapeza njira zopezera ndalama pogulitsa afisi. Iye akuti afisiwa amathandiza posaka, chitetezo pakhomo komanso kukwera pamene uli paulendo. Mkuluyu akuti pakhomo pake tsopano sipasowa kanthu. Ndidali kunyumba kwa mkuluyu komwe ndidapita kukagula fisi wamkazi. Umu ndimo zidalili ku ulendowo:Hynas

Muli bwanji wawa?

Ine ndili bwino, koma anthu akutha. Iii, maliro awirikiza m’mudzi muno.

Kodi muno ndi m’mudzi mwa ndani?

Muno ndi m’mudzi mwa Masakaniza, T/A Kaphuka m’boma la Dedza. Ine ndi Njale Biweyo. Komatu sindidakudziweni, ndinu ndani komanso mwabwerera chiyani?

Ndine mtolankhani, koma ndabwera kudzagula afisi, ndamva kuti muli nawo ndipo mumagulitsa…

Aaah! Wakuuzani ndani? Ndiye mufuna mugule?

Ndangomva mwa anthu, eya ndikufuna kugula.

Chabwino, koma mwakonzeka? Chifukwatu simungangobwera.

Kukonzeka? Ndimayenera ndikonzeke motani?

Aaa! muganiza mungotenga? Muyenera mukhaletu ndi ndalama ngati mwatsimikiza kuti mukufunadi kupeza fisiyo.

Ine ndakonzeka, nanga inu mwakonzeka kundigulitsa?

Zonse zili ndi inu. Koma ndimayesa mwati mumalemba nkhani? Ndiye mufunanso mukalembe? Kapena mufuna akangokutetezani pamene mugwira ntchito yanu?

Ndikufuna wonditeteza komanso ndilembe nkhani. Ndi zotheka ndilembe nkhani?

Apezeka ndikugulitsani. Nkhani mutha kulemba koma mantha anga ndi oti mukalemba nkhani ndiye kuti boma lifuna kuti ndizikhomera msonkho chifukwa ndikupeza ndalama. Komabe lembani kuti anthu ena athenso kudzagula.

Mumapanga ndalama zingati?

Fisi wamphongo ndimagulitsa K8 000 pamene wamkazi amadula chifukwa amakakuswera ndiye ameneyu gulani pa K9 000.

Kodi ungawawone afisiwa?

Ayi, amenewa ndi ako basi. Kaya utakwera palibe amene angawawone.

Kusonyeza kuti nanenso ndikuyenera kukhwima?

Iyayi, izitu si zokhwimanso. Momwe mwabwereramu basi. Mukapereka ndalama ndikupatsani fisi wanu.

Ndimunyamula bwanji?

Timamunyamula m’chikwama. Palibe katundu amene mukuyenera kutenga, tengani ndalama basi.

Ndikamusunga potani?

Paliponse koma pasamafike munthu amene angatenge chikwamacho.

Ntchito azigwira nthawi yanji? Komanso tafotokozani bwino ntchito yake.

Ntchito amagwira usiku. Iyitu ndi ntchito yosaka komanso kuteteza ngati kwabwera munthu kunyumba kwanu kuti akufuna kukuberani. Munthu atabwera kufuna kukuberani basi ameneyo amuluma ndithu. Mukafuna ulendo, kwerani, ndi njinga yanu imeneyo. Kaya mufuna akusakireni ndiwo, akatero ndithu.

Kodi angakafike ku Blantyre kuchokera ku Lilongwe? Nanga angatenge nthawi yotani?

Aaa! Pali chaninso apa? Apapa pakutha maola awiri wafika kale. Inu mungogwira timakututo basi ndiye amalira amvekere hi-hi-hi! [waseka].

Kodi amasaka chiyani?

Ndiwo basi, iyi ndi ndiwo iliyonse yamagazi ungafune.

Moti inu wakusakirani chiyani masiku amenewa?

Sabata yatha adandipezera kandiwo. Ndi kamene mukaona kali pamenepaka.

Mumamudyetsa chiyani?

Basi amatolatola yekha, kaya apeza kanyama m’thengo agwira.

Sakugwira mbuzi za eni amenewa?

Aaa! Mwatani kodi. M’tchire basi….

Muli ndi afisi angati? Nanga mumawasunga bwanji?

Alipo awiri, wamkazi ndi wammuna. Ndidalinawo 5 koma achibale adadzatenganso. Amenewa ali m’chikwama ndipo ali m’nyumba yangayo.

Kodi wina sangasowetse chikwamacho?

Ayi, iiii ndiye kuputa zokhomatu. Komanso ndimakonza bwino pamalopo kuti wina asafikepo.

Kukonza bwanji?

Aaa inu! Mwatani kodi? Kukonza ndikukonza basi, mufuna ndichite kufotokoza zomwe ndimachitazo?

Mudayamba liti kuweta afisiwa? Nanga adakuphunzitsani ndani?

Ndidayamba mu 1965. Kungoti ndakhala madera ambiri komwe ndimakamva za chitetezochi. Ndidapita ku Ntchisi komwe ndinkagwira ntchito kukagula. Ndakhalanso zaka 11 mumzinda wa Lilongwe ndiye maderawa adandipangitsa kuti ndikhale ndi zokuteteza chifukwa ntchito yanga ndi ya ulonda. Inu mukafuna kugula fisi ndiye kuti ndikupangirani wanu osati awiri ndilinawowa.

Kusonyeza kuti mukamalondera amagwira ntchito ndi afisiwo?

Eyatu, ha-ha-ha! Amenewo ndiye alondawo. Ine ndimangogona basi agalu angawo n’kumagwira ntchito.

Komadi amakhwimitsa chitetezo?

Kwambiri, inetu komwe ndikugwira ntchito ndakhalako zaka 9. Pamene ankandilemba ine ntchito n’kuti pamalopo pakubedwa kwambiri koma chilowereni ine palibe adabapo. Komanso pali mpingo wina womwe anthu amakonda kubapo, fisi mmodzi akuteteza pameneponso.

Kodi sangandifere?

Ayi, aaa ndiye patavutatu. Ngati adayenda kolakwika ndiye amuthira machaka ndiye imfa yake ingakhale yomweyo.

Nanga wamkaziyo amaswa wopanda mphongo?

Ayi amafunika mphongo ndithu. Inuyo mukagula ndikuuzani anzanu amene ali ku Blantyre komweko amene adadzagula fisi kuno. Mukakweretsa ndipo akaswa.

Kodi anthu ambiri agulapo?

Eee ndi ambiri, ena ali ndi makola awo a ziweto ndipo adzatenga kuno afisi amene akusamalira ziweto kumeneko.

Nanga nditafa amapita kuti?

Pamenepo ndiye zimavuta chifukwa amavuta kwambiri ngati sudasiyire munthu wina. Uyenera kupeza munthu womukhulupirira kaya mkazi ngakhale mwana wako kuti ukadzafa adzasamale fisiyo. Komatu mafunsowa achuluka, mugula koma?

Ndikabwerenso koma chifukwa sindidatenge ndalama…

Ndiye basi zinazo mudzafunsa mukabwera kudzagula.

Koma akuthandizani bwanji?

Andithandiza, komabe mudzafunsa mukabwera, yendani bwino. Komabe musanapite ndiguleni lichero ndi madengu, musangopita, ayi, mutenge kanthu pano.

  • zandiopsa izi

    mpaka kuweta afisi zirombo Yehova timenyereni nkhondo

« »