Kucheza: Chidya abusa–Nthumbwana zodya olisha ziweto okha

November 8, 2014 • Kucheza • Written by :

Nthumbwana za ng’ombe kapena mbuzi zimaperekedwa kwa akuluakulu monga mafumu kapena alendo pakakhala zochitika. Ambirinso amakonda kudya nthumbwana ngati ndiwo pomwe ena amangokhwasula. Komatu pali chiwalo china panthumbwana chimene ena amakhulupirira kuti nchoyenera kudya abusa kapena kuti osamalira ziweto. Nidacheza ndi Vincent Kalimba yemwe akulongosola motere:

Kodi zolemba munthu ntchito yoweta ziweto kwanu zimachitika?

Kwabasi ndipo anthu ambiri omwe ali ndi ziweto ali ndi antchito osamala ziwetozo. Pena zimatheka wantchito mmodzi kumasamala ziweto za anthu angapo bola ngati akukwanitsa kulongosola pokazilowetsa m’khola madzulo zikakhuta.

Kodi akati chidya abusa amanena chiyani?

Amanena nthumbwana ina yake yomwe kawirikawiri imapezeka m’mimba mwa ng’ombe kapena mbuzi.

Imawoneka motani?

Imakhala ngati chija ena amati chibulangete kapena thaulo koma zimasiyana kuti chidya abusa chimakhala chofewa kwambiri.

Zidatani kuti chikhale chidya abusa?

Ndi dzina lomwe makolo kalelo adapereka potengera kuti eni ziweto akapha, mbusa amamupatsa nthumbwana imeneyo kuti akadye. Mchitidwewu udazolowereka moti olo mwini ziweto aphe zingapo, mbusa amatenga nthumbwana zimenezozo.

Malipiro ake amakhala chidya abusacho basi?

Ayi, amatha kumpatsanso nyama ina monga momwe mwini wakeyo wawonera koma samalephera kumpatsa chidya abusacho.

Nanga poti ena amati nthumbwana zimayenera kuperekedwa kwa mafumu kapena alendo ngati ulemu?

Nzoona koma chidya abusacho amatenga ndi wosamala ziweto. Mafumu ndi alendo amawapatsa nthumbwana zinazo.

Padalibe tanthauzo lapadera lochitira izi?

Padalibe, kungoti kumakhala ngati kumulemekeza osamalayo komanso zimapangitsa wosamalayo kulimbikira pantchito yakeyo. Abusa ena amatha kunyanyala ngati chiweto chaphedwa koma osawona chidya abusa.

Kunyanyala kwake kumakhala kotani?

Pena umatha kudabwa kuti dzuwa lakwera koma khola likadali lotseka. Kufufuza umangomva kuti m’busa wako watsegulira makola ena nkudupha lakolo ndiye umangodziwa kuti akulonjerera chidya abusa cha chiweto chomwe udapha.

Ndiye kukambirana kwake kumakhala kota?

Kukambirana basi monga anthu. Mwina kungopepesana ndi mawu ngati mumamvana kapena kumpatsa mazira ngakhalenso ndalama kuti apitirize ntchitoyo.

Limakhala pangano polembana ntchitoyo?

Ayi ndithu koma kuti zidangokhala ngati mwambo wake kuti mbusayo azilandira nthumbwana imeneyo ndipo ambiri amangowotcha nkudya osatinso kudikira zokaphika kunyumba.

Bwanji mabwanawo samangomusiya wonyanyalayo nkulemba wina?

Ziweto nzovuta kwambiri makamaka ng’ombe ndi mbuzi. Ena amakhulupirira kuti khola limatengera mutu wa mbusa ndiye kusinthasintha abusa nthawi zina kumasokoneza mphumi. Komanso pali ng’ombe zina zomwe zimazolowera mbusa wawo moti akasintha zimakhoza kuchita ukali nchifukwa pena mumaona kuti mbusa watsegula khola koma ng’ombe zina sizikutuluka.

Nanga pano za chidya abusa zikadalipo?

Zilipo m’madera ena koma mwambiri zidazimirira nkutsukuluzika kwa chikhalidweku komanso kusakanikirana kwa Mitundu ndiye zina zidazilala.

« »