Kucheza: Kuchipinda kwaphweka ndi juwisi wa mbatata

August 16, 2014 • Kucheza • Written by :

Bayisoni: Ntchito yambiri kuchipinda ndi ya abambo

Bayisoni: Ntchito yambiri kuchipinda ndi ya abambo

Macheza a kuchipinda aphweka. Kungomwa juwisi wa mbatata ya mtundu wa zondeni akuti zikutheka. Amene amacheza ndi mayi akunyumba kamodzi patsiku akuti akuonjezera mphamvu moti atha kucheza nawo kanayi tsiku limodzi. Rhoda Bayisoni mayi wa m’mudzi mwa Mujiwa ndi bambo Mevisoni Mujiwa a m’mudzi mwa Mujiwa kwa T/A Njema m’boma la Mulanje ndi mboni. Kodi aona zotani atamwa juwisiyu? Akusimba mphamvu zomwe apata.

————————————————————————————

Q. Tidziwane wawa…

A. Ndine Mevisoni Mujiwa, ndikuchokanso m’mudzi mwa Mujiwa koma sindine mfumu. Ndine mlimi wa zakumunda komanso ndili ndi ziweto.

Q. Kodi nchiyani chimenechi?

A. Uyu ndi juwisi wa mbatata ya mtundu wa zondeni. Inayi ndi mbatata, zondeni tikukamba apa ndi ameneyu. Imeneyi ndiyo mbatata yomwe takonzera chakumwachi.

Q. Mutanthauza kuti juwisiyu wachokera ku mbatatayi?

A. Eya, anthutu akaona sakhulupirira kuti zikuchokera ku mbatatayi, koma khulupirirani. Mwapeza titapanga kale koma achikhala munabwera chakummawa tidakapanga mukuona.

Q. Mumatani kuti mutulutse juwisiyu?

A. Timasenda mbatatayi, timayiphika ngati tikufuna timwere tiyi. Timathira mchere ndi mandimu komanso shuga. Ikapsa timayipota ngati tikuphika nsima. Phala lija timaliyika musefa momwe timayisefa uko ndikukanikiza ndiye imatulutsa madzi. Apotu timakhala takhazika kabeseni momwe mumagwera madziwo. Madzi amenewa ndiye juwisi ali m’botoloyu.

A. Ntchito ya juwisiyu nchiyani?

Kumwa basi monga tichitira ndi juwisi wa kugolosale.

Q. Amathandiza chiyani m’thupi?

A. Ali ndi mavitamini amene amapereka zofunikira zambiri zathupi koma ntchito yaikulu amapereka mphamvu m’thupi.

Q. Mphamvu zotani?

A. Aaaa mphamvu basi, monga ndikati mphamvu simudziwa? Kufunsira dala eti.

Q. Masukani, mphamvu zakumunda kapena?

A. Kumundako zimathandizanso chifukwa muli vitamini A koma mphamvu ndikukambazi ndi za kuchipinda. Ukamwa ayi umasimba mwayi.

Q. Kodi kuchipinda kumafunika mphamvu?

A. Tikamatitu uyu ndi mwamuna timanena momwe amachezera ndi mayi kuchipinda. Ngati mwamuna alibe mphamvu ndiye simwamunatu ameneyo.

Q. Kodi mphamvu zimatha?

A. Ayi sizitha koma zimangochepera. Ukamwa juwisiyu ndiye kuti umatengera mphamvu moti akazi ako kumakutchula kuti ‘amunanga’ molimba mtima.

Q. Mumadziwa bwanji kuti mphamvu zachepa?

A. Macheza ndi mayi amakhala akanthawi kochepa, komanso mukacheza lero ndiye kuti pamatha masiku kuti muchezenso.

Q. Ndiye mukamwa chimasintha nchiyani?

A. Macheza amachitika pafupifupi chifukwa mphamvu zimakhala zachuluka m’thupi. Sizingatheke kuti patsiku mucheze kawiri kokha, ayi ndithu mphamvu zimakhala zachuluka.

Q. Inu mwathandizika bwanji?

Mayi akhala akundidandaula, ndikacheza nawo lero ndiye kuti patha mwina sabata ndikulephera kucheza nawonso.

Q. Chimakuchitikirani nchiyani?

A. Basitu kupita kuchipinda kungokhala kusowa kuti nditani. Mayiwo amadandaula tsiku lililonse ndiye pakatha sabata basi mphamvu zipezeke.

Q. Pano zikutani?

A. Angotalikira, bwenzi atakuuzani wokha. Patsiku ndi kawiri kapena katatu. Akusangalala ndithu. Monga mukundioneramu ndakulatu koma mphamvu zikupezeka ngati mwana.

(Kutembenukira kwa mayiwo)

Q. Tikudziweni mayi….

A. Ndine Rhoda Bayisoni. Ndinenso mboni ya juwisi wa mbatatayu. Amathandizadi maka ntchito yakuchipinda.

Q. Kodi amayinunso mumapeza mphamvuzi?

A. Amayife timapeza koma ndi pang’ono koma abambo ndiye amapeza mphamvu zambiri. Kuchipindatu ntchito yambiri imakhala ya abambo ndiye akakhala ndi mphamvu zonse zimachitika nchimwemwe.

Q. Kodi pabanja panunso mukumwa?

A. Eya tikumwa ndipo akuthandiza, zinthu zasintha pabanja panga kusiyana ndi kale.

Q. Kale zinkatani? Nanga pano

?

A. Poyamba amunanga ndimacheza nawo kamodzi pa mwezi, sizimandisangalatsa koma nanga ndikadatani. Titayamba kumwa juwisiyu zinthu zasintha. Patsiku tikucheza kanayi kapena katatu. Zabweretsa chimwemwe pabanja langa.

Q. Kodi adakuuzani izi ndani?

A. Alangizi omwewa ndiwo atiphunzitsa.

Q. Alangizi ayamba kukulawulani?

A. Sikulawula, nayensotu mlimi amafunika zotere.

Q. Kodi zimamveka bwanji ukamamwa?

A. Amakoma monga akhalira juwisi wakusitolo, ngati mudamwapo juwisi wakusitolo simungasiyanitse ndi uyuyu.

Q. Ndingalaweko kuti ndimve momwe zikuchitira?

A. Talawani, bwanji? Ali bwinotu…….tangogulani botolo lonseli mukamwe ndi mayi kunyumba ndipotu mukasimba inuyo. Botolo limeneli ingotipatsani K750, pamene lidzikatha botolo limeneli mukasimbatu inuyo.

  • Kenny

    A Bobby, tikudikira ndemanga yanu. Mutalawa chinachitika ndi chani? Kunyumba anakudabwani kapena?

« »